Eks. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Guwa la nsembe zopsereza(Eks. 38.1-7)

1“Upange guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Likhale lalibanda: muutali mwake likhale masentimita 229, muufupi mwake chimodzimodzi: masentimita 229, msinkhu wake masentimita 137.

2Upange nyanga pa ngodya zake zinaizo, zilumikizane ndi guwalo, ndipo ulikute ndi mkuŵa.

3Upangenso mbale zake zolandirira phulusa, mafosholo, mabeseni, mafoloko aakulu ndiponso ziŵiya zosonkhapo moto. Zipangizo zonse za ku guwalo zikhale zamkuŵa.

4Upangenso chitsulo chamkuŵa choboolaboola ngati sefa. Pa ngodya zake za chitsulocho upange mphete zamkuŵa zonyamulira.

5Uike sefayo m'munsi mwake mwa chibumi cha guwalo, ndipo ilekeze pakati pa guwalo.

6Upange mphiko ya mtengo wa kasiya yonyamulira guwalo, ndipo uikute ndi mkuŵa.

7Ponyamula guwalo, mphikozo azizipisa m'mphete za pa mbali ziŵiri za guwalo.

8Ndipo guwalo udzalipange mogoba m'kati mwake. Ulipange monga momwe ndikukulangizira paphiri pano.

Za chinsalu chochinga bwalo(Eks. 38.9-20)

9“Pambuyo pake upange bwalo la chihema, lochingidwa. Chakumwera kwake kukhale nsalu zochinga za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, kutalika kwa mbali imodzi kukhale mamita 46.

10Nsanamira zake 20 ndi masinde ake 20 zikhale zamkuŵa, koma ngoŵe za nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zikhale zasiliva.

11Momwemonso pa mbali yakumpoto, uike nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 46, ndi nsanamira zamkuŵa makumi aŵiri. Nsanamirazo zimangidwe pa masinde ake makumi aŵiri, koma ngoŵe za nsanamirazo ndi mitanda yake zikhale zasiliva.

12Muufupi mwake mwa bwalolo cha mbali yakuzambwe, pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira khumi ndi masinde khumi.

13Chakuvuma, komwe kuli chipata chake, bwalolo likhalenso mamita 23 muufupi mwake.

14Pa mbali ina ya chipata pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu.

15Chimodzimodzi pa mbali ina pakhalenso nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu.

16Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Kutalika kwake kukhale mamita asanu ndi anai. Ikhale ndi nsanamira zinai zomangidwa pa masinde anai.

17Nsanamira zonse kuzungulira bwalolo zilumikizidwe ndi mitanda yasiliva, ndipo ngoŵe zake zikhalenso zasiliva, koma masinde ake akhale amkuŵa.

18Kutalika kwake kwa bwalolo kukhale mamita 46, muufupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu zochingazo zikhale za thonje losankhidwa bwino kwambiri ndi lopikidwa, ndipo masinde ake akhale amkuŵa.

19Zipangizo zonse zogwiritsira ntchito zosiyanasiyana m'chihemamo, pamodzi ndi zikhomo za chihemacho ndi za bwalolo, zonsezo zikhale zamkuŵa.

Masamalidwe a nyale(Lev. 24.1-4)

20“Uŵalamule Aisraele kuti akupatse mafuta aolivi opsinyidwa bwino, oyatsira nyale, kuti ziziyaka kosalekeza.

21Aroni ndi ana ake aamuna aziyatsa nyale m'chihema chamsonkhanomo amakumana ndi anthu ake, kunja kwa chochinga, patsogolo pa miyala yaumboni ija. Tsono nyalezo ziziyaka kumeneko kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Lamulo limeneli adzalisunge Aisraele ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help