Mas. 118 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lothokoza chifukwa cha kupambana

1 1Mbi. 16.34; 2Mbi. 5.13; 7.3; Eza. 3.11; Mas. 100.5; 106.1; 107.1; 136.1; Yer. 33.11 Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino,

ndipo chikondi chake nchamuyaya.

2Aisraele anene kuti,

“Chikondi chake nchamuyaya.”

3Banja la Aroni linene kuti,

“Chikondi chake nchamuyaya.”

4Anthu oopa Chauta anene kuti,

“Chikondi chake nchamuyaya.”

5Pamene ndinali m'mavuto ndidapemphera kwa Chauta,

ndipo Iye adandichotsera mavutowo.

6 Ahe. 13.6 Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha.

Munthu angandichite chiyani?

7Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize.

Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.

8Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino

kupambana kukhulupirira munthu.

9Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino

kupambana kukhulupirira mafumu.

10Adani a mitundu yonse adandizinga,

koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta.

11Adandizinga, inde adandizinga pa mbali zonse,

koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta.

12Adandizinga ngati njuchi,

koma adatha msanga ngati moto wapaminga.

Ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta.

13Adandikankha kwambiri,

kotero kuti ndinali pafupi kugwa,

koma Chauta adandithandiza.

14 Eks. 15.2; Yes. 12.2 Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga.

Ndiye mpulumutsi wanga.

15Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu,

nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti,

“Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu,

16dzanja lamanja la Chauta lapambana,

dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”

17Sindidzafa, ndidzakhala moyo,

ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta.

18Chauta wandilanga koopsa,

koma sadandisiye kuti ndife.

19Tsekulireni zipata za Nyumba ya Mulungu,

kuti ndifike ku malo ake achilungamo,

ndikathokoze Chauta.

20Ichi ndicho chipata cha Chauta,

anthu okhawo ochita chifuniro chake adzaloŵera pamenepa.

21Ndikukuyamikani popeza kuti mwandiyankha,

ndipo mwasanduka Mpulumutsi wanga.

22 Lk. 20.17; Ntc. 4.11; 1Pet. 2.7 Mt. 21.42; Mk. 12.10, 11 Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana,

womwewo wasanduka mwala wapangodya.

23Chauta ndiye amene wachita zimenezi,

zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.

24Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga.

Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

25 Mt. 21.9; Mk. 11.9; Yoh. 12.13 Tipulumutseni, tikukupemphani Inu Chauta.

Chauta, tikukupemphani kuti zinthu zitiyendere bwino.

26 Mt. 21.9; 23.39; Mk. 11.9; Lk. 13.35; 19.38; Yoh. 12.13 Ngwodala amene alikudza m'dzina la Chauta.

Tikufunirani madalitso ochokera m'nyumba ya Chauta.

27Chauta ndi Mulungu,

ndipo watipatsa kuŵala.

Yambani mdipiti wachikondwerero mutatenga nthambi,

mpaka kukafika ku guwa lansembe.

28Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakuthokozani.

Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakutamandani.

29Thokozani Chauta pakuti ngwabwino,

ndipo chikondi chake chosasinthika nchamuyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help