1 Mt. 21.33; Mk. 12.1; Lk. 20.9 Ntamuimbirako bwenzi langa
nyimbo yokamba za wokondedwa wanga
ndi munda wake wamphesa.
Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa
pa phiri la nthaka yachonde.
2Adautipula nachotsa miyala yonse,
ndipo adaokamo mipesa yabwino kwabasi.
Adamanga nsanja pakati pa mundawo,
nasema mopondera mphesa m'kati momwemo.
Adaayembekeza kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,
koma ai, udabala mphesa zachabechabe.
3Ndiye wokondedwa wanga akuti,
“Inu amene mumakhala ku Yerusalemu,
ndi inu anthu a ku Yuda,
ndakupembani, taweruzani
pakati pa ine ndi munda wanga wamphesawu.
4Kodi chilipo chinanso
chimene ndidaayenera kuuchitira munda wanga wamphesa,
koma sindidachite?
Pamene ndinkayembekeza kuti udzabala mphesa zabwino,
bwanji udabala mphesa zachabechabe?
5“Tsopano taimani nkuuzeni
zimene ndidzauchite munda wanga wamphesawo.
Ndidzazula mpanda wake,
ndipo mundawo udzaonongeka.
Ndidzagwetsa chipupa chake,
ndipo nyama zidzapondapondamo.
6Ndidzausandutsa tsala,
udzakhala wosatengulira ndi wosalimira,
ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.
Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pamundapo.”
7Tsonotu munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonseyo
ndi dziko la Israele,
ndipo Ayuda ndiwo mipesa yake yokondweretsa.
Iye ankayembekeza ntchito zabwino,
koma adangoona kuphana.
Ankayembekeza chilungamo,
koma adangomva kulira kwa anthu ozunzidwa.
Zoipa za anthu8Tsoka kwa amene amangokhalira kulumikiza nyumba
amene amangokhalira kuwonjezera minda,
mpaka kulanda malo onse,
kuti dziko lonse likhale la iwo okha.
9Ndamva Chauta Wamphamvuzonse akulumbira kuti:
“Ndithudi, nyumba zambirizo zidzasanduka mainja,
nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
10Munda wamphesa wa mahekitara khumi,
vinyo wake adzangodzaza mbiya imodzi.
Kufesa madengu khumi a mbeu,
zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”
11 Lun. 2.7-9 Tsoka kwa amene amadzuka m'mamaŵa
nathamangira chakumwa choledzeretsa,
amene amamwa mpaka usiku
kufikira ataledzera kotheratu.
12Amangoimba zeze, pangwe, ng'oma ndi chitoliro,
nkumamwa vinyo pa maphwando ao.
Koma sasamala ntchito za Chauta,
sapenya ntchito za manja ake.
13Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo
chifukwa cha kusamvetsa zinthu.
Atsogoleri ao olemekezeka adzafa ndi njala,
ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
14Nchifukwa chake kumanda sikukhuta,
kwangoti kukamwa yasa
kuti kulandire aliyense.
Anthu otchuka a mu Yerusalemu
pamodzi ndi anthu wamba ochuluka,
adzagweramo ali wowowo,
m'kuledzera kwaoko.
15Munthu aliyense adzatsitsidwa,
onse adzachepetsedwa,
anthu odzikuza adzaŵachititsa manyazi.
16Koma Chauta Wamphamvuzonse adzalemekezedwa
chifukwa cha chilungamo chake,
Mulungu Woyera adzaonetsa kuyera kwake
pochita zaungwiro.
17Tsono anaankhosa adzadya pamenepo ngati pabusa pao,
ndipo anaambuzi adzadya m'mabwinja.
18Tsoka kwa amene amadzikokera machimo ambiri
ndi kunama kwao,
amene amalephera kudzimasula ku machimo awo.
19Amanena kuti, “Chauta afulumire,
agwire ntchito yake mwamsanga,
kuti ntchitoyo tiiwone.
Zimene Woyera uja wa Israele afuna kuchita,
zichitiketu kuti tizidziŵe.”
20Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino
ndipo zabwino amaziyesa zoipa,
amene mdima amauyesa kuŵala,
ndipo kuŵala amakuyesa mdima,
amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna,
ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa!
21Tsoka kwa amene amadziwona ngati anzeru
ndipo amadziyesa ochenjera!
22Tsoka kwa zidakwa
zimene zimaika mtima pa vinyo!
Tsoka kwa anthu amene saopa konse
kusakaniza zakumwa zaukali!
23Amalungamitsa wolakwa chifukwa cha chiphuphu
nkuipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24Nchifukwa chake monga momwe moto umaonongera chiputu,
monga momwenso udzu wouma umapsera m'malaŵi a moto,
momwemonso muzu wao udzaola,
ndipo maluŵa ao adzafota ndi kuuluka ngati fumbi,
chifukwa adakana malamulo a Chauta Wamphamvuzonse,
adanyoza mau a Woyera uja wa Israele.
25Nchifukwa chake ukali wa Chauta waŵayakira anthu ake.
Iye watambalitsa dzanja lake pa anthuwo kuti aŵakanthe.
Mapiri agwedezeka,
ndipo mitembo ya anthuwo yangoti mbwee
ngati zinyalala pakati pa miseu.
Koma ngakhale Mulungu watero,
mkwiyo wake sudaleke,
dzanja lake lidakali chitambalitsire.
26Chauta adzapereka chizindikiro
kuitana mtundu wa anthu akutali.
Adzaŵaitana anthuwo ndi khweru,
kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.
Tsono iwo adzabweradi mothamanga kwambiri.
27Palibe ndi mmodzi yemwe wodzatopa kapena kukhumudwa,
kuwodzera kapena kugona.
Palibe lamba wam'chiwuno amene adzamasuke,
palibe chingwe cha nsapato zao chimene chidzaduke.
28Mivi yao ndi yakuthwa,
mauta ao onse ngokoka,
ziboda za akavalo ao nzolimba ngati mwala,
magaleta ao ndi aliŵiro ngati kamvulumvulu.
29Kufuula kwao kuli ngati kubangula kwa mkango,
amabangula ngati misona ya mkango,
imene imadzuma pogwira nyama,
nipita nazo popanda ndi mmodzi yemwe wozipulumutsa.
30Tsiku limenelo
adzaŵakokolola monga momwe mtsinje waukulu
umakokololera chilichonse chomwe chili mu njira yake
ndi mkokomo wa madzi amphamvu.
Ndipo wina kuti ayang'ane dzikolo,
adzangoona mdima ndi zovuta.
Ngakhale kuŵala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.