1Munthu aliyense adalembedwa ntchito yakalavulagaga,
ana a Adamu amasenza goli lolemera,
kuyambira pamene adatuluka m'mimba mwa amai ao,
mpaka pamene adzabwerere ku nthaka, mai wa onse.
2Chimene chimaika m'mitima mwao maganizo opweteka
ndiponso mantha, ndi nkhaŵa yodikira tsiku la kufa kwao.
3Ngakhale munthu akhale pa mpando waufumu ndi
waulemerero,
kapena akhale wosauka wongoti mbwerekete pa
fumbi ndi pa phulusa,
4ngakhale munthu akhale wovala zamlangali ndi
nsangamutu yaufumu,
kapena akhale wovala chiguduli,
5onsewo amangopeza ukali ndi nsanje, nkhaŵa ndi mavuto,
kuwopa imfa, kuyambana ndiponso ndeu.
Akapita kukagona usiku,
kutulo amangoganiza zina ndi zina za mtundu womwewo.
6Mwina angousa pang'ono, mwina osausa konse,
ndipo amavutika kwambiri kutuloko,
monga momwe amachitira ali maso.
Amavutika ndi maloto oŵaŵa,
ngati munthu wothaŵa ku malo a nkhondo.
7Pamene ali pafupi kupulumuka, amatsitsimuka,
nkumadabwa kuti amachita mantha popanda chifukwa.
8Zolengedwa zonse, anthu kapena nyama,
anthu ochimwa ndiye kasanunkaŵiri,
9zimapeza imfa, magazi, kumenyana, lupanga,
masoka, njala, mazunzo ndi mliri.
10Zonsezi zidalengedwa chifukwa cha anthu ochimwa,
ndipo chigumula chija chidachitika chifukwa cha iwowo.
11Zonse zochokera ku nthaka zimabwereranso ku nthaka,
ndipo zonse zochokera m'madzi zimabwereranso ku nyanja.
12Ziphuphu ndi zosalungama, zonsezi zidzatha,
koma chikhulupiriro choona chidzakhalapo mpaka muyaya.
13Chuma cha anthu oipa chidzaphwa ngati mtsinje,
chidzangozimirira ngati mphezi yogunda
mwamphamvu nthaŵi yamvula.
14Munthu wachifundo adzapeza kusangalala,
koma anthu osamvera Malamulo adzaonongeka.
15Anthu osapembedza Mulungu sadzakhala ndi adzukulu ambiri,
ali ngati mitengo yozika mizu yopanda mphamvu pa mwala.
16Bango lomera m'mbali mwa mtsinje,
adzalizula asanazule udzu wina.
17Kuchita zachifundo ndi ngati munda wodalitsidwa,
kupatsa mwaufulu nchinthu chokhala nthaŵi zonse.
18Amapeza bwino munthu amene ali pa ntchito
ndiponso munthu amene amadziimira payekha,
koma wopeza chuma amakondwera koposa aŵiriwo.
19Munthu akakhala ndi ana namanga mzinda, amatchuka,
komabe kukhala ndi mkazi wabwino nkwabwino koposa.
20Vinyo ndi zoimbaimba zimasangalatsa mtima,
koma kukonda nzeru ndiye chinthu chopambana zonsezo.
21Zitoliro ndi azeze zimakometsa nyimbo,
koma liwu lokongola loimba ndi pakamwa
limapambana zonsezi.
22Maso amakhumbira maonekedwe abwino ndi okongola,
koma mmera wobiriŵira wam'minda umaposa zonsezi.
23Kukumana ndi bwenzi kapena mnzako nchokondwetsa,
koma mkazi ndi mwamuna wake akakumana,
nchokondwetsa koposa.
24Achibale ndi ogwirizana nawo ali bwino pa
nthaŵi yamavuto,
koma kupereka zachifundo kumapulumutsa kopambana.
25Golide ndi siliva zimalimbitsa munthu,
koma malangizo abwino ndiye chinthu chopambana zonsezo.
26Chuma ndi mphamvu zimalimbitsa mtima,
koma kuwopa Ambuye kumapambana ziŵirizo.
Munthu woopa Ambuye sasoŵa kanthu,
sayeneranso kufunafuna womthandiza.
27Kuwopa Ambuye kuli ngati munda wodalitsidwa,
kumateteza munthu kupambana mbiri yabwino kwabasi.
28Mwana wanga, usakhale munthu wopemphapempha,
ndi bwino kufa kupambana kupemphapempha.
29Munthu wodalira chakudya cha mnzake
sakhala ndi moyo weniweni,
amaipitsa kum'mero kwake ndi chakudya cha wina.
Munthu wanzeru ndi wotsata mwambo amalewa zinthu zotere.
30Munthu wopanda manyazi amati kupempha nkwabwino,
koma m'mimba mwake muli moto woyaka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.