Tob. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tobiyasi abwerera kwa atate ake

1Akufika pafupi ndi mzinda wa Kaserini, kuyang'anana ndi Ninive, Rafaele adauza Tobiyasi kuti,

2“Ukudziŵa m'mene tidasiyira bambo wako.

3Tithamange, titsogoleko, mkazi wako azititsata kumbuyo, kuti tikakonzeretu m'nyumba imene akaloŵemo.”

4Aŵiriwo adapitadi. Paja Rafaele adaalangiza Tobiyasi kuti atenge ndulu ija ya nsombayi. Galu wa Tobiyasi uja ankatsagana nawo.

5Hana anali atakhala pansi, kumayang'ana kunjira kumene adaayenera kutulukira mwana wake.

6Adamuwona alikudza patali, ndipo adauza bambo wake kuti, “Uyotu mwana wanu akubwera ndi munthu uja adaapita nayeyu.”

7Rafaele adauza Tobiyasi asanafike kwa tate wake kuti, “Ndikudziŵa kuti maso ake adzapenya.

8Ukadzoze maso ake ndi ndulu ya nsomba ija. Pamenepo maso akewo adzaŵaŵa pang'ono, khungu limene lili m'masolo lidzachoka. Kenaka bambo wako adzathanso kupenya, nadzaona kuŵala.”

9Hana uja adathamanga nalumphira pakhosi pa mwana wake, ndipo adati, “Ndakuwona mwana wanga, tsopano ndingathe kufa.” Ndipo adayamba kulira misozi.

10Tobiti adadzuka, natuluka pa khomo la bwalo ali dzandidzandi.

11Tobiyasi adadza kwa iye, ndulu ya nsomba ija ili m'manjamu. Adauzira m'maso mwake, nati, “Khulupirirani, atate.” Adampaka mankhwala aja,

12Ntc. 9.18ndipo ndi manja aŵiri, akuyambira pa ngodya za maso, adamatula kakhungu kaja.

13Pamenepo Tobiti adapenya mwana wake namgwira m'khosi mwake. Adayamba kulira misozi, nati,

14“Ndikutha kukuwona mwana wanga, iwe kuŵala kwa maso anga.” Tsono adati,

“Mulungu atamandike,

dzina lake lalikulu litamandikenso.

Angelo ake oyera atamandike,

dzina lake lalikulu litamandike mpaka muyaya.

15“Chifukwa Iye adaandilanga,

koma wandichitira chifundo,

motero tsopano ndikumuwona Tobiyasi,

mwana wanga.”

Tobiyasi adaloŵa m'nyumba ali wokondwa, ndipo adayamika Mulungu mokweza mau. Adakambira bambo wake za ulendo wake wonse, kuti unali ulendo wabwino, ndalama zija adakatenga, ndipo kuti komweko adakwatira mkazi. Pa nthaŵiyo nkuti Sara, mwana wa Raguele, ali pafupi kufika ku chipata cha Ninive.

16Tobiti adasangalala nayamika Mulungu, ndipo adanyamuka kupita ku chipata cha Ninive kukakumana naye mpongozi wakeyo. Anthu a ku Ninive atamuwona akuyenda ndi liŵiro ndiponso mwamphamvu, popanda wina wotsakana naye, adadabwa kwambiri.

17Tobiti adauza khamu la anthulo kuti Mulungu adamchitira chifundo ndi kumtsekula maso ake. Tsono atafika pafupi ndi Sara, mkazi wa mwana wake Tobiyasi, adamdalitsa nati, “Ndikukulandira ndi mtima wokondwa, mwana wanga. Atamandike Mulungu wako, amene wakubweretsa kwathu kuno, mwana wanga. Akhale wodala bambo wako, akhalenso wodala mwana wanga Tobiyasi pamodzi ndi iweyo, mwana wanga. Loŵa m'nyumba mwako mokondwa, ukhale ndi madalitso ndi chimwemwe, mwana wanga.” Tsikulo Ayuda onse a ku Ninive adakondwa.

18Ndipo Ahikare ndi Nadabu, ana a abale a Tobiti, iwonso adafika kudzasangalala nawo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help