1Chaka chachitatu cha ufumu wa Hoseya, mwana wa Ela, mfumu ya ku Israele, Hezekiya, mwana wa Ahazi, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu.
2Anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Abi, mwana wa Zekariya.
3Hezekiya adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira Davide kholo lake.
4
5Hezekiyayo adakhulupirira Chauta, Mulungu wa Aisraele, kotero kuti panalibe wofanafana naye pakati pa mafumu onse a ku Yuda iyeyo atafa, ngakhale pakati pa amene analipo kale iye asanaloŵe ufumu.
6Iyeyo ankakangamira kwa Chauta. Sadaleke kutsata Chauta, koma ankasunga malamulo amene Iye adapatsa Mose.
7Nchifukwa chake Chauta anali naye. Kulikonse kumene ankapita, zinthu zinkamuyendera bwino. Hezekiyayo adapandukira mfumu ya ku Asiriya, mwakuti sankaitumikiranso ai.
8Adakantha Afilisti mpaka ku Gaza ndi ku dera lake lonse. Adaononga mudzi uliwonse ndi mzinda uliwonse.
9Chaka chachinai cha ufumu wa Hezekiya chimene chinali chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Hoseya, mwana wa Ela, mfumu ya ku Israele, Salimanezere mfumu ya ku Asiriya adabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya, ndipo adauzinga ndi zithando zankhondo.
10Tsono adaulanda patapita zaka zitatu. Chaka chachisanu ndi chimodzi cha ufumu wa Hezekiya chimene chinali cha chisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Israele, mzinda wa Samariya udalandidwa.
11Mfumu ya ku Asiriya idatenga Aisraele kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya. Adakaŵakhazika ku mzinda wa Hala, ndinso pafupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndi ku mizinda ya Amedi.
12Izi zidachitika chifukwa choti anthuwo sadamvere mau a Chauta Mulungu wao, koma adaphwanya chipangano chake, pamodzi ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Chauta adaŵalamula. Sadatsate zimenezo kapena kuzigwiritsa ntchito.
Senakeribu athira nkhondo ku Yuda(2 Mbi. 32.1-19; Yes. 36.1-22)13Chaka cha 14 cha ufumu wa Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya adadzathira nkhondo mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda nailanda.
14Ndipo Hezekiya mfumu ya ku Yuda adatumiza mau ku Lakisi kwa mfumu ya ku Asiriya, onena kuti, “Ndidalakwa ine. Lekeni. Chilichonse chimene munene ndidzachita.” Pamenepo mfumu ya ku Asiriya idamlamula Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, kuti azipereka makilogramu a siliva okwanira 3,000 ndi makilogramu a golide 1,000.
15Tsono Hezekiya adapereka kwa mfumuyo siliva yense wa ku Nyumba ya Chauta, pamodzi ndi wa ku nyumba zosungira chuma cha mfumu.
16Nthaŵi imeneyo mpamene Hezekiya adakanganula golide wa pa zitseko za Nyumba ya Chauta ndi wa pa mphuthu za makomo, amene iye yemweyo anali atamatapo. Tsono Hezekiyayo adapereka golideyo kwa mfumu ya ku Asiriya.
17Komabe mfumu ya ku Asiriya idatuma mtsogoleri wankhondo, nduna yaikulu ndi kazembe wankhondo, pamodzi ndi gulu lankhondo lalikulu kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwowo adapita nakafika ku Yerusalemu, ndipo adakaima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku malo a mmisiri wa nsalu.
18Pamenepo iwo adaitana mfumu, ndipo anthu atatu adatuluka mu mzinda nakakumana nawo. Anthu aŵa: mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu, dzina lake Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika.
19Kazembe wankhondo uja adaŵauza kuti akanene kwa Hezekiya mau aŵa: “Mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya, ikuti, ‘Chimene chikulimbitsa chikhulupiriro chako motere nchiyani?
20Kodi ukuganiza kuti mau okha nkulingana ndi luso ndi mphamvu pa nkhondo? Kodi tsono ukudalira yani kuti uzindigalukira?
21Makamaka ukuyembekeza kuti Ejipito adzakuthandiza ati. Koma kuteroko kuli ngati kukhulupirira bango lothyoka limene litha kumbaya munthu m'manja ataliyesa ndodo yoyendera. Ndimo m'mene mfumu ya ku Ejipito imamchitira aliyense woidalira.
22“ ‘Kapena undiwuza kuti mumakhulupirira Chauta Mulungu wanu. Kodi si Mulungu yemweyo amene akachisi ake ndi maguwa ake Hezekiya adaŵathetsa, nauza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa ili la ku Yerusalemu?”
23Tiye tsono utembezane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ndidzakupatsa akavalo okwanira zikwi ziŵiri, ngati iwe ungathe kupeza anthu ake okwerapo.
24Ungathe bwanji kupambana ngakhale mmodzi yekha mwa akazembe ang'onoang'ono a mbuye wanga, pamene ukukhulupirira Aejipito, kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo?
25Ndiponso kodi sukudziŵa kuti ndi Chauta amene wandibweretsa kuno, kuti ndidzathire nkhondo dziko lino ndi kuliwononga? Chautayo ndiye adachita kundiwuza kuti ndilimbane nalo ndi kuliwononga dziko lano.’ ”
26Pamenepo Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, ndiponso Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.”
27Koma kazembe uja adati, “Kodi mukuganiza kuti mfumu yanga idandituma kuti ndilankhule mau ameneŵa kwa inu nokha ndi kwa mfumu yanu basi? Iyai, ndikulankhulanso kwa anthu amene akhala pakhomawo, amene adzayenera kudya ndoŵe yao yomwe ndi kumwa mkodzo wao womwe, monga momwe mudzachitire inuyo.”
28Tsono kazembe uja adaimirira nafuula m'Chiyuda kuti, “Mverani mau a mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya.
29Mfumuyo ikuti, Musalole kuti Hezekiya akunyengeni, chifukwa sadzatha kukupulumutsani m'manja mwanga.
30Asakukakamizeni kuti mudalire Chauta pokuuzani kuti mosapeneka konse Chauta wanuyo adzakupulumutsani, ndipo kuti mfumu ya ku Asiriya sidzalanda mzinda wanuwu.
31Musamumvere Hezekiya. Mfumu ya ku Asiriya ikukulamulani kuti mutulukemo mumzindamo, ndipo muigonjere. Mukatero, aliyense mwa inu azidzadya mphesa ndi nkhuyu zake ndi kumamwa madzi a m'chitsime chake.
32Mudzachita choncho mpaka nthaŵi imene mfumuyo idzakutengeni kupita nanu ku dziko lolingana ndi lanuli, dziko la chonde la mwana alirenji, kuti kumeneko mudzakhale moyo, osafa. Ndiye inu chenjerani, Hezekiya asakupusitseni pokuuzani kuti Chauta adzakupulumutsani.
33Mwa milungu ya anthu a mitundu ina, kodi alipo ndi mmodzi yemwe amene adapulumutsapo dziko lake kwa mfumu ya ku Asiriya?
34Kodi milungu ya Hamati ndi Aripadi ili kuti? Nanga milungu ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva ili kuti? Kodi milunguyo idaupulumutsa mzinda wa Samariya kwa mbuye wanga?
35Kodi ndi iti mwa milungu yonse ya maikoŵa imene idapulumutsapo maiko ao kwa mfumu yathu, kuti inu muziti Chauta nkupulumutsa Yerusalemu kwa mfumu yathuyo?”
36Koma anthu adangokhala chete, osayankhapo kanthu chifukwa mfumu Hezekiya adaaŵalamula kuti, “Musamuyankhe ai.”
37Tsono Eliyakimu mwana wa Hilikiya, amene ankayang'anira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika, adang'amba zovala zao mwachisoni, ndipo adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza zimene kazembe wa ku Asiriya uja adaalankhula.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.