1Pa nthaŵi imeneyo Yuditi adamva zimene zinkachitika. Iyeyo anali mwana wa Merari, mwana wa Okisi, mwana wa Yosefe, mwana wa Oziele, mwana wa Elekiya, mwana wa Ananiya, mwana wa Gideoni, mwana wa Rafaimu, mwana wa Ahitubi, mwana wa Eliya, mwana wa Hilikiya, mwana wa Eliyabu, mwana wa Natanaele, mwana wa Salamiele, mwana wa Sarasadai, mwana wa Israele.
2Mwamuna wake Manase, amene anali wa fuko lake ndi wa m'banja lake la Yuditi, anali atamwalira pa nthaŵi yodula barele.
3Pamene anali ku minda kukayang'anira omanga mitolo, dzuŵa lamphamvu lidamchititsa chizungulire. Adakagona pabedi pake mu mzinda wa Betuliya, kufa kunali komweko. Tsono adamuika m'manda pafupi ndi makolo ake m'munda wa pakati pa Dotani ndi Balamoni.
4Yuditi adakhala kwao zaka zitatu ndi miyezi inai ali wamasiye.
5Owe. 3.20; 2Maf. 4.10Adadzikonzera chipinda chakechake pamwamba pa nyumba yake. Ankamanga chiguduli m'chiwuno, namavala zaumasiye.
6Chiyambire cha umasiye wakewo ankasala zakudya masiku onse, kupatula tsiku loyembekeza Sabata ndi la Sabata limene, tsiku loyembekeza kukhala kwa mwezi, ndi lokhala mwezi limene, ndiponso masiku aakulu ndi achikondwerero a fuko la Aisraele.
7Anali mkazi wokongola kwambiri ndi wochititsa kaso. Mwamuna wake Manase adaamusiyira golide, siliva, akapolo aamuna ndi aakazi, ziŵeto ndi minda, ndipo ankayang'anira bwino chuma chake.
8Panalibe ndi mmodzi yemwe amene ankakamba zoipa za iye, poti anali mkazi wokonda kupembedza ndi woopa Mulungu.
Yuditi akumana ndi akuluakulu amumzinda9Yuditi adamva mau oipa amene anthu adaamunena Uziya, iwowo atafooka chifukwa chosoŵa madzi. Adamvanso zimene Uziya adaanena, ndipo kuti adaalumbira kuti adzaupereka mzindawo kwa Aasiriya, patapita masiku asanu.
10Adatumiza mdzakazi wake amene ankayang'anira chuma chake, kuti akaitane Uziya, Kabrisi ndi Karmisi, akuluakulu a mumzindamo.
11Akuluakuluwo atafika, Yuditi adaŵauza kuti, “Pepani, mundimvere, inu atsogoleri a anthu a m'Betuliya muno. Ndithu mwalakwa pouza anthu zija mwanena lerozi. Inu ndithu nkumalumbira pamaso pa Mulungu kuti mudzapereka mzindawu kwa adani athu, ngati Ambuye satithandiza pa masiku angapo!
12Deut. 6.16; Yob. 38.2Inu ndinu yani kuti muziyesa Mulungu chotere ndi kudzikweza pamalo pa Mulungu pakati pa anthu?
13Kuteroku nkuŵapenekera Ambuye Amphamvuzonse. Kodi mudzadziŵa liti zinthu?
14Aro. 11.33, 34; 1Ako. 2.11Simungathe kudziŵa za mumtima mwa munthu ndi zimene akuganiza. Nanji Mulungu amene adalenga anthu, kodi inu mungaŵadziŵe ndi kuŵamvetsa maganizo ake? Pepani, abale anga, musamautse mkwiyo wa Ambuye, Mulungu wathu.
15Ngati Iye safuna kutipulumutsa pasanapite masiku asanu, angathebe kutipulumutsa nthaŵi iliyonse imene akufuna, kapenanso kulola kuti adani athu atiwononge.
16Simungathe kuŵaika pa mpani Ambuye, Mulungu wathu. Mulungu sali ngati munthu, kuti inu nkumuwopseza, kapena kumkopa ndi mau ochonderera.
17Iyai, koma ife tizingoyembekeza kuti atipulumutse. Tsono tizipemphera kuti atithandize, ndipo zikamkomera adzatimvera.
18“Pa mbadwo wathu uno, ngakhale pa masiku ano, pakati pathu palibe fuko, kapena banja, kapena mzinda, m'mene anthu ake amapembedza milungu yopangidwa ndi anthu, monga momwe ankachitira makolo athu kale.
19Nchifukwa chake makolo athuwo adaperekedwa kwa adani ao kuti aphedwe ndi kufunkhidwa, ndipo adaonongedwadi koopsa.
20Ife sitidziŵa mulungu wina koma Ambuye. Motero tikukhulupirira kuti sadzatisiya, sadzasiya wina aliyense pa mtundu wathu.
21Ngati adani agwira mzinda wathu, adzagwiranso dziko lonse ndipo Nyumba yathu yopembedzeramo adzaifunkha. Tsono Nyumbayo ikadzaipitsidwa, Mulungu adzatilanga.
22Adzatizenga mlandu chifukwa cha kuphedwa ndi kutengedwa ukapolo kwa anthu a m'dziko lathu, chifukwanso cha kuwonongedwa kwa dziko lathu. Zimenezi zidzatinyazitsa kulikonse kumene tidzakhale akapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Odzatigulawo adzatinyoza ndi kutiseka kumeneko.
23Ngakhale tikaŵagonjera tsopano, adani athu sadzatichitira chifundo, ndipo tikadzatero, Mulungu wathu adzatinyazitsa pamaso pa anthu onse.
24“Choncho inu abale anga, tiyeni tipereke chitsanzo chabwino kwa anzathu, poti moyo wao ukugonera pa ife. Nyumba yopembedzeramo Mulungu ndiponso guwa lansembe, zonse zikudalira ifeyo.
25Ambuye Mulungu wathu akutiyesa monga momwe adaayesera makolo athu, tiŵathokoze ndithu, ngakhale pakati pa mavuto pano.
26Gen. 22.1-18; 29.1—31.55Kumbukirani m'mene adachitira ndi Abrahamu, m'mene adayesera Isaki, ndi zimene zidachitikira Yakobe ku Mesopotamiya ku Siriya, pamene ankagwira ntchito yoŵeta nkhosa kwa malume wake Labani.
27Mulungu sakuyesa chikhulupiriro chathu ndi moto monga m'mene adaachitira ndi iwowo, ndipo sakutilipsira ife, koma chilango chakechi nchotichenjeza ifeyo amene tikumtumikira.”
28Pamenepo Uziya adayankha kuti, “Mai, ukunena zoona, ndipo palibe amene angatsutsepo.
29Ino si nthaŵi yoyamba imene watiwonetsa luntha lako. Pa moyo wako wonse watiwonetsa kuti ndiwe munthu wa nzeru zabwino ndi woweruza molungama.
30Koma anthu adaataya mtima chifukwa chomva ludzu. Tsono adaatikakamiza kuti tilonjeze ndi kulumbira zimene sitingaziphwanye tsopano.
31Komabe poti ndiwedi mkazi wokonda kupemphera, utipempherere kwa Ambuye kuti atumize mvula idzadzaze zitsime zathu, kuti tisalefukenso ndi ludzu.”
32Yuditi adayankha kuti, “Mumve zimene nditi ndilankhule. Lero ndichita chinthu chimene mtundu wathu sudzaiŵala mpaka pa mibadwo yonse.
33Mukhale pa chipata usiku, kuti ine ndituluke ndi mdzakazi wanga. Lisanafike tsiku limene mudalonjeza kuti mudzapereka mzinda kwa adani athu, Ambuye adzapulumutsa Aisraele kudzera mwa ine.
34Koma musayese kuloteza zimene ndifuna kuti ndichite. Sindikuuzani mpaka nditatha kuchita zimene ndakonzekera.”
35Uziya ndi akuluakulu aja adauza Yuditi kuti, “Ai, pita ndi mtendere, Ambuye Mulungu akutsogolere, kuti ulipsire adani athu.”
36Atatero iwowo adachoka kunyumba kwa Yuditi kuja, nabwerera kumalo kwao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.