1 Chiv. 15.3 Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati,
“Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana,
waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe.
2 Mas. 118.14; Yes. 12.2 Chauta ndiye mphamvu zanga,
ndiye amene ndimamuimbira,
ndiye chipulumutso changa.
Iye ndiye Mulungu wanga,
ndipo ndidzamtamanda.
Ndiye Mulungu wa atate anga,
ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
3Chauta ndi wankhondo,
Chauta ndilo dzina lake.
4“Chauta adaponya m'nyanja magaleta a Farao
pamodzi ndi gulu lake lankhondo,
adammizira atsogoleri ake amphamvu m'Nyanja Yofiira.
5Nyanja yozamayo idaŵaphimba onse,
adamira mpaka pansi pa nyanja ngati miyala.
6Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero,
chifukwa cha nyonga zake,
dzanja lanu lamanja limatswanya adani.
7Mumagonjetsa adani anu ndi ulemerero wanu wopambana.
Ukali wanu woyaka ngati moto
ukuŵatentha ngati mapesi.
8Mutauzira mpweya wanu,
madzi adaunjikana pa malo amodzi.
Madzi oyenda adangoima kuti chilili, ngati khoma.
Nyanja yozamayo idalimba mpaka pansi pake.
9Mdani uja adati,
‘Ndidzaŵalondola nkuŵagwira.
Chuma chao ndidzachigaŵagaŵa,
ndipo mtima wanga udzakhutira nacho.
Ndidzasolola lupanga,
ndipo ndidzaŵaononga ndi dzanja langa.’
10Koma Inu mudangouzira ndi mphepo yanu,
ndipo nyanja idaŵamiza.
Adangomira ngati chitsulo mpaka pansi pa madzi.
11“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu?
Ndani amafanafana ndi Inu,
amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu?
Ndani amafanafana nanu,
Inu amene muli oopsa
chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
12Mudatambalitsa dzanja lanu lamanja,
ndipo nthaka idaŵameza.
13“Koma anthu amene mudaŵaombola,
mudaŵatsogolera ndi chikondi chanu chosasinthika.
Mudaŵatsogolera ku malo anu oyera ndi mphamvu zanu.
14Anthu a mitundu ina amva mbiriyi,
ndipo anjenjemera ndi mantha.
Mantha oopsa aŵagwira Afilisti.
15Tsopano lino mafumu a ku Edomu ataya mtima.
Atsogoleri a ku Mowabu ayambapo kunjenjemera.
Onse a ku Kanani agooka m'nkhongono.
16Onsewo agwidwa ndi mantha oopsa.
Iwo akhala chete ngati mwala,
chifukwa cha kuwopa mphamvu zanu zazikulu.
Angokhala chete
mpaka anthu anu, Inu Chauta, atabzola,
anthu amene mudaŵaombola mu ukapolo.
17Mudzaŵaloŵetsa ndi kuŵakhazika pa phiri lanu,
pa malo amene Inu Chauta mudaŵapanga
kuti akhale anu,
m'nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga.
18Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya.”
Nyimbo ya Miriyamu19Pamene akavalo a Farao, pamodzi ndi magaleta ndi okwerapo ake omwe, adaloŵa m'nyanja, Chauta adaŵabweza madziwo, ndipo adamiza onsewo. Koma Aisraele adayenda pouma m'kati mwa nyanjayo.
20Miriyamu, mneneri wamkazi, mlongo wa Aroni, adatenga kang'oma, ndipo akazi onse adamtsata pambuyo akuimba ting'oma, ndi kumavina.
21Ndipo Miriyamu adaŵaimbira iwowo nyimbo yakuti,
“Imbirani Chauta chifukwa wapambana,
waponya m'nyanja akavalo
pamodzi ndi okwerapo ake omwe.”
Za madzi oŵaŵa22Tsono Mose adatsogolera Aisraele ku Nyanja Yofiira kuja nakaloŵa m'chipululu cha Suri. Adayenda m'menemo masiku atatu, osapeza madzi.
23Ndipo adakafika ku Mara, koma kumeneko madzi ake anali oŵaŵa, kotero kuti sadathe kuŵamwa. Nchifukwa chake malowo adaŵatcha kuti Mara.
24Apo anthu aja adadandaulira Mose, namufunsa kuti, “Kodi ife timwa chiyani?”
25Mphu. 38.5Tsono Mose adapemphera dzolimba kwa Chauta, ndipo Chauta adamuwonetsa kamtengo. Mose adaponya kamtengoko m'madzi, ndipo madziwo adaleka kuŵaŵako.
Kumeneko Chauta adapatsa anthuwo lamulo lokhazikika, ndipo adaŵayesanso komweko.
26Adati, “Mukamandimvera Ine Chauta, Mulungu wanu, kumachita zolungama, kumasamala malamulo anga ndi kumamvera zimene ndikukulamulani, sindidzakulangani ndi nthenda zilizonse zimene ndidalanga nazo Aejipito. Ine ndine Chauta amene ndimakuchiritsani.”
27Pambuyo pake adakafika ku Elimu kumene kunali akasupe khumi ndi aŵiri, ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi aŵiri. Tsono adamanga mahema ao kumeneko pafupi ndi madzi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.