1Anthu akunena kuti,
“Tiyeni, tibwerere kwa Chauta.
Watikadzula, komabe adzatichiritsa.
Watikantha, komabe adzamanga mabala athu.
2Posachedwa adzatitsitsimutsa.
Patangopita masiku aŵiri kapena atatu,
adzatiwukitsa kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3Tiyeni tilimbikire kusamala za Chauta.
Adzabwera kwa ife mosapeneka konse ngati mbandakucha.
Kubwera kwake kudzakhala madalitso ngati mvula,
mvula yake yachilimwe
imene imakhathamiza nthaka.”
4Koma Chauta akuti,
“Inu Aefuremu, kodi ndikuchiteni chiyani?
Nanga inu Ayuda, ndikuchiteni chiyani?
Chikondi chanu chimazimirira
ngati nkhungu yam'maŵa,
chili ngati mame okamuka msanga.
5Nchifukwa chake ndakuŵazani ngati nkhuni
ndi machenjezo a aneneri,
ndakuphani ndi mau anga.
Chigamulo changa nchoonekeratu ngati kuŵala kwa dzuŵa.
6 Mt. 9.13; 12.7 Kunena zoona Ine ndimafuna chikondi chosasinthika,
osati nsembe chabe.
Ndifuna kuti anthu andidziŵe Ine Mulungu
m'malo mwa kumangopereka nsembe zopsereza.
7“Koma anthuwo adaphwanya chipangano changa
monga adachitira Adamu.
Potero, adandichitira zosakhulupirika.
8Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoipa,
akungophana basi.
9Monga mbala zimalalira munthu,
momwemonso ansembe amasonkhana
kuti azipha anthu pa njira ya ku Sekemu.
Zoonadi amachita zachifwamba zambiri.
10Pakati pa Aisraele ndaonapo zinthu zonyansa.
Aefuremu adachita zadama,
Aisraele adadziipitsa pakupembedza mafano.
11“Inunso Ayuda mudzakolola chilango.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.