Mik. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yerusalemu mzinda wa Chauta(Yes. 2.1-4)

1Pa masiku akudzaŵa,

phiri la Nyumba ya Chauta

adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse,

lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse.

Mitundu yonse ya anthu

idzathamangira ku phiri limenelo.

2Anthu a mitundu yambiri adzabwera,

ndipo adzanena kuti,

“Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta,

ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe,

ndipo adzatiphunzitsa njira zake,

ndipo tiziyenda m'njira zakezo.”

Pakutitu nku Ziyoni

kumene kudzafumira malangizo akewo,

nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.

3 Yes. 2.4; Yow. 3.10 Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu,

adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu,

ngakhale akutali omwe.

Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu,

ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika.

Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga,

sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.

4 Zek. 3.10 Koma munthu aliyense azidzangodzikhalira mwamtendere

patsinde pa mtengo wake wamphesa,

ndi patsinde pa mkuyu wake.

Palibe amene adzaŵachititsa mantha,

pakuti mwiniwake, Chauta Wamphamvuzonse,

wanena zimenezi.

5Mitundu yonse ya anthu imayenda,

uliwonse m'njira ya mulungu wake;

koma ife tidzayenda m'njira ya Chauta,

Mulungu wathu,

mpaka muyaya.

Aisraele adzabwerera kwao

6Chauta akunena kuti,

“Pa tsiku limenelo,

ndidzasonkhanitsa opuwala,

ndidzakusa amene adachotsedwa kwao,

ndiponso amene ndidaŵalanga.

7Opundukawo ndidzaŵasandutsa anthu anga otsala,

amene adachotsedwa kwao

ndidzaŵasandutsa mtundu wamphamvu.

Ine Chauta ndidzakhala mfumu yao pa phiri la Ziyoni,

kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya.

8“Tsono iwe Ziyoni,

nsanja yotetezera nkhosa zanga,

phiri la anthu anga,

zimene ndidaakulonjeza zidzachitikadi.

Ufumu wako wakale uja udzakubwereranso,

Anthu a ku Yerusalemu ufumu wao uja udzafikanso.”

9Kodi ukuliriranji mokuŵa chonchi mzinda iwe?

Ukusaukiranji ngati mkazi

pa nthaŵi yake yochira?

Kodi ndiye kuti ulibe mfumu,

kapena phungu wokulangiza?

10Muphiriphithe ndi kubuula,

inu anthu a ku Ziyoni,

ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.

Pakuti tsopano mudzachoka mumzindamo,

mukakhala mumidzi.

Mudzachotsedwa kupita ku Babiloni.

Komabe kumeneko mudzapulumutsidwa,

kumeneko Chauta adzakuwombolani kwa adani anu.

11Tsopano mitundu yambiri yasonkhana

kuti imenyane ndi iwe Ziyoni.

Ikunena kuti, “Tiyeni timuipitse,

tiwone kutha kwake kwa mzinda wa Ziyoniwu.”

12Koma anthuwo maganizo a Chauta saŵadziŵa,

zimene Iye akukonzekera, iwo sazimvetsa.

Sadziŵa kuti Iye waŵaunjika

ngati mitolo ya tirigu pa malo opunthira.

13Yamba kupuntha iwe Ziyoni,

ndidzakusandutsa wamphamvu

ngati nkhunzi ya nyanga zachitsulo,

ngati nkhunzi ya ziboda zamkuŵa.

Udzatswanya mitundu yambiri ya anthu,

zimene adapindula udzazipereka kwa Chauta,

chuma chao udzachipereka kwa Ambuye

a dziko lonse lapansi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help