1Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
2Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai.
3Ndikufuna kubwerezanso kuuza aliyense woumbalidwa, kuti ayenera kutsata Malamulo onse a Mose.
4Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu.
5Koma kunena za ife, chifukwa cha kulandira Mzimu Woyera ndiponso pakukhulupirira, tikuyembekeza kuti Mulungu adzatiwona kuti ndife olungama pamaso pake.
6Pakuti pamene tili mwa Khristu Yesu, kuumbalidwa kapena kusaumbalidwa kulibe kanthu, chachikulu nchakuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.
7Munkathamanga bwino lomwe. Tsono adakuletsani ndani kuti musamverenso choona?
8Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Mulungu amene amakuitanani.
91Ako. 5.6Chofufumitsira chapang'ono chabe chimafufumitsa buledi yense.
10Ndili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye, kuti simudzakhala ndi maganizo osiyana ndi anga. Koma amene akukusokonezaniyo, ngakhale akhale yani, Mulungu adzamlanga ndithu.
11Koma kunena za ine, abale, ngati ndikulalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, nanga bwanji ndikuzunzidwabe? Ndikadalalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, sibwenzi ndikuŵakhumudwitsa pakulalika mtanda wa Khristu.
12Ndikadakonda kuti amene akukuvutaniwo angodzithena basi.
13Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
14Lev. 19.18 Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
15Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.
Za ntchito za khalidwe lokonda zoipa, ndi za zipatso za Mzimu Woyera16Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
17Aro. 7.15-23Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.
18Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose.
19Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa,
20kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
21dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
22Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
23kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
24Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
25Ngati Mzimu Woyera adatipatsa moyo, tilolenso kuti Mzimu yemweyo azititsogolera.
26Tisakhale odzitukumula, oputana, kapena ochitirana dumbo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.