1Tsono popeza kuti ndife ogwirizana ndi Mulungu pa ntchito yake, takupembani musaŵasandutse achabe madalitso amene Mulungu adakupatsani.
2Yes. 49.8 Paja Mulungu akuti,
“Pa nthaŵi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima,
ndidakumvera,
pa nyengo ya kupulumutsa anthu,
ndidakuthandiza.”
Mvetsani, ndi inotu nthaŵi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi Lerotu tsiku la chipulumutsolo.
Za kumva zoŵaŵa chifukwa cha Uthenga Wabwino3Sitifuna kupatsa anthu chifukwa chonyozera ntchito yathu, nchifukwa chake sitikhumudwitsa munthu aliyense ndi kanthu kalikonse.
4Koma pa zonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu pakupirira kwambiri m'masautso, m'zoŵaŵa ndiponso m'nkhaŵa.
5Ntc. 16.23Tidakwapulidwa, tidaponyedwa m'ndende, ndipo anthu adatiwukira mwachipolowe. Tidagwira ntchito kwambiri, mwina osagona tulo, osaona chakudya.
6Timatsimikiza kuti ndife atumiki a Mulungu pakuyera mtima, pakudziŵa zinthu mozama, pakuleza mtima, pakukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, mwa chikondi chosanyenga,
7mwa mau oona, ndiponso mwa mphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili m'dzanja lathu lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo.
8Anthu amatilemekeza, komanso amatinyoza. Amatinenera zoipa, komanso zabwino. Anthu amatiyesa onyenga, komabe ndife oona.
9Amatiyesa osadziŵika, komabe ndife odziŵika kwambiri. Amatiyesa anthu amene alikufa, komabe onani, tili moyo. Amatiyesa olangidwa, komabe sitidaphedwe.
10Amatiyesa achisoni, komabe ndife okondwa masiku onse. Amatiyesa amphaŵi, komabe timalemeretsa anthu ambiri. Amatiyesa opanda kanthu, komabe tili ndi zonse.
11Inu anthu a ku Korinto, talankhula nanu momasuka, ndipo tatsekula mtima wathu ndithu.
12Malo sakusoŵani mumtima mwathu, koma mumtima mwanu ndimo mukusoŵa malo.
13Ndikulankhula nanu ngati ana anga. Mutibwezere zomwezo zimene ifenso tidakuchitirani inu, pakutitsekulira mtima wanu.
Aŵachenjeza kuti azilewa zachikunja14Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?
15Kodi Khristu nkuvomerezana ndi Satana? Kodi mkhristu ndi mkunja angagaŵanenso chiyani pamodzi?
161Ako. 3.16; 6.19; Lev. 26.12; Ezek. 37.27 Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti,
“Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo.
Ndidzakhala Mulungu wao,
iwo adzakhala anthu angaanga.”
17 Yes. 52.11 Nchifukwa chake Ambuye akuti,
“Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula.
Musakhudze kanthu kosayera,
ndipo ndidzakulandirani.
18 2Sam. 7.14; 1Mbi. 17.13; Yes. 43.6; Yer. 31.9 Ndidzakhala Atate anu,
inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,
akutero Ambuye Mphambe.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.