1 Deut. 22.30 Mbiri yawanda ponseponse yonena kuti pakati panu pali dama. Ndipo damalo ndi la mtundu wakuti ndi anthu akunja omwe sachita. Ndamva ndithu kuti munthu wina akukhala ndi mkazi wa bambo wake.
2Ndipo inu mukudzitukumulabe! Kwenikweni mukadayenera kumva chisoni, ndi kumchotsa pakati panu munthu amene adachita zimeneziyo.
3Kunena za ine, ngakhale sindili nanu pamodzi, komabe mtima wanga uli nanu ndithu. Mwakuti ndamuweruza kale munthu amene adachita zimeneziyo, monga ngati ndili nanu pamodzi.
4Tsono mutasonkhana m'dzina la Ambuye Yesu, inenso m'maganizo ndili nanu pomwepo, ndi mphamvu ya Ambuye athu Yesu,
5munthuyo mumpereke kwa Satana, kuti thupi lake liwonongedwe, ndipo pakutero mzimu wake udzapulumutsidwe pa tsiku la Ambuye.
6 Aga. 5.9 Pamenepo palibe choti inu nkunyadira ai. Kodi simuŵadziŵa mau aja akuti, “Chofufumitsira buledi chapang'ono chimafufumitsa mkate wonse?”
7Eks. 12.5Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Paska, adaphedwa kale ngati nsembe.
8Eks. 13.7; Deut. 16.3 Tiyeni tsono, tichite chikondwererocho, osati ndi chofufumitsira chakale chija cha uchimo ndi cha kuipa mtima, koma ndi buledi wosafufumitsa, wa kuyera mtima ndi wa choona.
9M'kalata imene ndidaakulemberani, ndidaakuuzani kuti musamayanjane nawo anthu adama.
10Sindiye kuti muziŵapewa anthu onse apansipano amene ali adama, aumbombo, achifwamba, kapena opembedza mafano ai. Kuti mutero kukadafunika kuti mungochokamo m'dziko lino lapansi.
11Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.
12 Deut. 13.5; 17.7 Nanga kuweruza anthu amene adakali kunja, ndi ntchito yanga ngati? Si koma amene ali mu mpingo ndiwo muyenera kuŵaweruza?
13Ndi Mulungu amene amaweruza anthu akunjawo. Paja mau a Mulungu akuti, “Munthu woipayo mumchotse pakati panu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.