1 Deut. 17.6; 19.15 Aka nkachitatu tsopano kuti ndibwere kwanuko. Mau a Mulungu akuti, “Mlandu uliwonse uzitsimikizika ndi umboni wa anthu aŵiri kapena atatu.”
2Inu amene mudaachimwa kale, ndiponso ena onse, paja ndidaakuuzani pamene ndinali kwanuko kachiŵiri kaja ndipo ndikubwereza kukuuziranitu tsopano ndisanafike, kuti ndikadzabweranso, sindidzamchitira chifundo wina aliyense.
3Pamenepo mudzaona chitsimikizo chimene mukufuna chakuti Khristu amalankhula kudzera mwa ine. Iyeyu sali wofooka pa zimene amachita nanu, koma amaonetsa mphamvu zake pakati panu.
4Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu.
5Muzidziyesa nokha inuyo kuti mutsimikize ngati mukusungadi chikhulupiriro chanu. Muzidzifunsitsa nokha. Simudziŵa nanga kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Ngati si choncho, mwalephereratu.
6Koma ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitidalephere.
7Tikupempha Mulungu kuti musachite choipa chilichonse. Osati kuti ife tiwoneke ngati opambana, koma kuti inu muchite zimene zili zoyenera, ngakhale ife tiwoneke ngati talephera.
8Pakuti sitingathe kuchita chilichonse chotsutsana ndi choona, koma zokhazokha zothandizira choonacho.
9Timakondwa pamene ife tili ofooka koma inu muli amphamvu. Chimene tikupempha Mulungu nchakuti mudzasanduke angwiro.
10Ndikulemba zimenezi ndisanafike kwanu, kuti ndikadzafika, pasadzakhale chifukwa choti ndidzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwaukali. Ambuye adandipatsa ulamulirowo kuti ndilimbitse mpingo, osati kuti ndiupasule.
11Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
12Mupatsane moni mwa chikondi choona.
13Anthu onse a Mulungu akukupatsani moni.
14Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.