Mt. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Afarisi ndi Asaduki apempha chizindikiro chozizwitsa(Mt. 12.38-39; Mk. 8.11-13; Lk. 11.16; 12.54-56)

1 Pakutero ankangofuna kumutchera msampha.

2Koma Yesu adaŵauza kuti, “Pamene dzuŵa likuloŵa, mumati, ‘Maŵa kucha bwino, popeza kuti kumwamba kuli psuu.’

3Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino.

4 Atatero, Yesu adaŵasiya nachokapo.

Za zophunzitsa zonama za Afarisi ndi Asaduki(Mk. 8.14-21; Lk. 12.1)

5Pamene ophunzira aja adakafika kutsidya, anali ataiŵala kutenga buledi.

6 ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa.

19Mt. 18.18; Yoh. 20.23Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”

20Yesu atanena zimenezi, adalamula ophunzira aja kuti asauze munthu aliyense kuti Iye ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Yesu aneneratu za kufa ndi kuuka kwake(Mk. 8.31-33; Lk. 9.22)

21Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kudziŵitsa ophunzira ake kuti, “Ndiyenera kupita ku Yerusalemu, kumeneko akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzandizunza kwambiri. Ndidzaphedwa koma mkucha wake ndidzauka.”

22Apo Petro adamtengera pambali nayamba kumdzudzula. Adati, “Pepani Ambuye, zisatero ai. Mulungu asalole zimenezi.”

23Koma Yesu adacheuka namdzudzula. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Ufuna kundilakwitsa. Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.”

Za kusenza mtanda ndi kutsata Yesu(Mk. 8.34—9.1; Lk. 9.23-27; Yoh. 12.25)

24 Mt. 10.38; Lk. 14.27 Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.

25Mt. 10.39; Lk. 17.33; Yoh. 12.25Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.

26Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?

27Mt. 25.31; Mas. 62.12; Aro. 2.6Ndipotu Mwana wa Munthu adzabwera ndi angelo ake ali ndi ulemerero wa Atate ake. Pamenepo adzabwezera aliyense molingana ndi zochita zake.

28Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Mwana wa Munthu akubwera ndi ulemerero waufumu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help