1Aisraele onse adanyamuka kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, kudzanso dziko la Giliyadi, ndipo adasonkhana pamaso pa Chauta ku Mizipa.
2Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse a Aisraele adabwera ku msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo 400,000 oyenda pansi omenya nkhondo ndi lupanga.
3M'menemo nkuti anthu a fuko la Benjamini atamva kuti Aisraele apita ku Mizipa. Tsono Aisraele adati, “Tiwuze, kodi zoipa zoterezi zachitika bwanji?”
4Apo Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwayo, adati, “Ndidafika ku Gibea, mzinda wa Abenjamini, ineyo ndi mzikazi wanga, kuti tigone kumeneko.
5Anthu a ku Gibea adandiwukira nazinga nyumba imene munali ine nthaŵi ya usiku. Ankafuna kundipha ndipo adamchita zoipa mzikazi wangayo mwakhakhamizo mpaka iye adafa.
6Ndidamtenga mzikaziyo ndi kumduladula nthulinthuli, nkuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraele. Ndithudi anthu amene aja achita zinthu zonyansa ndi zoipa kwabasi m'dziko lino la Israele.
7Nzimenezotu, inu Aisraele, ndikuuza nonsenu, mupereke malangizo anu ndipo mupangane pompano.”
8Anthu onse adadzuka pamodzi nati, “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa ife amene apite ku hema lake, palibe amene abwerere kunyumba kwake.
9Koma tsono zimene tiŵachite anthu a ku Gibea ndi izi: tipita kukalimbana nawo mzindawo potsata zimene maere atiwuze.
10M'mafuko onse a Aisraele tisankhula anthu khumi pa anthu 100 aliwonse. Ameneŵa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Gibea, mzinda wa ku Benjamini, chifukwa cha tchimo lao lonyansa zedi limene adachita m'dziko la Israele.”
11Motero Aisraele onse adasonkhana atagwirizana chimodzi pofuna kulimbana nawo mzindawo.
12Mafuko a Aisraele adatuma anthu kwa fuko lonse la Benjamini, kuti akafunse kuti, “Kodi zoipa zimene mwachita pakati panupazi nzotani?
13Ndiye ife tsopano tikuti mubwere nawo anthuwo, anthu achabechabe aja a ku Gibea, kuti tiŵaphe, kuti potero tichotse kulaulaku m'dziko la Israele.” Koma Abenjamini sadafune kumva mau a Aisraele, abale ao.
14Choncho Abenjamini onse adatuluka m'mizinda yao ku Gibea kukamenyana nkhondo ndi Aisraele.
15Tsiku limenelo Abenjamini adasonkhanitsa ankhondo 26,000, osaŵerenga anthu ena a ku Gibea 700 osankhidwa.
16Mwa anthu onseŵa panali anthu 700 amanzere, amene ankatha kulasa ndi mwala ngakhale tsitsi limodzi, osaphonya konse.
17Aisraele onse, kupatula Abenjamini, adasonkhanitsa anthu amalupanga 400,000, anthu ake odziŵa bwino nkhondo.
Aisraele amenyana nkhondo ndi Abenjamini.18Aisraele adanyamuka napita ku Betele kukafunsa kwa Mulungu kuti, “Ndani mwa ife amene ayambe kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini?” Chauta adayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo limene liyambe.”
19Tsono Aisraele adadzuka m'maŵa nakamanga zithando zao moyang'anana ndi Gibea.
20Aisraele adapita kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini, nakhazika ankhondo ao kuyang'ana mzinda wa Gibea.
21Nawonso Abenjamini adatuluka ku Gibea ndipo tsiku limenelo adapha Aisraele 22,000.
22Koma Aisraelewo adalimbitsana mtima ndipo adakhazika ankhondo ao kachiŵiri pa malo omwe aja pamene adaaŵakhazika tsiku loyamba lija.
23Tsono Aisraelewo adapita kukalira pamaso pa Chauta mpaka madzulo. Adakafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kachiŵiri kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu?” Chauta adayankha kuti, “Inde pitani mukamenyane nawo.”
24Choncho Aisraele adafika pafupi, kuti akalimbane ndi Abenjamini tsiku lachiŵiri lake.
25Abenjamini adatulukanso mu mzinda wa Gibea, kukalimbana nawo tsiku lachiŵirilo, ndipo adapha ankhondo a Aisraele 18,000.
26Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta.
27Bokosi lachipangano la Chauta linali kumeneko masiku amenewo.
28Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye ankayang'anira bokosilo masiku amenewo. Choncho Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu, kapena tingoleka?” Chauta adayankha kuti, “Pitaninso, pakuti maŵa ndidzaŵapereka m'manja mwanu.”
29Choncho Aisraele adaika anthu obisalira mozungulira mzinda wa Gibea.
30Adapita kukamenyana ndi Abenjamini tsiku lachitatu lake, nakhazika ankhondo ao kuti athire nkhondo mzinda wa Gibea monga masiku ena aja.
31Abenjamini nawonso adatuluka kukamenyana nawo anthuwo, napita chapatali ndithu ndi mzindawo. Ndipo monga mwa masiku onse, adayamba kuŵamenya koopsa ndi kupha Aisraele makumi atatu amene anali m'miseu yaikulu, ena mu mseu waukulu wa ku Betele, ena mu mseu waukulu wa ku Gibea ndiponso ena kwina koyera.
32Ndipo adati, “Taŵapirikitsa monga poyamba paja.” Koma Aisraele adati, “Tiyeni tithaŵe kuti apite ku miseu chapatali ndithu ndi mzinda wao.”
33Choncho Aisraelewo adanyamuka m'malo ao, nakandanda ku Baala-Tamara. Pamenepo Aisraele amene adaabisalira aja adatuluka m'malo ao kuzambwe kwa Geba.
34Aisraele osankhidwa amene adabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibea analipo 10,000, ndipo nkhondo idalimba kumeneko. Koma Abenjamini sankadziŵa kuti zoopsa zili pafupi kuŵagwera.
35Tsono Chauta adagonjetsa Abenjamini pamaso pa Aisraele, ndipo Aisraelewo adaononga ankhondo a Abenjamini okwanira 25,100 tsiku limenelo.
36Motero Abenjamini adaona kuti agonjetsedwa.
Aisraele agonjetsa adani ao pa nkhondo.Paja gulu lalikulu la Aisraele lidaathaŵa Abenjamini chifukwa linkadalira anthu aja amene lidaaŵaika kuti abisalire mzinda wa Gibea.
37Apo anthu obisalira aja adafulumira kuuthira nkhondo mzinda wa Gibeawo. Adapha anthu onse amumzindamo ndi lupanga.
38Tsono chizindikiro chimene adaapangana Aisraele a gulu lalikulu ndi anthu obisalira aja chinali chakuti, akafukiza utsi wambiri ngati mtambo mumzindamo,
39Aisraele ambiriwo abwerere kudzamenya nkhondo. M'menemo nkuti Abenjamini atayamba kuŵamenya Aisraelewo koopsa ndi kupha anthu makumi atatu. Iwo ankati, “Ndithu, taŵapha monga poyamba paja.”
40Koma pamene utsi wachizindikiro uja udayamba kuti tolotolo kukwera kumwamba mumzindamo, Abenjamini adayang'ana kumbuyo, nkuwona mu mzinda wonsewo utsi uli tolotolo kukwera kumwamba.
41Pomwepo Aisraele adabwerera ndipo Abenjamini adayamba kuwopa ndi kutaya mtima, pakuti adaaona kuti zoopsa zili pafupi kuŵagwera.
42Nchifukwa chake Abenjamini adayamba kuthaŵa Aisraelewo, naloŵa njira ya ku dondo. Koma nkhondo idaŵapeza, ndipo adaphedwa ndi Aisraele amene ankatuluka mu mzinda.
43Adaŵazinga Abenjaminiwo naŵapirikitsa ndi kuŵaonongeratu osaŵachitira chifundo mpaka ku dera la Gibea kuvuma kwake.
44Abenjamini amene adaphedwa analipo 18,000. Onsewo anali anthu olimba mtima kwambiri.
45Anthu amene adatsalira, adatembenuka nathaŵira ku dondo ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowo anthu 5,000 adaphedwa m'miseu yaikulu. Adaŵapirikitsabe Abenjaminiwo mkaka ku Gidomu, naphanso enanso 2,000.
46Choncho Abenjamini onse amene adafa tsiku limenelo adakwanira ankhondo 25,000. Onsewo anali anthu olimba mtima kwambiri.
47Koma anthu 600 okha adakafika ku dondo ku thanthwe la Rimoni, nakakhala ku thanthwe la Rimoniko miyezi inai.
48Tsono Aisraele adabwerera m'mbuyo kukamenyana ndi Abenjamini otsala, naŵapha ndi lupanga, anthu ndi nyama zomwe, pamodzi ndi zonse zimene adakumana nazo. Ndipo adatentha mizinda yonse imene adaipeza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.