1Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaaŵagwira nkupita nawo ku ukapolo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
2Adabwera pamodzi ndi atsogoleri aŵa: Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana.
Nachi chiŵerengero cha anthu aamuna a Aisraele:
3A banja la Parosi, 2,172.
4A banja la Sefatiya, 372.
5A banja la Ara, 775.
6A banja la Pahatimowabu, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa ndi Yowabu, 2,812.
7A banja la Elamu, 1,254.
8A banja la Zatu, 945.
9A banja la Zakai, 760.
10A banja la Bani, 642.
11A banja la Bebai, 623.
12A banja la Azigadi, 1,222.
13A banja la Adonikamu, 666.
14A banja la Bigivai, 2,056.
15A banja la Adini, 454.
16A banja la Atere, ndiye kuti la Hezekiya, 98.
17A banja la Bezai, 323.
18A banja la Yora, 112.
19A banja la Hasumu, 223.
20A banja la Gibara, 95.
21Amuna a ku Betelehemu, 123.
22Amuna a ku Netofa, 56.
23Amuna a ku Anatoti, 128.
24A banja la Azimaveti, 42.
25A banja la Kiriyati-Arimu, Kefira ndi Beeroti, 743.
26A banja la Rama ndi Geba, 621.
27Amuna a ku Mikimasi, 122.
28Amuna a ku Betele ndi ku Ai, 223.
29A banja la Nebo, 42.
30A banja la Magabisi, 156.
31A banja la Elamu wina, 1,254.
32A banja la Harimu, 320.
33A banja la Lodi, Hadidi ndi Ono, 725.
34A banja la Yeriko, 345.
35A banja la Sena, 3,630.
36Ansembe anali aŵa: a banja la Yedaya, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa, 973.
37A banja la Imeri, 1,052.
38A banja la Pasuri, 1,247.
39A banja la Harimu, 1,017.
40Alevi anali aŵa: a banja la Yesuwa ndi la Kadimiyele, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya, 74.
41Oimba nyimbo anali aŵa: a banja la Asafu, 128.
42Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Salumu, a banja la Atere, a banja la Talimoni, a banja la Akibu, a banja la Hatita, ndi a banja la Sobai, onse pamodzi 139.
43Antchito a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Ziha, a banja la Hasufa, a banja la Tabaoti,
44a banja la Kerosi, a banja la Siyaha, a banja la Padoni,
45a banja la Lebana, a banja la Hagaba, a banja la Akubu,
46a banja la Hagabu, a banja la Salimai, a banja la Hanani,
47a banja la Gidele, a banja la Gahara, a banja la Reaya,
48a banja la Rezini, a banja la Nekoda, a banja la Gazamu,
49a banja la Uza, a banja la Paseya, a banja la Bosai,
50a banja la Asina, a banja la Meunimu, a banja la Nefisimu,
51a banja la Bakibuki, a banja la Hakufa, a banja la Harihuri,
52a banja la Baziluti, a banja la Mehida, a banja la Harisa,
53a banja la Barikosi, a banja la Sisera, a banja la Tema,
54a banja la Neziya ndi a banja la Hatifa.
55Mabanja a antchito ake a Solomoni anali aŵa: a banja la Sotai, a banja la Hasopereti, a banja la Peruda,
56a banja la Yaala, a banja la Darikoni, a banja la Gidele,
57a banja la Sefatiya, a banja la Hatili, a banja la Pokereti-Hazebaimu ndi a banja la Ami.
58Antchito onse a ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo zidzukulu za antchito a Solomoni, onse analipo 392 pamodzi.
59Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai.
60A banja la Delaya, a banja la Tobiya ndi a banja la Nekoda, 642.
61Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Habaya, a banja la Hakozi ndi a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo).
62Iwoŵa adafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe, naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo.
63Num. 27.21Bwanamkubwa adaŵauza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya choperekedwa kwa Mulungu, mpaka wansembe wodziŵa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu atapezeka.
64Chiŵerengero cha anthu onse obwerako ku ukapolo aja chinali 42,360.
65Kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito ao aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Anali nawonso anthu oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, okwanira 200.
66Akavalo ao analipo 736, nyulu zao zinalipo 245,
67ngamira zao zinalipo 435 ndipo abulu ao analipo 6,720.
68Pamene adabwera ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zaufulu, kuperekera Nyumba ya Mulungu, kuti imangidwenso pamalo pake pakale.
69Adapereka kwa msungachuma wa ntchitoyo molingana ndi chuma chao, golide wa makilogaramu 500, ndi siliva wa makilogaramu 2,800, ndiponso zovala za ansembe zokwanira 100.
70 1Mbi. 9.2; Neh. 11.3 Ansembe, Alevi ndi anthu ena ankakhala mu mzinda wa Yerusalemu ndi m'midzi yake yozungulira. Anthu oimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso Aisraele ena onse, ankakhala m'midzi ya makolo ao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.