Owe. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ayuda ndi Asimeoni agwira Adonibezeki.

1Yoswa atafa, Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Ndani mwa ife amene ayambe kulimbana ndi Akanani, kumenyana nawo nkhondo?”

2Chauta adayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo limene lipite. Ndikuŵapatsa dzikolo m'manja mwao.”

3Pamenepo Ayuda adauza abale ao, anthu a fuko la Simeoni, kuti, “Tiyeni tipite limodzi m'dziko limene Chauta adagaŵira ife, kuti tikamenyane ndi Akanani. Pambuyo pake nafenso tidzapita nanu limodzi m'dziko limene adagaŵira inu.” Choncho Asimeoni adatsakana nawo.

4Onsewo adapita, ndipo Chauta adapereka Akananiwo m'manja mwao pamodzi ndi Aperizi omwe. Ndipo adagonjetsa anthu 10,000 ku Bezeki.

5Kumeneko Ayuda adakumana ndi ankhondo a mfumu Adonibezeki, ndipo adamenyana nawo; adaŵagonjetsa Akanani ndi Aperizi omwe.

6Adonibezekiyo adathaŵa, koma adamthamangira namgwira, ndipo adadula zala zake zazikulu zakumanja ndiponso zala zake zazikulu zakumwendo.

7Apo Adonibezeki adati, “Mafumu makumi asanu ndi aŵiri oduka zala zazikulu zakumanja ndi zakumwendo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu wandichita zomwe ndidaŵachita iwowo.” Anthu ake adapita naye ku Yerusalemu ndipo iye adafera komweko.

Ayuda agonjetsa Yerusalemu ndi Hebroni.

8Pambuyo pake Ayuda adathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, naulanda. Adapha anthu ambiri, natentha mzinda wonsewo ndi moto.

9Kenaka Ayudawo adapita kukamenyana ndi Akanani amene ankakhala m'dziko lamapiri, m'dziko la Negebu lakumwera, ndiponso m'zigwa.

10Adakalimbananso ndi Akanani amene ankakhala ku Hebroni, (mzinda umene kale ankautchula kuti Kiriyati-Ariba). Kumeneko adagonjetsa mabanja a Sesai, Ahimani ndiponso Talimai.

Otiniyele agonjetsa mzinda wa Debiri.(Yos. 15.13-19)

11Kuchokera kumeneko anthu a ku Yuda aja adapita kukalimbana ndi anthu a ku Debiri. Mzinda umenewu kale unkatchedwa Kiriyati-Sefere.

12Tsono Kalebe adati, “Mkulu wa ankhondo amene athire nkhondo mzinda wa Kiriyati-Sefere, naulanda, ndidzampatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.”

13Mng'ono wake wa Kalebe, Otiniyele, mwana wa Kenazi, adaulanda mzindawo. Choncho Kalebe adampatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.

14Tsiku lina, Akisayo atafika, Otiniyele adamuumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo wake. Tsono Akisa atatsika pa bulu wake, Kalebe adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kanthu?”

15Iye adayankha kuti, “Ndimati mundipatseko mphatso. Popeza kuti mwandikhazika m'dziko la Negebu lopanda madzi, mundipatsenso akasupe a madzi.” Pamenepo Kalebe adampatsa akasupe akumtunda ndi akuchigwa omwe.

Ayuda ndi Abenjamini agonjetsa adani ao.

16Tsono zidzukulu za Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zidapita nawo limodzi anthu a fuko la Yuda kuchokera ku mzinda wamigwalangwa mpaka ku chipululu chimene chili kumwera kwa Aradi, m'dziko la Yuda. Kumeneko adakakhala ndi Aamaleke.

17Ayuda adatsakana ndi abale ao Asimeoni ndipo adagonjetsa Akanani amene ankakhala mu mzinda wa Zefati, naononga mzindawo kwathunthu. Choncho mzindawo adautcha Horima.

18Ayuda adalandanso mzinda wa Gaza ndi dziko lake lonse lozungulira, Asikeloni ndi dziko lake lonse lozungulira, ndiponso Ekeroni ndi dziko lake lonse lozungulira.

19Chauta adaŵathandiza Ayuda, ndipo Ayudawo adalanda dziko lamapiri, koma sadathe kupirikitsa nzika zam'chigwa, chifukwa chakuti zinali ndi magaleta achitsulo.

20Yos. 15.13, 14 Mzinda wa Hebroni udapatsidwa kwa Kalebe, monga adaanenera Mose. Ndipo Kalebeyo adapirikitsa mafuko atatu a Anaki mumzindamo.

21Yos. 15.63; 2Sam. 5.6; 1Mbi. 11.4 Koma Abenjamini sadapirikitse Ayebusi amene ankakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusi akukhala nawobe Abenjamini mu Yerusalemu mpaka pano.

Mafuko a Yosefe agonjetsa Betele.

22Mafuko a Yosefe nawonso adapita kukalimbana ndi mzinda wa Betele, ndipo Chauta anali nawo iwowo.

23Adatuma anthu oti akazonde Betele, (mzinda umene kale ankautchula Luzi).

24Anthu ozondawo adaona munthu akutuluka mumzindamo namuuza kuti, “Chonde tatidziŵitsaniko njira yoloŵera mumzindamu, ife tikuchitirani zabwino.”

25Munthuyo adaŵasonyeza njira yoloŵera mumzindamo. Iwo aja adapha anthu onse amumzindamo ndi lupanga, koma munthu uja adamleka osamupha, pamodzi ndi banja lake.

26Munthuyo adapita ku dziko la Ahiti nakamangako mzinda nkuutcha dzina loti Luzi. Limenelo ndilo dzina lake mpaka pano.

Anthu amene Aisraele sadaŵapirikitse.

27 Yos. 17.11-13 Koma a fuko la Manase sadapirikitse nzika za mu Beteseani ndi za m'midzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mu Taanaki ndi za m'midzi yake yozungulira. Sadapirikitsenso nzika za mu Dori ndi za m'midzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mu Ibleamu ndi za m'midzi yake yozungulira. Nazonso nzika za mu Megido ndi za m'midzi yake yozungulira sadazipirikitse. Choncho Akanani adapitirirabe kukhala m'dzikomo.

28Pamene Aisraele adasanduka amphamvu, adayamba kuŵagwiritsa Akananiwo ntchito yaukapolo, koma sadaŵapirikitse.

29 Yos. 16.10 Aefuremu sadapirikitse Akanani amene ankakhala mu Gezere. Choncho Akananiwo ankakhala pakati pao ku Gezereko.

30Azebuloni sadapirikitse nzika za mu Kitironi ndi nzika za mu Nahaloli. Choncho Akananiwo ankakhala pakati pao nasanduka oŵagwirira ntchito yaukapolo.

31Aasere sadapirikitse nzika za mu Ako, nzika za mu Sidoni, nzika za mu Alabu, nzika za mu Akizibu, nzika za mu Heliba, nzika za mu Afiki ndiponso nzika za mu Rehobu.

32Koma Aasere adakhala pakati pa Akanani, nzika za dzikolo, pakuti sadaŵapirikitse Akananiwo.

33Anafutali sadapirikitse nzika za mu Betesemesi ndi nzika za mu Betanati, koma ankakhala pakati pa Akananiwo, nzika za dzikolo. Komabe nzika za mu Betesemesi ndi za mu Betanati ankazigwiritsa ntchito yaukapolo.

34Aamori adapirikitsira anthu a fuko la Dani ku dziko lamapiri ndipo sadaŵalole kuti atsikire ku zigwa.

35Aamori sadachoke koma ankakhalabe ku phiri la Heresi, ku Aiyaloni, ndiponso ku Salibimu. Koma a fuko la Yosefe adasanduka amphamvu, nagwiritsa Aamoriwo ntchito yaukapolo.

36Tsono malire a Aamori adayambira ku chikwera cha Akirabimu, nkuloŵera ku Sela, napitirira kumapita chakumapiri ndithu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help