1 Am. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Yonatani adazindikira kuti zinthu zikumuyendera bwino. Motero adasankhula anthu ena, naŵatuma ku Roma kuti akalimbitse ndi kutsimikiza kuyanjana kwa Ayuda ndi Aroma.

2Adatumizanso kwa Asparta ndi ku maiko ena makalata ofuna zokhazokhazo.

3Anthuwo adanka ku Roma, nakaloŵa m'nyumba ya bungwe la akuluakulu ndipo adati, “Yonatani, mkulu wa ansembe, pamodzi ndi akuluakulu a mtundu wa Ayuda, atituma kuti tidzayambitsenso chibwenzi ndi kugwirizana, monga zinaliri kale.”

4Tsono a ku Roma aja adaŵapatsa makalata kuti akaŵapereke kwa akukuakulu a ku maiko onse kumene ankayenera kudzerako, kuti potero aŵafikitse mwamtendere ku dziko la Yudeya.

5Naŵa mau a m'kalata imene Yonatani adaalembera Asparta:

6“Ndife Yonatani mkulu wa ansembe, akuluakulu a Ayuda, ansembe ndi Ayuda ena onse, tikupereka moni kwa abale athu Asparta.

7Kale Ariyo, amene anali mmodzi mwa mafumu anu, adaatumizira Oniyasi, mkulu wa ansembe athu, kalata yonena kuti ndinu abale athu. Inali ngati kalata yomwe tabwera nayoyi.

8Oniyasi adamlandira ndi ulemu munthu amene mudaamtuma, navomera mau a m'kalatayo, onena za kugwirizana ndi za chibwenzi.

9Kwenikweni ifeyo sitikuzisoŵa zimenezo, popeza kuti tili nawo mabuku oyera otilimbitsa mtima.

10Komabe tidaganiza zotuma anthu athu kwa inu, odzayambitsanso ubwenzi wachibale, kuti tingaoneke ngati alendo kwa inu. Taona kuti papita masiku ambiri kuyambira tsiku limene mudaatuma anthu anu.

11Tsono nthaŵi zonse ife timakumbukira inu pa masiku a chikondwerero chachikulu ndi pa masiku ena oyera, ndi popereka nsembe zathu ndi pakupemphera, monga kuyenera pokumbukira abale athu.

12Tikukondwerera ukulu wanu.

13Koma ife takhala tikuzunzika ndi zovuta ndi nkhondo zambiri zotipweteka, chifukwa mafumu otizungulira akhala akutithira nkhondo.

14Komabe pakati pa nkhondo zimenezo sitidafune kukuvutani, inuyo kapena oyanjana nafe kapena abwenzi athu.

15Pakutitu timalandira chithandizo kuchokera kumwamba, mwakuti tidapulumuka kwa adani athu, ndipo iwowa adathyoledwa.

16Nchifukwa chake tidasankhula Numeniyo, mwana wa Antioko ndi Antipatere, mwana wa Yasoni, nkuŵatuma kwa Aroma kuti tipale nawonso chibwenzi ndi kugwirizana monga kale.

17Tsono taŵalamula kuti adzerenso kwa inu, adzakupatseni moni ndi kupereka kwa inu kalata yathuyi yotsimikizanso za ubale wathu.

18Ndipo tikupempha kuti mutitumizire yankho lanu pa zimenezo.”

19Naŵa mau a m'kalata imene Asparta adatumizira Oniyasi:

20“Ndine Ariyo, mfumu ya Asparta, ndikupereka moni kwa Oniyasi, mkulu wa ansembe onse.

21Ena kuno adapeza m'buku lina mau onena kuti ife Asparta ndi inu Ayuda tili pa chibale, ndipo kuti tonse ndife a m'fuko la Abrahamu.

22Ndiye poti tadziŵa zimenezo, mudzachita bwino mukadzatilembera ndi kutiwuza m'mene inu muliri kwanuko.

23Ifenso tikukulemberani kuti ziŵeto zanu ndi chuma chanu ndi zathu, ndipo zathu ndi zanu. Talamula kuti amithenga athu akudziŵitseni zimenezo.”

Nkhondo ina ndi Demetriyo

24Ena adauza Yonatani kuti atsogoleri a ankhondo a Demetriyo adabwera ndi gulu lankhondo lalikulu kupambana lakale lija, kuti adzamenyane naye nkhondo.

25Atamva zimenezi, Yonatani adanyamuka ku Yerusalemu, napita kukakumana nawo ku dziko la Hamate, osaŵapatsa mpata woloŵera ndi nkhondo m'dziko lake.

26Adatuma azondi ku zithando zao zankhondo, ndipo iwo atabwerako, adamdziŵitsa kuti adaniwo ankakonzekera zodzaŵathira nkhondo Ayudawo ndi usiku.

27Dzuŵa litaloŵa, Yonatani adalamula ankhondo ake kuti akhale maso ndi kugwira zida zao m'manja, usiku wonse akhale okonzekera nkhondo. Tsono adaika asilikali olonda, kuzungulira zithando zao.

28Koma adani ao atamva kuti Yonatani ndi anthu ake ngokonzeka kumenyana nawo, adachita mantha, nayamba kuda nkhaŵa. Ndiye adangosonkha moto m'zithando zao, iwo nkuthaŵa.

29Yonatani ndi anthu ake sadadziŵe zimenezo mpaka m'maŵa, chifukwa ankaona moto ukuyaka.

30Tsono ngakhale Yonatani adaŵalondola, sadapezane nawo, chifukwa iwowo anali ataoloka kale mtsinje wa Eleutere.

31Pamenepo Yonatani adatembenukira kwa Aluya otchedwa Azabade. Adaŵagonjetsa nafunkha chuma chao.

32Atachoka kumeneko, adanka ku Damasiko nayendera dziko lonselo.

33Simoni nayenso adanyamuka, napita mpaka ku mzinda wa Askaloni ndi ku nyumba zankhondo zoyandikana nawo. Adatembenukira ku mzinda wa Yopa, naulanda modzidzimutsa,

34chifukwa anali atamva kuti anthu akumeneko ankaganiza zopereka nyumba yao yankhondo kwa anthu othandizana ndi Demetriyo. Motero Simoni adaikamo kagulu ka asilikali kuti kazilonda mzindawo.

35Atabwerera ku Yerusalemu, Yonatani adasonkhanitsa akuluakulu, napangana nawo zomanga malinga ankhondo ku Yudeya.

36Adapangana nawonso zokulitsa malinga a Yerusalemu, ndi kumanga khoma lalitali pakati pa boma lankhondo ndi mzinda kuti azilekanitse. Ankafuna kuti bomalo likhale palokha, kuti anthu ake asamachiteko malonda aliwonse.

37Choncho adasonkhana kuti amangenso mzinda. Chigawo china cha khoma lolambalala mtsinje wa Kedroni chakuvuma chinali chitagwa. Adakonzanso chigawo chotchedwa Kafenata.

38Simoni nayenso adamanga mzinda wa Adida ku Sefela, naulimbitsa, nkuikako zitseko ndi mipiringidzo yake.

Trifone agwira Yonatani

39Tsono Trifone adafuna kukhala mfumu ya ku Asiya, ndi kulanda ufumu wa Antioko.

40Komabe ankaopa, atadziŵa kuti Yonatani sadzamlola kuchita zimenezo mpaka kudzamenyana naye nkhondo. Choncho ankafuna kumgwira ndi kumupha. Adanyamuka, nabwera ku Betisane.

41Yonatani adadzamchingamira ndi ankhondo olimba mtima okhaokha 40,000, nafika ku Betisane.

42Poona kuti Yonatani wabwera ndi ankhondo ochuluka chotere, Trifone adaopa kulimbana naye.

43Adamlandira ndi ulemu, adamuyamikira pamaso pa abwenzi ake onse, nampatsa mphatso. Adalamula abwenzi ake ndi ankhondo ake kuti azimumvera chimodzimodzi ngati iye yemwe.

44Tsono adafunsa Yonatani kuti, “Chifukwa chiyani waŵatopetsa anthu onseŵa, chonsecho palibe nkhondo pakati pa inu ndi ife?

45Uŵabweze kwao. Ungosankhula anthu oŵerengeka okha kuti akuperekeze, kenaka upite nane ku Ptolemaisi. Ndidzakupatsa mzinda umenewo ndi nyumba zina zankhondo ndi magulu ena ankhondo otsala ndiponso atsogoleri omwe. Pambuyo pake ndidzachoka kupita kwathu. Zimenetu ndadzera kuno nzimenezi.”

46Yonatani adamumvera, nachita monga momwe mnzakeyo adaanenera. Adauza asilikali ake kuti abwerere kwao ku Yudeya.

47Adangosungako asilikali 3,000. Mwa ameneŵa adasiyako 2,000 ku Galileya, ndipo 1,000 okha adamperekeza.

48Koma Yonatani atangoloŵa mu mzinda wa Ptolemaisi, anthu akumeneko adatseka zipata za mzindawo, namgwira iyeyo. Adapha ndi lupanga onse amene adaaloŵa naye.

49Nthaŵi yomweyo Trifone adatumiza gulu lankhondo ndi okwera pa akavalo ku Galileya, kuti akaononge anthu onse othandizana ndi Yonatani.

50Koma iwowo atamva kuti Yonatani amugwira, adaganiza kuti wafa pamodzi ndi anzake okhala naye. Choncho adalimbitsana mtima, nayenda pa mizere yankhondo, atakonzekera nkhondo.

51Adani oŵalondola aja atazindikira kuti akulimbikira kuteteza moyo wao, adabwerera.

52Pamenepo Ayudawo adabwerera mwamtendere ku dziko la Yudeya. Adalira maliro a Yonatani ndi anzake, ndipo adagwidwa ndi mantha. Aisraele adalira maliro kwambiri.

53Anthu onse a mitundu ina oŵazungulira adayesa kuŵaononga, nati, “Tsopano alibe mfumu kapena woŵathandiza. Tiyeni tikamenyane nawo nkhondo ndi kufafaniziratu mbiri yao pakati pa anthu.”

Ayuda apatsa Simoni ulamuliro
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help