Yer. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yeremiya aneneratu za ukapolo wa Aisraele

1Chauta adandiwuza kuti,

2“Usadzakwatire, usadzabale ana aamuna kapena aakazi ku malo ano.

3Ndithu kunena za ana aamuna kapena ana aakazi obadwira kuno, kapenanso za amai ao ndi atate ao amene adabereka anawo m'dziko muno,

4onsewo adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzaŵalira maliro kapena kuŵaika m'manda. Adzakhala ngati ndoŵe yotayikira pansi. Ena adzafera pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakuthengo.”

5Chauta akunena kuti, “Usaloŵe m'nyumba ya maliro. Usaloŵemo kuti ukalire kapena kutonthoza anthu, pakuti ndaŵachotsera mtendere wanga. Ndachotsanso chikondi changa chosasinthika ndiponso chifundo changa.

6Akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, onsewo adzafa m'dziko lino. Koma maliro ao sadzaikidwa, iwowo sadzaŵalira. Palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi chifukwa cha malirowo.

7Palibe amene adzapatse chakudya munthu wolira kuti amtonthoze chifukwa cha akufawo. Sadzamupatsa chakumwa kuti amtonthoze, ngakhale amwalire atate ake kapena amai ake.

8“Usadzaloŵe m'nyumba m'mene muli phwando, kuti udye nao ndi kumwa nao,”

9Yer. 7.34; 25.10; Chiv. 18.23Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pa nthaŵi yanu yomwe, ndiponso pa malo omwe ano ndidzathetsa mau achisangalalo ndi achimwemwe, ndipo ndidzachotsa liwu la mkwati wamwamuna ndi la mkwati wamkazi inuyo mukuwona.

10“Tsono ukadzaŵauza anthuwo mau ameneŵa, makamaka adzakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta wanena kuti tsoka lotere lidzatigwera ifeyo? Kodi tidalakwanji? Kodi Inu Chauta, Mulungu wathu, takuchimwirani chiyani?’

11Tsono iwe udzayankhe kuti, ‘Nchifukwa chakuti makolo anu adandisiya Ine,’ akuterotu Chauta. ‘Adatsata milungu ina, namaitumikira ndi kumaipembedza. Adandisiya Ine, ndipo sadamvere malamulo anga.

12Komanso inu mudachimwa koposa kupambana makolo anu: aliyense mwa inu akutsata zoipa ndi mtima wake wokanika, m'malo momandimvera Ine.

13Motero Ine ndidzakupirikitsani m'dziko lino ndi kukuloŵetsani m'dziko limene inu ndi makolo anu simulidziŵa. Kumeneko mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, chifukwa Ine sindidzakuchitiraninso chifundo.’ ”

Chauta adzatulutsa Aisraele mu ukapolo

14Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Masiku akubwera pamene anthu polumbira sazidzatinso, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko la Ejipito!’

15Koma azidzati, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko lakumpoto, ndi ku maiko konse kumene adaŵabalalitsira!’ Ndithu ndidzaŵabwezera ku malo amene ndidapatsa makolo ao.”

Kudza kwa chilango

16Chauta akuti, “Ndidzaitana adani ambiri okhala ngati asodzi a nsomba, ndipo adzaŵagwira anthuŵa ngati nsomba. Pambuyo pake ndidzaitana adani enanso ambiri okhala ngati alenje, kuti akaŵasake anthuŵa ku mapiri, ku zitunda, ndiponso m'mapanga am'matanthwe.

17Maso anga amaona makhalidwe ao onse oipa, ndi osabisika pamaso panga. Palibenso tchimo lililonse limene sindikulidziŵa.

18Ndidzaŵalanga moŵirikiza, chifukwa cha kuipa kwao ndi machimo ao. Ndidzatero chifukwa chakuti aipitsa dziko langa ndi mafano ao amene ali ngati mitembo, ndipo dziko limene lili choloŵa changa adalidzaza ndi mafano ao onyansa.”

Yeremiya apemphera mokhulupirira

19Inu Chauta, ndinu mphamvu zanga ndi linga langa,

ndinu pothaŵira panga pa nthaŵi ya mavuto.

Anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu

kuchokera ku malire onse a dziko lapansi.

Adzati, “Makolo athu anali ndi milungu yonama,

anali ndi mafano achabechabe opanda phindu.

20Kodi munthu nkudzipangira milungu yeniyeni?

Atati apange, singakhale milungu konse.”

21Chauta akuti, “Nchifukwa chake ndidzaŵaphunzitsa, ndidzaŵaphunzitsa kokha kano kuti adziŵe mphamvu zanga zopambana. Ndithudi adzadziŵa kuti Ine dzina langa ndine Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help