1Inu Chauta, mudakomera mtima dziko lanu,
mudaƔakhazikanso pabwino a m'banja la Yakobe.
2Mudakhululukira machimo a anthu anu,
mudafafaniza zolakwa zao zonse.
3Mudaleka ndithu ukali wanu woopsa,
mudaletsa mkwiyo wanu woyaka moto.
4Mutibwezerenso mwakale, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.
5Kodi mudzakhalabe mukutikwiyira mpaka muyaya?
Kodi mudzapitiriza kukwiya mpaka pa mibadwo yathu yonse?
6Kodi simudzatipatsanso moyo,
kuti ife anthu anu tikondwere mwa Inu?
7Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta,
ndipo mutipulumutse.
8Ndimve zimene Chauta adzalankhula,
chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake,
kwa anthu ake oyera mtima,
ngati sabwereranso ku zopusa zao.
9Zoonadi, Mulungu ali wokonzekera
kuti apulumutse amene amamuwopa,
kuti ulemerero wake ukhale m'dziko lathu.
10Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana.
Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana.
11Anthu ake adzakhala okhulupirika pansi pano,
ndipo Mulungu wakumwamba adzaƔalungamitsa.
12Inde, Chauta adzapereka zabwino,
ndipo dziko lathu lidzabereka zokolola zambiri.
13Mulungu ndi wolungama chikhalire,
chilungamo chake chimaongolera zochita zake zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.