Daniel Greek 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Phwando la Belisazara

1Tsiku lina mfumu Belisazara adakonza phwando lalikulu naitana akalonga ake okwanira chikwi chimodzi. Paphwandopo adamwa vinyo pamodzi ndi anthu onsewo.

2Pamene ankamwa, Belisazara adalamula kuti abwere ndi zikho ndi ziŵiya zagolide ndi zasiliva zimene bambo wake Nebukadinezara adaalanda ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Ankafuna kumweramo iyeyo pamodzi ndi akalonga ake, nduna zake, akazi ake enieni ndiponso akazi ake apambali.

3Motero adabwera nazo zikho ndi ziŵiya zagolide ndi zasiliva zimene zidaalandidwa ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo mfumu idayamba kumweramo pamodzi ndi akalonga ake, nduna zake, akazi ake enieni ndi akazi ake apambali.

4Alikumwa choncho, ankatamanda milungu yao yagolide, yasiliva, yamkuŵa, yachitsulo, yamtengo ndi yamwala.

5Mwadzidzidzi padaoneka dzanja la munthu. Dzanjalo lidayamba kulemba pa khoma la nyumba ya mfumu, kuyang'anana ndi nyale. Mfumuyo nkumapenyetsetsa dzanjalo likulemba.

6Pamenepo kumaso kwake kudasinthika, m'kamwa fuu ndi mantha, m'nkhongono zii, maondo gwedegwede!

7Mfumu Belisazara adafuula kuitana oombeza, alauli ndi alosi kuti abwere. Adauza anzeru a ku Babiloniwo kuti, “Aliyense amene angathe kuŵerenga zimene zalembedwa apazi ndi kundiwuza tanthauzo lake, ndidzamuveka zovala zofiirira, ndi ukufu wagolide m'khosi. Adzakhala wolamulira wachitatu m'dziko muno.”

8Anzeru onse a mfumuyo adabwera, koma sadathe kuŵerenga kapena kuimasulira mfumu zolembedwazo.

9Pamenepo mfumu Belisazara adaopsedwa kwambiri, m'thupi monse kungoti zii. Akalonga akenso adangoti kakasi.

10Mfumukazi itamva mau a mfumu ndi a akalonga ake, idaloŵa m'chipinda cha phwando. Ndipo idati, “Mukhale ndi moyo wautali amfumu. Pepani, musavutike, nkhope yanu isatumbuluke.

11M'dziko mwanu muno muli munthu amene ali ndi nzeru za milungu yoyera. Pamene bambo wanu anali mfumu, munthu ameneyo adawonetsa maganizo akucha, kumvetsa zinthu, ali ndi nzeru ngati za milungu. Motero mfumu Nebukadinezara bambo wanu adamsandutsa mkulu wa amatsenga, oombeza, alauli ndi alosi.

12Munthu ameneyu dzina lake lenileni ndi Daniele, koma mfumu idamutcha Belitesazara. Iyeyu ali ndi nzeru zamtundu, ndi wodziŵa zinthu ndiponso ali ndi luso lomasulira maloto, kufotokoza miyambi ndiponso mau ophiphiritsa. Mumuitane, adzatiwuze kumasula kwake kwa zimenezi.”

Daniele amasulira malembo

13Motero adabwera naye Daniele pamaso pa mfumu. Mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi Daniele uja ndiwe, mmodzi mwa akapolo amene mfumu, bambo wanga, adaŵatenga ku Yuda?

14Ndamvatu kuti uli ndi nzeru za milungu yoyera, ndipo kuti ndiwe wa maganizo akucha, womvetsa zinthu ndiponso wa nzeru zabasi.

15Anthu anzeru ndi oombeza adabwera nawo kuno kuti aŵerenge malembo aŵa ndi kundiwuza tanthauzo lake, koma adalephera.

16Tsono ndamva kuti iweyo umatha kumasula maloto ndiponso mau ophiphiritsa. Ngati uŵerenga malembo ameneŵa nundiwuza tanthauzo lake, ndidzakuveka zovala zofiirira, ndiponso ukufu wagolide m'khosi, ndipo udzakhala wolamulira wachitatu m'dziko muno.”

17Daniele adayankha mfumu kuti, “Pepani amfumu, koma mphatsozo musunge, kapena mupatse ena. Ine ndingokuŵerengerani chabe zimene zalembedwazo ndi kukuuzani tanthauzo lake.

18Inu mbuyanga mfumu, Mulungu Wopambanazonse adapatsa atate anu Nebukadinezara mphamvu, ulemerero ndi ufumu.

19Chifukwa cha mphamvu zimene adampatsazo, anthu a mitundu yonse, a mafuko onse ndi a zilankhulo zosiyanasiyana, ankanjenjemera pamaso pake ndi kuchita naye mantha. Akafuna kupha munthu, ankamuphadi; akafuna kumleka, ankamleka. Akafuna kukweza munthu, ankamukweza; akafuna kutsitsa munthu, ankamutsitsadi.

20Koma pamene adayamba kudzitama nkusanduka wokanika, namachita zankhalwe, adachotsedwa pa mpando wake waufumu, ndipo adataya malo ake aulemerero.

21Adampirikitsira kutali ndi anthu, ndipo mtima wake udasanduka ngati wa nyama. Ankakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndipo ankadya udzu ngati ng'ombe. Thupi lake lidanyowa ndi mame, mpaka adadziŵa kuti Mulungu Wopambanazonse ndiye mfumu yolamulira maufumu a anthu, ndiyenso amene amampatsa aliyense monga momwe Iye afunira.

22Koma inu Belisazara, mwana wake wa Nebukadinezarayo, simudadzichepetse, ngakhale munkazidziŵa zonsezi.

23Mwadzikuza motsutsana ndi Ambuye a Kumwamba. Zikho za ku Nyumba ya Mulungu abwera nazo ku phwando lanu. Ndipo inuyo mwamweramo vinyo pamodzi ndi akalonga anu, nduna zanu, akazi anu enieni ndi akazi anu apambali. Mwatamanda milungu yasiliva, yagolide, yamkuŵa, yachitsulo, yamtengo ndi yamwala, imene siiwona kapena kumva kapena kudziŵa kanthu. Simudalemekeze Mulungu amene akusunga m'manja mwake mpweya wanu, ndi kuyang'anira mayendedwe anu onse.

24“Nchifukwa chake Mulungu watuma dzanjalo kuti lidzalembe mau ameneŵa.

25Mau amene adalembedwawo ndi aŵa: MENE, MENE, TEKELE, PARASINI.

26Tsono tanthauzo lake ndi ili: MENE ndiye kuti, Mulungu waŵerenga masiku a ufumu wanu ndipo wauthetsa.

27TEKELE ndiye kuti inu mwayesedwa pa sikelo, ndipo mwapereŵera.

28PARASINI ndiye kuti ufumu wanu wagaŵidwa, ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Apersi.”

29Pomwepo Belisazara adalamula kuti Daniele amuveke zovala zofiirira zaufumu, ndipo kuti amuveke ukufu wagolide m'khosi. Kenaka adalengeza kuti akhale wolamulira wachitatu m'dzikomo.

30Usiku womwewo, Belisazara mfumu ya ku Babiloni adaphedwa.

31Ndipo Dariusi Mmedi adalanda ufumuwo. Nthaŵi imeneyo nkuti Dariusi ali wa zaka 62.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help