1 Am. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Antioko, mwana wa mfumu Demetriyo, amene ankakhala ku zilumba zam'nyanja, adatumiza kalata kwa Simoni, wansembe ndi mtsogoleri wa Ayuda, ndi kwa anthu a mtundu wake.

2Kalatayo idati, “Ndine mfumu Antioko, ndikupereka moni kwa Simoni, mkulu wa ansembe ndi wolamulira mtundu wa Ayuda.

3Popeza kuti anthu ena anjiru adalanda ufumu wa makolo athu, ndatsimikiza za kuulandanso kuti ndiukonze monga momwe unaliri kale. Nchifukwa chake ndalemba ankhondo ambiri aganyu, ndipo ndapanga zombo zambiri zankhondo.

4Ndimati ndidzakocheze kumtundako kuti ndiŵalondole amene adaononga dziko lathunasandutsa bwinja mizinda yambiri ya mu ufumu wanga.

5Tsono ndikutsimikizira zilolezo za kusakhoma msonkho, zimene adakupatsani mafumu akale, ndipo ndikukukhululukirani ndalama zimene mukadayenera kupereka kwa ine.

6Ndikukulola kusindikiza ndalama ndi dzina lako m'dziko lonse.

7Ndikutsimikiza kuti Yerusalemu ndi Nyumba ya Mulungu zikhale zaufulu. Ndipo zida zonse zimene udazipanga, ndi nyumba zonse zankhondo zimene udazimanga, zikhale zako ndithu.

8Ngongole zako za m'chuma cha mfumu, zatsopano ndi zam'tsogolo, zafafanizika, tsopano ndi mpaka muyaya.

9Tikadzalandanso ufumu wathu, tidzakulemekeza ndi ulemu waukulu, iweyo ndi mtundu wako ndi Nyumba ya Mulungu yomwe, kotero kuti ulemerero wanu udzadziŵika m'dziko lonse lapansi.”

10Chaka cha 174, Antioko adanyamuka nkuloŵa ku dziko la makolo ake. Ankhondo onse adadzasonkhana pafupi ndi iye, mwakuti oŵerengeka okha adatsala ndi Trifone.

11Antioko adalondola Trifoneyo amene anali atathaŵira ku Dora, dooko la nyanja.

12Adaadziŵa kuti zoopsa zikumfikira, popeza kuti ankhondo ake adaamsiya.

13Antioko adadzamanga mahema ake pafupi ndi Dora, ali ndi ankhondo oyenda pansi 120,000 ndi okwera pa akavalo 8,000.

14Adazinga mzindawo, ndipo zombo zidauzinga chakunyanja. Motero adaupanikiza ku mtunda ndi ku nyanja, osalola ndi mmodzi yemwe kuti aloŵemo kapena kutulukamo.

Kalata ya Aroma kwa Ayuda

15 1Am. 12.16 Nthaŵi imeneyo Numeniyo ndi anthu okhala naye adafika kuchokera ku Roma, ali ndi makalata amene Aroma adaalembera mafumu ndi anthu ao. Adaalembamo mau akuti,

16“Ndine Lusiyo, kazembe wa Aroma, ndikupereka moni kwa mfumu Ptolemeyo.

17Akazembe a Ayuda adabwera kwa ife ngati abwenzi athu ndi athandizi athu. Adabwera kudzayambitsanso chibwenzi ndi chigwirizano chathu chakale. Ndi mkulu wa ansembe Simoni ndi mtundu wa Ayuda amene adaŵatuma.

18Adabwera ndi chishango chagolide, kulemera kwake makilogramu 500.

19Nchifukwa chake taganiza za kuŵalembera mafumu ndi anthu ao kuti asayese kuŵavuta Ayudawo kapena kuthira nkhondo iwowo kapena mizinda yao kapena dziko lao. Taŵauzanso kuti asapalane chibwenzi ndi onse ofuna kumenyana ndi Ayudawo.

20Tidavomera kulandira chishango chaocho.

21Tsono ngati anthu oipa adathaŵa ku dziko lao, kudzaloŵa kwanu, muŵapereke kwa mkulu wa ansembe Simoni, kuti aŵalange potsata malamulo ao.”

22Lusiyo adatumizanso kalata ya mtundu womwewo kwa Demetriyo, Atale, Ariyarate ndi Arisake.

23Adaŵatumizirakonso anthu a m'maiko aŵa: Sampsame, Sparta, Delosi, Miyinde, Sikiyone, Kariya, Samosi, Pamfiliya, Lisiya, Halikarinase, Rodesi, Faselisi, Kosi, Side, Aradusi, Gortina, Kinido, Kipro ndi Kirene.

24Kalata yonga yomweyo adamtumizirakonso Simoni mkulu wa ansembe.

Antioko afuna kuvuta Ayuda

25Monsemo nkuti mfumu Antioko akuzinga mzinda wa Dora kachiŵiri. Ankaupanikiza ndi asilikali ake ndi makina ake ankhondo. Adamtsekera Trifone momwemo, mpaka anthu ake sadathenso kuloŵamo kapena kutulukamo.

26Simoni adatumizira mfumu anthu 2,000, olimba mtima, kuti akamthandize pa nkhondo. Adatumizanso siliva ndi golide ndi zida zambiri.

27Koma mfumu Antioko adakana kulandira anthuwo, ndipo adaphwanya malonjezano onse amene adaachita ndi Simoni, nkuthetsa chibwenzi chao.

28Adatuma Atenobiyo, mmodzi mwa abwenzi ake, kuti akakambe naye Simoni ndi kumuuza kuti, “Inu Ayuda, mwakhazikika ku Yopa ndi ku Gazara ndiponso m'boma lankhondo la ku Yerusalemu. Komatu yonseyo ndi mizinda ya ufumu wanga.

29Mwaŵaononga madera amenewo, mwakhala mukuchita zoipa zambiri m'dziko, ndi kulanda malo ambiri a mu ufumu wanga.

30Tsono mutibwezere mizinda imene mudalandayo. M'maiko amene mudalanda kunja kwa Yudeya mudalandiramo ndalama za misonkho, zonsezo mundipatsenso.

31Apo ai, m'malo mwake mupereke makilogramu 17,000 a siliva kulipira maikowo. Mupereke makilogramu enanso 17,000 a siliva kulipira zonse zimene mudaononga, otinso aloŵe m'malo mwa msonkho umene mizindayo yakhala ikukhoma. Mukakana pamenepo, tibwera komweko kudzakuthyolani.”

32Atenobiyo, bwenzi la mfumu, atafika ku Yerusalemu, adaona ulemerero wa Simoni ndi bokosi losungiramo ziŵiya zagolide ndi zasiliva, lodzaza ndi zinthu zina zokoma. Ndiye adadabwa kwabasi. Tsono adadziŵitsa Simoni mau a mfumu.

33Simoni adamuyankha kuti, “Si dziko lachilendotu talandali, ndipo zabwino zimene tili nazozi, si za wina. Zimenezi ndi zomwe makolo athu adatisiyira, zimenenso adani athu adaalanda mopanda chilungamo, nasunga pakanthaŵi.

34Ndiye ifeyo poona kuti nthaŵi yoyenera yafika, tidalandanso dziko la makolo athulo.

35Tsopano ndinene za Yopa ndi Gazara, mizinda imene mukuipempha. Mizinda imeneyi yakhala ikuvuta kwambiri mtundu wathu ndi dziko lathu. Komabe tidzaiperekera makilogramu 3,400 a siliva.” Atenobiyo sadayankhe ndi mau amodzi omwe.

36Adabwerera kwa mfumu ali wopsa mtima zedi. Adamdziŵitsa mau amene Simoni adayankha ndi za chuma chimene adachiwona. Nayonso mfumu idapsa mtima kwambiri.

37Nthaŵi yomweyo Trifone adaloŵa m'chombo nathaŵa kupita ku Ortosiya.

38Mfumu idasankhula Kendebeo kuti akhale nduna yolamula ankhondo a dera lakunyanja, nampatsanso magulu a ankhondo oyenda pansi ndi okwera pa akavalo.

39Idamlamula kumanga mahema ake pafupi ndi Yudeya, kumanganso Kedroni ndi kulimbitsa zipata zake, ndiponso kuyambana nkhondo ndi anthu akumeneko. Iyo mfumu idalondola Trifone.

40Kendebeo adapita ku Yaminiya. Kumeneko adayamba kuŵapsetsa mtima anthu. Adaloŵa ku Yudeya, nagwira anthu nkuŵapha.

41Adamanganso Kedroni, naikako ankhondo okwera pa akavalo ndi oyenda pansi, kuti aziyenda nkumachita zachifwamba m'miseu ya ku Yudeya, monga momwe mfumu idaalamulira.

Ana a Simoni apambana Kendebeo
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help