1Tsono Chauta adauza Mose kuti,
2“Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, uutse chihema chamsonkhano.
3Bokosi m'mene muli miyala yaumboni uliike m'menemo, ndipo bokosilo uliphimbe ndi nsalu kuti ulichinge.
4Ukhazikemonso tebulo, pamwamba pake uikepo zipangizo zake, ndipo uikemo choikaponyale ndi nyale zake.
5Tsono uike guwa lagolide lofukizirapo lubani patsogolo pa bokosi laumboni. Pa chipata cha Nyumba ya Mulungu utsekepo ndi nsalu zochinga.
6Uike guwa lootcherapo nsembe patsogolo pa chihema chamsonkhanocho.
7Beseni uliike pakati pa chihema chamsonkhano ndi guwa, ndipo uthiremo madzi.
8Upange bwalo kuzungulira chihemacho, ndi kukoloŵeka nsalu zochingira pa chipata chake cha bwalolo.
9“Pambuyo pake utenge mafuta odzozera aja, udzoze Nyumba ya Mulungu ndi zonse za m'menemo. Uipereke kwa Mulungu Nyumbayo, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, kuti idzakhale yoyera.
10Tsono udzozenso guwa loperekapo nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zomwe. Guwalo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera ndipo lidzakhaladi loyera kopambana.
11Udzoze beseni losambira, pamodzi ndi phaka lake lomwe, ndipo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera.
12“Pambuyo pake ubwere ndi Aroni ku chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake omwe, ndipo onsewo asambe kumeneko.
13Aroniyo umuveke zovala zopatulika. Umdzoze, ndipo umpatule kuti akhale wansembe wonditumikira Ine.
14Ana ake abwerenso, ndipo uŵaveke miinjiro.
15Tsono uŵadzoze monga momwe udadzozera bambo wao, kuti akhale ansembe onditumikira Ine. Kudzozedwako kudzaŵasandutsa ansembe pa mibabwo ndi mibadwo.”
16Mose adachita zonse, monga momwe Chauta adamlamulira.
17Motero pa tsiku loyamba la mwezi woyamba chaka chachiŵiri, malo opatulika adautsidwa.
18Poutsa malowo, Mose adakhazika masinde ake pansi, ndipo adautsa mafulemu ake, nalumikiza mitanda yake, nautsanso nsanamira zake zija.
19Pambuyo pake adautsa chihema pamwamba pa malo opatulikawo, nachiphimba ndi chophimbira chake cha chihema, monga momwe Chauta adamlamulira.
20Tsono adatenga miyala yaumboni ija naiika m'bokosi muja. Adapisa mphiko zija m'mphete za bokosilo, naika chivundikiro pamwamba pake.
21Kenaka adaika bokosilo m'malo opatulika, ndipo adaika nsalu zochingira. Motero adachinga bokosi laumboni, monga momwe Chauta adamlamulira.
22Tsono m'chihema chamsonkhanomo adaikamo tebulo, chakumpoto kwa malo opatulika, kunja kwa nsalu yochinga ija,
23ndipo pamwamba pa tebulolo adaikapo buledi, monga momwe Chauta adamlamulira.
24M'chihema chamsonkanomo adaikamo choikaponyale mopenyana ndi tebulo chakumwera kwake kwa malo opatulika.
25Tsono pa choikaponyalecho adaikapo nyale, kuti zikhale pamaso pa Chauta, monga momwe Iye adalamulira Mose.
26M'chihema chamsonkhanomo adaikamo guwa lagolide patsogolo pa nsalu yochinga.
27Adafukiza lubani wa fungo lokoma paguwapo, monga momwe Chauta adamlamulira.
28Pa khomo la malo opatulika adaikapo nsalu yochinga.
29Ndipo adaika guwa la nsembe zopsereza pa khomo la chihema chamsonkhano. Pa guwa limenelo adaperekapo nsembe zopsereza ndiponso chopereka cha chakudya, monga momwe Chauta adamlamulira.
30Kenaka adaika beseni losambira lija pakati pa chihema chamsonkano ndi guwa, nathiramo madzi osamba.
31Apo Mose, Aroni ndi ana ake adasamba m'manja natsuka mapazi ao.
32Nthaŵi zonse akaloŵa m'chihema chamsonkhanomo, kapena kusendera ku guwalo, ankasamba, monga momwe Chauta adalamulira Mose.
33Adamanga bwalo lonse lozungulira chihema chija ndi guwa. Adaikanso nsalu yochinga pa chipata cha bwalolo. Motero Mose adamaliza ntchito yonseyo.
34 1Maf. 8.10, 11; Yes. 6.4; Ezek. 43.4, 5; Chiv. 15.8 Mtambo udaphimba chihema chamsonkhanocho, ndipo ulemerero wa Chauta udachidzaza
35Mose sadathe kuloŵa m'chihema chamsonkhanocho chifukwa mtambo unali momwemo, ndipo ulemerero wa Chauta udaadzaza chihema chake.
36Pa maulendo ao onse, mtambo ukachoka pachihemapo, Aisraelewo ankachoka pamene analiripo.
37Koma mtambowo ukapanda kuchoka, Aisraele sankachokanso pachigonopo. Ankadikira tsiku lakuti mtambo wachokapo.
38Unkakhala pachihemapo masana, usiku mumtambomo munkayaka moto, ndipo Aisraele onse ankatha kuupenya. Zinkatero pa ulendo wao wonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.