1Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga,
ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya.
2Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku,
ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya.
3Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri,
ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
4Mibadwo ndi mibadwo idzatamanda ntchito zanu,
idzalalika ntchito zanu zamphamvu.
5Ndidzasinkhasinkha za ulemerero
ndi za ufumu wanu waukulu,
ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
6Anthu adzasimba za mphamvu zanu zoopsa,
inenso ndidzalalika za ukulu wanu.
7Adzasimba za ubwino wanu,
adzaimba nyimbo zotamanda kulungama kwanu.
8Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika.
9Chauta ndi wabwino kwa onse,
amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.
10Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta,
anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani.
11Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu,
adzasimba za mphamvu zanu,
12kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu,
kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
13Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,
ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse.
Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse,
ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse.
14Chauta amachirikiza onse ogwa m'mavuto,
amakweza onse otsitsidwa.
15Maso onse amayang'anira kwa Inu,
ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake.
16Mumafumbatula dzanja lanu,
ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.
17Chauta ndi wolungama m'zochita zake zonse,
ndi wachifundo pa zonse zimene achita.
18Chauta ali pafupi ndi onse
amene amamutama mopemba.
Ali pafupi ndi onse
amene amamutama mokhulupirika.
19Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao,
amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
20Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga,
koma Chauta adzaononga oipa onse.
21Pakamwa panga padzayamika Chauta,
zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.