1Chauta adauza Mose kuti,
2“Upange malipenga aŵiri asiliva, uchite kusula. Uziimba malipengawo poitana mpingo, ndi pochoka pa mahema.
3Akaliza aŵiri onsewo, mpingo wonse usonkhane kwa iwe pa chipata cha chihema chamsonkhano.
4Koma akangoliza limodzi lokha, atsogoleri a mafuko a Aisraele ndiwo asonkhane kwa iwe.
5Mukaliza lipenga lochenjeza, anthu a m'mahema akuvuma ayambepo ulendo.
6Mukaliza lipenga lochenjeza kachiŵiri, anthu a m'mahema akumwera ayambepo ulendo. Muziŵalizira lipenga lochenjezalo nthaŵi zonse akamanyamuka ulendo.
7Pamene mpingo wonse uyenera kusonkhana pamodzi, mulize lipenga, koma musalize lipenga lochenjeza.
8Ana a Aroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipenga. Ntchito ya malipengayi ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse.
9Pamene mukukamenya nkhondo m'dziko mwanu ndi adani amene akukuzunzani, nthaŵi imeneyo mulize malipenga ochenjeza, kuti Chauta wanu akukumbukeni, ndipo adzakupulumutsani kwa adani anu.
10Pa tsiku lanu losangalala, pa masiku osankhidwa a zikondwerero zanu, ndi pa masiku oyamba a miyezi, mulize malipenga pamene mukupereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zachiyanjano. Malipengawo adzakuthandizani kumkumbukira Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.”
Za m'mene aziyendera11Pa chaka chachiŵiri, mwezi wachiŵiri, tsiku la 20, mtambo udachoka pa chihema chaumboni.
12Tsono Aisraele adanyamuka ulendo wao m'magulumagulu kuchokera ku chipululu cha Sinai. Mtambowo udakaima m'chipululu cha Parani.
13Kameneka kanali koyamba kuti Aisraele anyamuke, Chauta atalamula kudzera mwa Mose.
14Otsata mbendera ya zithando za fuko la Yuda ndiwo adayamba kunyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Nasoni mwana wa Aminadabu.
15Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanele mwana wa Zuwara.
16Mtsogoleri wa gulu la fuko la Zebuloni anali Eliyabu mwana wa Heloni.
17Anthu atagwetsa chihema cha Mulungu, ana a Geresoni ndi ana a Merari, oyenera kunyamula chihema cha Mulungu, adanyamuka ulendo wao.
18Pambuyo pake otsata mbendera ya zithando za fuko la Rubeni adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Elizuri mwana wa Sedeuri.
19Mtsogoleri wa gulu la Asimeoni anali Selumiele mwana wa Zurishadai.
20Mtsogoleri wa gulu la fuko la Agadi anali Eliyasafu mwana wa Deuwele.
21Tsono Akohati atasenza zinthu zopatulika, adanyamuka. Malo opatulika anali atamangidwiratu iwowo asanafike.
22Otsata mbendera ya zithando za fuko la Efuremu adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Elisama mwana wa Amihudi.
23Mtsogoleri wa gulu la fuko la Manase anali Gamaliele mwana wa Pedazuri.
24Mtsogoleri wa fuko la Abenjamini anali Abidani mwana wa Gideoni.
25Potsiriza otsata mbendera ya zithando za Adani amene anali kumbuyo kwa anthu a mahema onse, adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Ahiyezere mwana wa Amishadai.
26Mtsogoleri wa gulu la fuko la Asere anali Pagiyele mwana wa Okarani.
27Mtsogoleri wa gulu la fuko la Nafutali anali Ahira mwana wa Enani.
28Umenewu ndiwo mndandanda wa kayendedwe ka Aisraele, pamene ankanyamuka ulendo wao m'magulumagulu.
29Mose adauza Hobaba, mwana wa Reuele Mmidiyani, mpongozi wake uja, kuti, “Tikupita ku malo amene Chauta adati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiyeni tipite limodzi, ndipo tidzakuchitirani zabwino, pakuti Chauta walonjeza Aisraele zinthu zabwino.”
30Koma iye adayankha kuti, “Sindipita nao, ndipita kwathu kwa abale anga.”
31Ndipo Mose adati, “Musatisiye, ndapota nanu, poti inu mukudziŵa kumene tingamange mahema m'chipululu muno, ndipo mudzakhala maso athu.
32Mukapita nao, zilizonse zimene Chauta adzatichitire, ife tidzakuchitirani zomwezo.”
Anthu anyamuka ulendo33Choncho adanyamuka ku phiri la Chauta, nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi lachipangano la Chauta lidatsogola, nayenda nalo ulendo wa masiku atatu, kuti akapeze malo oti anthu onse aja akapumuleko.
34Mtambo wa Chauta unkaŵaphimba masana, nthaŵi iliyonse pamene ankanyamuka pamahemapo.
35 Mas. 68.1 Nthaŵi iliyonse pamene Bokosi lachipangano linkanyamuka, Mose ankati, “Dzambatukani, Inu Chauta, muŵamwaze adani anu. Onse odana nanu athaŵe akakuwonani.”
36Mtambowo ukaima, Mose ankati, “Inu Chauta, bwererani kwa Aisraele anu amene ali zikwi zosaŵerengeka.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.