1Isiboseti, mwana wa Saulo, atamva kuti Abinere adakafera ku Hebroni, adataya mtima, ndipo Aisraele onse adachita mantha kwambiri.
2Isibosetiyo anali ndi anthu aŵiri amene anali atsogoleri a magulu ankhondo. Wina anali Baana, wina anali Rekabu, onsewo ana a Rimoni, wa fuko la Benjamini, wa ku Beeroti (pakuti Beeroti ndi chigawo cha Benjamini.
3Abeeroti adathaŵira ku Gitaimu, ndipo akhala akukhala nao kumeneko mpaka pano).
4 2Sam. 9.3 Yonatani, mwana wa Saulo, anali ndi mwana wake wolumala miyendo, dzina lake Mefiboseti. Ndiye kuti mwanayo ali wa zaka zisanu, mbiri ya imfa ya Saulo ndi Yonatani idamveka ku Yezireele. Tsono mlezi wake wa mwanayo atamva, adamtenga mwana uja, nkuyamba kuthaŵa. Ndiye pothaŵa mofulumira choncho, mwanayo adampulumuka, nagwa pansi, nkuvulala. Kulumala kunali komweko.
5Tsono Rekabu ndi Baana, ana aja a Rimoni Mbeerotiŵa, adanyamuka. Masana dzuŵa likuswa mtengo, adakafika ku nyumba ya Isiboseti, nthaŵi imene iyeyo anali pa mpumulo wamasana.
6Mkazi wolonda pa khomo la nyumbayo ankapuntha tirigu, kenaka nkuyamba kuwodzera, nagona. Choncho Rekabu ndi Baana mbale wake adangoti kwakwalala kuloŵa.
7Aŵiriwo ataloŵa m'nyumbamo, adampeza Isibosetiyo ali gone pabedi pake. Iwo aja adambaya nkumupha, namdula mutu. Adanyamula mutuwo, nayenda nawo usiku wonse kudzera njira ya ku Araba.
8Tsono mutu wa Isibosetiwo adapita nawo kwa Davide ku Hebroni. Adauza mfumuyo kuti, “Amfumu, suwu mutu wa Isiboseti, mwana wa Saulo, mdani wanu uja ankafunafuna kukuphaniyu. Lero lino Chauta walipsirira Saulo ndi zidzukulu zake chifukwa cha inu mbuyanga.”
9Koma Davide adayankha Rekabu ndi Baana mbale wake kuti, “Ndithu pali Chauta wamoyo, amene waombola moyo wanga kwa adani anga onse,
102Sam. 1.1-16 pamene wina adaandiwuza kuti Saulo wamwalira, naganiza kuti wabwera ndi uthenga wabwino, ine ndidamgwira, ndipo ndidamupha ku Zikilagi. Imeneyo idaali mphotho yomwe adalandira chifukwa cha uthenga wakewo.
11Nanga nanji anthu oipa amene adapha munthu wopanda chifukwa ali gone m'nyumba mwake, kodi ndingapande kukulangani chifukwa cha imfa ya munthuyo, mpaka kukuchotsani pa dziko lapansi?”
12Motero Davide adalamula ankhondo ake, ndipo adaŵapha anthuwo, naŵadula manja ndi mapazi, naŵapachika pambali pa dziŵe la ku Hebroni. Koma adatenga mutu wa Isiboseti, nakauika m'manda a Abinere ku Hebroni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.