1Nthaŵi imeneyi Aisraele okhala ku Yudeya adamva zimene Holofernesi, mtsogoleri wamkulu wa ankhondo a Nebukadinezara, mfumu ya Aasiriya, adaŵachita maiko ena, ndi za m'mene adafunkhira ndi kupasula nyumba za milungu yao.
2Nchifukwa chake ankada nkhaŵa ndi kunjenjemera poganiza zimene Holofernesi ankadzauchita mzinda wa Yerusalemu ndi Nyumba ya Ambuye, Mulungu wao.
3Paja anali atangobwerera chatsopano kuchokera ku ukapolo, ndi kukhalanso pamodzi m'dziko la Yudeya. Ndipo Nyumba ya Mulungu, guwa lake ndi ziŵiya zake, zimene adani adaaziipitsa, anali atangozipatulira Mulungu posachedwa.
4Motero adatuma amithenga ku madera onse a Samariya, ku Kona, Betoroni, Belemaini, Yeriko, Khoba, Aesora ndi ku chigwa cha Salemu.
5Nthaŵi yomweyonso adakhazika ankhondo ao pamwamba pa mapiri onse, ndipo adazinga ndi malinga midzi yokhala m'mapirimo. Kenaka anasonkhanitsa tirigu kuti akonzekere kumenya nkhondo, poti anali atakolola posachedwapa.
6Mkulu wa ansembe Yowakimu, amene ankakhala ku Yerusalemu pa nthaŵiyo, adalembera kalata anthu okhala m'mizinda ya Betuliya ndi Betomesitaimu imene ikuyang'anana ndi Esdreloni, m'mbali mwa chigwa cha Dotani.
7Adaŵauza kuti akhazike ankhondo pa mipata ya pakati pa mapiri, imene adani akadadzera pofuna kulanda dziko la Yuda. Pamenepo chinali chapafupi kuŵabweza adaniwo, poti njira zake zinali zophaphatiza, zongolola anthu aŵiriaŵiri okha kudutsapo.
8Tsono Aisraele adatsata zimene adaŵalamula mkulu wa ansembe Yowakimu ndi gulu la akuluakulu atachita msonkhano ku Yerusalemu.
Aisraele apemphera9Anthu onse a ku Israele adalira kwa Mulungu ndi mtima wonse, ndipo adadzichepetsa posala zakudya.
10Yon. 3.7, 8; Esr. 4.1-3Iwo pamodzi ndi akazi ao, ana ao, ziŵeto zao, ndi ena onse okhala nao, antchito ndi akapolo omwe, adavala ziguduli m'chiwuno.
11Aisraele onse a ku Yerusalemu, akazi ndi ana omwe, adagwada pansi moŵeramitsa mutu, pakhomo pa Nyumba ya Mulungu, atadzola phulusa ku mutu, nayala ziguduli zao pamaso pa Ambuye.
12Adayalanso ziguduli pozungulira guwa. Kenaka onse pamodzi adalira kwa Mulungu wa Israele kuti ana ao asagwidwe, akazi ao asatengedwe, mizinda ya makolo ao isaonongedwe, ndipo Nyumba ya Mulungu isaipitsidwe ndi kunyozedwa, kuwopa kuti anthu a mitundu inawo angakondwerere mwachipongwe.
13Esr. 4.16Ambuye adamva pemphero laolo naŵamvera chifundo, chifukwa m'dziko lonse la Yuda ndi ku Yerusalemu anthu adasala zakudya masiku ambiri pakhomo pa Nyumba ya Ambuye Amphamvuzonse.
14Yow. 2.17Yowakimu mkulu wa ansembe, pamodzi ndi ansembe onse oima pamaso pa Ambuye namatumikira m'Nyumba ya Mulungu, ziguduli zili m'chiwuno, ankapereka kosalekeza nsembe zopsereza, pamodzi ndi zoperekera malumbiro ndi zopereka zaufulu za anthu.
15Atadzola phulusa pa zisoti zao, ankapemphera kwa Ambuye ndi mau okweza kuti achitire chifundo fuko lonse la Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.