1“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni.
2Mk. 4.24M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.
3Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe?
4Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene m'maso mwako momwe muli chimtengo?
5Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.
6“Musamapatsa agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zamtengowapatali, kuwopa kuti zingazipondereze, kenaka nkukutembenukirani ndi kukukadzulani.
Za kupemphera ndi mtima wokhulupirira(Lk. 11.9-15)7 2Es. 2.13 “Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
8Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
9Ndani mwa inu, mwana wake atampempha buledi, iye nkumupatsa mwala?
10Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka?
11Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
12Tob. 4.15; Lk. 6.31Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Za chipata chophaphatiza(Lk. 13.24)13 Mphu. 15.17 “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.
14Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Za mtengo ndi zipatso zake(Lk. 6.43-44)15“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
16Mphu. 27.6Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu?
17Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa.
18Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai.
19Mt. 3.10; Lk. 3.9Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto.
20Mt. 12.33Choncho mudzaŵadziŵira zochita zao.
Za pa tsiku lachiweruzo(Lk. 13.25-27)21“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.
22Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’
23Mas. 6.8Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’
Za anthu aŵiri omanga nyumba(Lk. 6.47-49)24“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.
25Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.
26Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga.
27Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”
Za kaphunzitsidwe ka Yesu28 Mk. 1.22; Lk. 4.32 Yesu atatsiriza kunena zimenezi, anthu onse aja adadabwa ndi kaphunzitsidwe kake,
29chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.