1Davide adaganiza mumtima mwake kuti, “Tsiku lina Saulo adzandipha. Palibe china chimene ndingachitepo, koma kuthaŵira ku dziko la Afilisti. Choncho Saulo adzaleka kumandifunafuna m'dziko la Aisraele, ndipo ndidzapulumuka kwa iye.”
2Tsono Davide adanyamuka, ndipo pamodzi ndi ankhondo 600 amene anali naye, adapita kwa Akisi, mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.
3Adakhala ndi Akisi ku Gati, iyeyo pamodzi ndi anthu ake, aliyense ndi banja lake. Davide anali ndi akazi ake aŵiri, Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wamasiye wa Nabala.
4Saulo atamva kuti Davide wathaŵira ku Gati, sadamfunefunenso.
5Pambuyo pake Davide adauza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, mundipatse malo pa mudzi wina m'dziko mwanu kuti ndizikhala kumeneko. Kodi ine mtumiki wanu ndizikhaliranji pamodzi ndi inu mu mzinda wanu waufumu?”
6Choncho tsiku limenelo Akisi adapatsa Davide mudzi wa Zikilagi. Nchifukwa chake mudzi wa Zikilagi ngwa mafumu a Yuda mpaka lero lino.
7Motero Davide adakhala ku dziko la Afilisti chaka chimodzi ndi miyezi inai.
8Tsono Davide ndi anthu amene anali naye ankapita kwa Agesuri, Agerizi, ndi Aamaleke nakaŵathira nkhondo onsewo. Mitundu imeneyi inali nzika za dzikolo kuyambira kale. Dziko lao linkafika ku Suri ndipo linkachita malire ndi dziko la Ejipito.
9Pa maulendo ake ankhondowo Davide ankapha anthu a m'dzikolo, osasiyapo wamoyo mwamuna kapena mkazi. Koma ankatenga nkhosa, ng'ombe, abulu, ngamila, ndi zovala, ndipo zonsezo ankabwerera nazo kwa Akisi.
10Akisi akafunsa kuti, “Kodi munakamenya nkhondo ndi yani lero?” Davide ankati, “Tinakamenya nkhondo kumwera kwa Yuda,” mwina ankati, “Ku dziko la Ayeramiyele,” mwina ankati, “Ku dziko la Akeni.”
11Davide sankasiya wamoyo, mwamuna kapena mkazi, kuwopa kuti wopulumukayo angakanene ku Gati kuti, “Davide adatichita zakutizakuti.” Davide ankachita choncho nthaŵi zonse pamene ankakhala ku dziko la Afilisti.
12Ndipo Akisi adamkhulupirira Davide namaganiza kuti, “Davide wadzisandutsa munthu woipa wodedwa ndi anthu ake omwe Aisraele. Nchifukwa chake adzakhala mtumiki wanga pa moyo wake wonse.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.