1 Mbi. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Anthu ankhondo ndi atsogoleri ao

1Nawu mndandanda wa atsogoleri a mabanja a Aisraele olamulira ankhondo zikwi ndiponso ankhondo mazana, pamodzi ndi akulu ao amene ankatumikira mfumu. Ankasinthanasinthana mwezi ndi mwezi pa chaka chilichonse, gulu lililonse linali ndi anthu okwanira 24,000.

2Yosobeamu mwana wa Zabidiele ankayang'anira gulu loyamba pa mwezi woyamba. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

3Iyeyu anali mdzukulu wa Perezi, ndipo ndiye anali mkulu wa atsogoleri onse ankhondo mwezi woyamba.

4Dodai Mwahohi anali woyang'anira gulu la mwezi wachiŵiri. Mtsogoleri wa gulu limeneli anali Mikiloti. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

5Mtsogoleri wa ankhondo pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa Yehoyada mkulu wa ansembe. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

6Benaya ameneyu ndiye amene ankatsogolera anthu makumi atatu aja. Amizabadi mwana wake ndiye amene ankatsatana naye polamulira gulu lakelo.

7Asahele, mbale wake wa Yowabu, anali mtsogoleri pa mwezi wachinai, ndipo mwana wake Zebadiya adaloŵa m'malo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

8Mtsogoleri pa mwezi wachisanu anali Samuti mdzukulu wa Izara. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

9Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chimodzi anali Ira, mwana wa Ikesi Mtekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

10Mtsogoleri pa mwezi wa chisanu ndi chiŵiri anali Helezi Mpeloni, mmodzi mwa zidzukulu za Efuremu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

11Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chitatu anali Sibekai Muhusa, wa m'banja la Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

12Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chinai anali Abiyezere, mmodzi mwa Aanetoti, Mbenjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

13Mtsogoleri pa mwezi wachikhumi anali Maharai, wa ku Netofa, wa m'banja la Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

14Mtsogoleri pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, mmodzi wa fuko la Efuremu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

15Mtsogoleri pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, mdzukulu wa Otiniyele. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

Oyang'anira mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele

16Atsogoleri amene ankayang'anira mafuko a Aisraele anali aŵa: Mtsogoleri wa Arubeni anali Eliyezere, mwana wa Zikiri. Mtsogoleri wa Asimeoni anali Sefatiya, mwana wa Maaka.

17Mtsogoleri wa Alevi anali Hasabiya, mwana wa Kemuwele. Mtsogoleri wa Aaroni anali Zadoki.

18Mtsogoleri wa Ayuda anali Elihu, mmodzi mwa abale a Davide. Mtsogoleri wa Aisakara anali Omuri, mwana wa Mikaele.

19Mtsogoleri wa Azebuloni anali Isimaya, mwana wa Obadiya. Mtsogoleri wa Anafutali anali Yeremoti, mwana wa Aziriele.

20Mtsogoleri wa Aefuremu anali Hoseya, mwana wa Azaziya. Mtsogoleri wa fuko lahafu la Manase lakuzambwe anali Yowele, mwana wa Pedaya.

21Mtsogoleri wa fuko lahafu la Manase lakuvuma, dera la Giliyadi anali Ido, mwana wa Zekariya. Mtsogoleri wa Abenjamini anali Yasiyele, mwana wa Abinere.

22Mtsogoleri wa Adani anali Azarele, mwana wa Yerohamu. Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mafuko a Aisraele.

23 Gen. 15.5; 22.17; 26.4 Davide sadaŵerengere kumodzi anthu osafika zaka 20 zakubadwa, pakuti Chauta adaalonjeza kuti Aisraele adzachuluka ngati nyenyezi zakumwamba.

242Sam. 24.15; 1Mbi. 21.1-14 Yowabu mwana wa Zeruya adayambapo kuŵerenga, koma sadatsirize ai. Mkwiyo wa Chauta udaŵagwera Aisraele chifukwa cha zimenezi, ndipo chiŵerengerocho sadachiloŵetse m'buku la mbiri ya mfumu Davide.

Anthu oyang'anira chuma cha Davide

25Azimaveti mwana wa Adiyele ankayang'anira chuma cha mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayang'anira chuma cham'miraga, cham'mizinda, cham'midzi ndi cha m'nyumba zankhondo.

26Eziri mwana wa Kelubi ankayang'anira anthu ogwira ntchito zolima ku minda.

27Simei wa ku Rama ankayang'anira minda yamphesa. Zabidi wa ku Sifamu ankayang'anira vinyo kuti asungike bwino mosungira mwake.

28Baala-Hanani wa ku Gederi anali woyang'anira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ku Sefera. Yowasi ankayang'anira mosungira mafuta.

29Sitirai wa ku Saroni ankayang'anira ziŵeto za ku busa la ku Saroni. Safati, mwana wa Adilai, ankayang'anira ziŵeto zakuzigwa.

30Obili Mwismaele ankayang'anira ngamira. Yedeiya Mmeronoti ankayang'anira abulu. Yazizi Muhagiri ankayang'anira nkhosa ndi mbuzi.

31Onseŵa ndiwo amene anali akulu oyang'anira chuma cha mfumu Davide.

Aphungu a Davide

32Yonatani, mtsibweni wake wa Davide, anali phungu wake, popeza kuti anali munthu womvetsa zinthu, ndiponso wophunzira bwino. Iyeyo pamodzi ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni, ankaphunzitsa ana a mfumu.

33Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndipo Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu.

34Ahitofele atamwalira, m'malo mwake mudaloŵa Yehoyada, mwana wa Benaya, ndiponso Abiyatara. Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help