Aro. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kumvera olamulira

1 Lun. 6.3 Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.

2Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.

3Olamulira sachititsa mantha anthu a makhalidwe abwino, koma a makhalidwe oipa. Kodi ufuna kukhala wosaopa wolamulira? Uzichita zolungama, ndipo iye adzakuyamikira,

4pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.

5Nchifukwa chake muziŵamvera olamulira, osati chifukwa cha kuwopa mkwiyo wa Mulungu chabe, komanso chifukwa chomvera umboni wa mtima.

6 Mt. 22.21; Mk. 12.17; Lk. 20.25 Ndichonso mumakhomera msonkho: olamulira amatumikira Mulungu pamene akugwira ntchito yaoyi.

7Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.

Za kukondana

8Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

9Eks. 20.14; Deut. 5.18; Eks. 20.13; Deut. 5.17; Eks. 20.15; Deut. 5.19; Eks. 20.17; Deut. 5.21; Lev. 19.18 Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

10Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Tsiku la Ambuye layandikira

11Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira.

12Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera.

13Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje.

14Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help