1Komatu abale, za nthaŵi ndi nyengo yake yodzachitika zimenezi, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani.
2Mt. 24.43; Lk. 12.39; 2Pet. 3.10Inu nomwe mukudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye likadzafika ngati mbala yausiku.
3Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba.
4Koma inu abale, simuli m'chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala.
5Paja nonsenu zanu zonse ndi zam'kuŵala, ndiye kuti zausana. Ife zathu si zausiku kapena zamumdima ai.
6Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera.
7Anthu ogona tulo, amagona usiku, anthu oledzera amaledzera usiku.
8Yes. 59.17; Aef. 6.13-17Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
9Paja Mulungu sadatisankhe kuti tidzaone mkwiyo wake, koma kuti tidzalandire chipulumutso kwa Ambuye athu Yesu Khristu.
10Iwo adatifera kuti tikakhale ndi moyo pamodzi naye, ngakhale pamene tili amoyo kapena titafa kale.
11Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Mau otsiriza12Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani.
13Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
14Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.
15Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse.
16Khalani okondwa nthaŵi zonse.
17Muzipemphera kosalekeza.
18Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
19Musayese kuletsa ntchito ya Mzimu Woyera.
20Musanyoze mau olalikidwa m'dzina la Mulungu,
21koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,
22ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse.
23Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
24Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi.
25Abale, muzitipempherera.
26Abale onse muŵapatseko moni mwachikondi.
27M'dzina la Ambuye ndikukulamulani kuti kalatayi muŵaŵerengere abale onse.
28Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.