Mas. 119 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Malamulo a Chauta

1Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira,

amene amayenda motsata malamulo a Chauta.

2Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta,

amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,

3amene sachita zolakwa,

koma amayenda m'njira za Chauta.

4Inu Chauta, mwapereka malamulo anu

ndipo mwalamula kuti atsatidwe kwathunthu.

5Ndikadakonda kuti njira zanga zikhale zokhulupirika,

pakumvera malamulo anu.

6Tsono anthu sadzandichititsa manyazi,

ndikatsata malamulo anu onse.

7Ndidzakutamandani ndikuchita zoyenera,

ndikaphunzira malangizo anu olungama.

8Ndidzatsata malamulo anu,

musandisiye konse ndekha.

Kumvera malamulo a Chauta

9Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake

kuti akhale angwiro?

Akaŵasamala potsata mau anu.

10Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse,

musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu.

11Ndasunga mau anu mumtima mwanga,

kuti ndisakuchimwireni.

12Mutamandike, Inu Chauta,

phunzitseni malamulo lanu.

13Ndimalalika ndi mau anga

malangizo onse a pakamwa panu.

14Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa,

kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.

15Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu,

ndipo ndidzatsata njira zanu.

16Ndidzakondwera ndi malamulo anu,

ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala.

Kukondwa kwa wosunga malamulo a Chauta

17Komereni mtima ine mtumiki wanu,

kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu.

18Tsekulani maso anga

kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu.

19Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi,

musandibisire malamulo anu.

20Mtima wanga wafooka

chifukwa cholakalaka malangizo anu nthaŵi zonse.

21Inu mumadzudzula onyada,

amene ali otembereredwa,

amene amasiya malamulo anu.

22Mundichotsere zonyoza zao zondinyodola,

chifukwa ndasunga malamulo anu.

23Ngakhale mafumu andichitire upo woipa,

ine mtumiki wanu ndidzasinkhasinkhabe za malamulo anu.

24Malamulo anu amandikondwetsa,

ndiwo amene amandilangiza.

Kufunitsitsa kumvera malamulo a Chauta

25Ndangoti thapsa m'fumbi.

Bwezereni moyo monga momwe mudalonjezera.

26Pamene ndidasimba za njira zanga,

Inu mudandiyankha.

Phunzitseni malamulo anu.

27Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu,

ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa.

28Ndafookeratu ndi chisoni.

Limbitseni monga momwe mudalonjezera.

29Mundichotse m'njira zondisokeza, kuti ndisayendemo.

Mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.

30Ine ndasankhula njira yoti ndizikhala wokhulupirika,

ndaika malangizo anu mumtima mwanga.

31Ndimakangamira malamulo anu, Inu Chauta,

musalole kuti anthu andichititse manyazi.

32Ndidzatsata mokondwa njira ya malamulo anu,

mukandiwonjezera nzeru.

Pemphero lopempha nzeru

33Chauta, phunzitseni njira zosungira malamulo anu,

ndipo ndidzazitsata mpaka kumathero.

34Patseni nzeru kuti ndizisunga malamulo anu,

ndiziŵatsata ndi mtima wanga wonse.

35Munditsogolere kuti ndimvere malamulo anu,

chifukwa ndimakondwera nawo.

36Muphunzitse mtima wanga

kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.

37Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe,

mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.

38Munditsimikizire ine mtumiki wanu chipangano chanu,

chimene mumachita ndi anthu okuwopani.

39Mundichotsere chipongwe chimene ndimachiwopa,

chifukwa malangizo anu ndi abwino.

40Onani ndikulakalaka kutsata malamulo anu.

Mundipatse moyo chifukwa ndinu olungama.

Kukhulupirira malamulo a Mulungu

41Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika,

mundipulumutse monga momwe mudalonjezera.

42Pamenepo ndidzakhala nchoŵayankha anthu ondinyodola,

pakuti ndimakhulupirira mau anu.

43Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe

kulankhula mau anu oona,

pakuti ndimakhulupirira malangizo anu.

44Ndidzatsata malamulo anu kosalekeza mpaka muyaya,

45ndipo ndidzayenda ndi ufulu,

chifukwa ndasamala malamulo anu.

46Ndidzalankhula malamulo anu pamaso pa mafumu,

ndipo anthu sadzandichititsa manyazi.

47Inetu ndimasangalala ndi malamulo anu

amene ndimaŵakonda.

48Ndimalemekeza malamulo anu amene ndimaŵakonda,

ndipo ndimasinkhasinkha za malamulowo.

Kukhulupirira malamulo a Chauta

49Kumbukirani mau anu aja kwa ine mtumiki wanu,

mau amene amandipatsa chikhulupiriro.

50Chimene chimandisangalatsa m'masautso anga

nchakuti malonjezo anu amandipatsa moyo.

51Anthu osasamala za Mulungu amandinyoza kwathunthu,

komabe sindisiyana nawo malamulo anu.

52Inu Chauta, ndikamalingalira malamulo anu akalekale,

ndimasangalala,

53Ndimapsa mtima kwambiri chifukwa cha anthu oipa

amene amaphwanya malamulo anu.

54Malamulo anu asanduka nyimbo yanga

kulikonse kumene ndimapita.

55Ndimakukumbukirani usiku, Inu Chauta,

ndipo ndimatsata malamulo anu.

56Madalitso ameneŵa andifikira ine,

pakuti ndimatsata malamulo anu.

Kudzipereka ku malamulo a Chauta

57Inu Chauta, zanga zonse ndinu,

ndikulonjeza kumvera mau anu.

58Ndikukupemphani ndi mtima wanga wonse,

mundikomere mtima molingana ndi malonjezo anu aja.

59Ndikamalingalira njira zanga,

ndimatembenuka kuti nditsate malamulo anu.

60Ndimafulumira,

sindizengereza kutsata malamulo anu.

61Ngakhale anthu oipa anditchere msampha,

sindiiŵala malamulo anu.

62Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikutamandeni,

chifukwa cha malangizo anu olungama.

63Ine ndine bwenzi la anthu okuwopani,

anthu otsata malamulo anu.

64Inu Chauta, dziko lapansi nlodzaza

ndi chikondi chanu chosasinthika,

phunzitseni malamulo anu.

Ubwino wa malamulo a Chauta

65Inu Chauta, mwandikomera mtima mtumiki wanune,

molingana ndi mau anu.

66Patseni luntha ndi nzeru,

chifukwa ndimakhulupirira malamulo anu.

67Ndisanayambe kulangika ndinkasokera,

koma tsopano ndimamvera mau anu.

68Inu ndinu abwino, ndipo mumachita zabwino,

phunzitseni malamulo anu.

69Anthu osasamala za Mulungu amandisinjirira,

komabe ndimatsata malamulo anu ndi mtima wanga wonse.

70Anthu otere ndi opulukira,

koma ine ndimakondwa ndi malamulo anu.

71Ndi bwino kuti ndidalangidwa,

kuti ndiphunzire malamulo anu.

72Malamulo a pakamwa panu amandikomera

kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.

Chilungamo cha malamulo a Chauta

73Manja anu adandilenga ndi kundiwumba.

Patseni nzeru zomvetsa,

kuti ndiziphunzira malamulo anu.

74Anthu okuwopani adzandiwona ndipo adzakondwa,

popeza kuti ndakhulupirira mau anu.

75Inu Chauta, ndikudziŵa

kuti kuweruza kwanu nkolungama,

ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.

76Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse

ine mtumiki wanu,

monga momwe mudalonjezera.

77Mundichitire chifundo kuti ndikhale ndi moyo,

pakuti malamulo anu amandikondwetsa.

78Anthu osasamala za Mulungu muŵachititse manyazi,

chifukwa andilakwira pondinamizira.

Koma ine ndidzasinkhasinkha za malamulo anu.

79Anthu okuwopani abwere kwa ine

kuti aphunzire malamulo anu.

80Mtima wanga ukhale wopanda choudzudzulira

pa malamulo anu,

kuti ndisachite manyazi.

Pemphero lopempha chipulumutso

81Moyo wanga wafooka podikira chipulumutso chanu,

ndikukhulupirira mau anu.

82Maso anga afiira nkuyang'anira malonjezo anu.

Ndimafunsa kuti,

“Kodi mudzandithandiza liti?”

83Ndasanduka ngati thumba lachikopa lokhwinyata,

komabe sindiiŵala malamulo anu.

84Kodi mtumiki wanune ndipirire mpaka liti?

Kodi anthu ondizunza mudzaŵalanga liti?

85Anthu osasamala za Mulungu,

osatsata malamulo anu, andikumbira mbuna.

86Malamulo anu onse ndi osasinthika.

Anthuwo amandizunza ndi mabodza ao; thandizeni!

87Adatsala pang'ono kundichotsa pa dziko lapansi,

komabe sindidaleke kutsata malamulo anu.

88Sungani moyo wanga

chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,

kuti nditsate malamulo anu.

Kukhulupirira malamulo a Chauta

89Inu Chauta, mau anu ngokhazikika kumwambako

mpaka muyaya.

90Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka pa mibadwo yonse.

Inu mwakhazikitsa dziko, ndipo siligwedezeka.

91Zolengedwa zikupezeka lero lino

chifukwa cha kulamula kwanu,

pakuti zinthu zonse zimakutumikirani.

92Malamulo anu akadapanda kundisangalatsa,

bwenzi nditafa ndi mazunzo anga.

93Sindidzaiŵala konse malangizo anu,

pakuti mwandipatsa nawo moyo.

94Ndine wanu, pulumutseni,

pakuti ndasamala malamulo anu.

95Anthu oipa amandiŵenda kuti andiwononge,

koma ine ndimalingalira za malamulo anu.

96Ndazindikira kuti zabwino zonse zili ndi malire,

koma malamulo anu alibe konse malire.

Kukonda malamulo a Chauta

97Ndimakonda malamulo anu kwambiri,

ndimasinkhasinkha za malamulowo tsiku lonse.

98Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga,

popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse.

99Ndili ndi nzeru za kumvetsa

kupambana aphunzitsi anga onse,

pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu.

100Ndili ndi nzeru kupambana okalamba,

pakuti ndimatsata malamulo anu.

101Ndimaletsa miyendo yanga

kuti isayende m'njira yoipa iliyonse,

kuti choncho ndizisunga mau anu.

102Sindisiyana nawo malangizo anu,

pakuti Inu mudandiphunzitsa

103mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa.

Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga.

104Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa

chifukwa cha malamulo anu.

Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.

Malamulo a Chauta amaunikira

105mau anu ndiye nyale ya mapazi anga,

ndipo amaunikira njira yanga.

106Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza

kuti ndidzamvera malangizo anu olungama.

107Ndazunzika koopsa,

Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja.

108Chauta, landirani mapemphero anga oyamika,

ndipo mundiphunzitse malangizo anu.

109Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse,

komabe sindiiŵala malamulo anu.

110Anthu oipa anditchera msampha,

komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu.

111Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya,

zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.

112Mtima wanga muuphunzitse

kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse.

Malamulo a Chauta amapulumutsa munthu

113Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri,

koma ndimakonda mau anu.

114Inu ndinu malo anga obisalako

ndiponso chishango changa,

ndimakhulupirira mau anu.

115Chokereni inu, anthu ochita zoipanu,

kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga.

116Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja,

kuti ndizikhala ndi moyo,

ndipo anthu asandichititse manyazi,

chifukwa ndine wokhulupirika.

117Chirikizeni kuti ndipulumuke,

kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu.

118Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu,

zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake.

119Anthu onse oipa a pa dziko lapansi,

mumaŵayesa ngati zakudzala,

nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu.

120Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani,

ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu.

Kumvera malamulo a Chauta

121Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino.

Musandisiye m'manja mwa ondizunza.

122Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino

mtumiki wanune,

musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze.

123Maso anga atopa

chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu,

chifukwa cha kudikira

kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi.

124Komereni mtima mtumiki wanune,

chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika,

ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

125Ndine mtumiki wanu,

mundipatse nzeru zomvetsa,

kuti ndizidziŵa malamulo anu.

126Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu,

popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu.

127Koma ine ndimasamala malamulo anu

kupambana golide, golide wosungunula bwino.

128Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga.

Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.

Kufunitsitsa kumvera malamulo a Chauta

129Malamulo anu ndi abwino,

nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse.

130Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala,

kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.

131Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa,

chifukwa ndimalakalaka malamulo anu.

132Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima

monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani.

133Chirikizani mayendedwe anga

molingana ndi mau anu aja,

musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira.

134Pulumutseni kwa anthu ondizunza,

kuti ndizitsata malamulo anu.

135Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu,

ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

136Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje,

chifukwa anthu satsata malamulo anu.

Chilungamo cha malamulo a Chauta

137Ndinu olungama Chauta,

ndipo kuweruza kwanu nkolungama.

138Malamulo amene mwatipatsa,

ndi olungama ndi okhulupirika ndithu.

139Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga,

chifukwa adani anga amaiŵala mau anu.

140Malonjezo anu ndi otsimikizika,

ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda.

141Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka,

komabe sindiiŵala malamulo anu.

142Kulungama kwanu nkwamuyaya,

ndipo malamulo anu ndi oona.

143Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe,

koma malamulo anu amandisangalatsa.

144Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya,

patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo.

Pemphero lopempha chipulumutso

145Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse,

mundiyankhe, Inu Chauta.

Ndidzatsata malamulo anu.

146Ndikukulirirani, mundipulumutse,

kuti ndizitsata malamulo anu.

147Ndimadzuka tambala asanalire,

kuti ndipemphe chithandizo.

Ndimakhulupirira mau anu.

148Ndimakhala maso usiku wonse,

ndikusinkhasinkha za malonjezo anu.

149Imvani liwu langa

chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

Inu Chauta, sungani moyo wanga

chifukwa cha chilungamo chanu.

150Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira.

Iwo ali kutali ndi malamulo anu.

151Koma Inu Chauta muli pafupi,

ndipo malamulo anu onse ndi oona.

152Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe

kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya.

Kupempha chipulumutso

153Yang'anani masautso anga,

ndipo mundipulumutse,

popeza kuti sindiiŵala malamulo anu.

154Munditchinjirize pa mlandu wanga,

ndipo mundiwombole.

Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja.

155Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa,

pakuti safunafuna malamulo anu.

156Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta,

mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu.

157Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka,

koma sindisiyana nawo malamulo anu.

158Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika,

chifukwa satsata malamulo anu.

159Onani m'mene ndimakondera malamulo anu,

sungani moyo wanga

chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika

160mau anu ndi oona okhaokha,

malangizo anu onse olungama ngamuyaya.

Kudzipereka ku malamulo a Chauta

161Mafumu amandizunza popanda chifukwa,

koma mtima wanga umaopa mau anu.

162Ndimakondwa ndi mau anu

monga munthu amene wapeza chuma chambiri.

163Ndimadana ndi anthu abodza,

zoonadi, ndimanyansidwa nawo,

koma ndimakonda malamulo anu.

164Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku,

chifukwa cha malangizo anu olungama.

165Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu,

palibe china chotha kuŵagwetsa.

166Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta,

ndipo ndimatsata malamulo anu.

167Mzimu wanga umatsata malamulo anu,

pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse.

168Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu,

pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona.

Pemphero lopempha chithandizo

169Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta.

Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja.

170Kupempha kwanga kumveke kwa Inu.

Mundipulumutse potsata malonjezo anu.

171Pakamwa panga padzakutamandani,

chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu.

172Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu,

chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.

173Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza,

chifukwa ndatsata malamulo anu.

174Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse.

Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa.

175Lolani kuti ndikhale moyo,

kuti ndizikutamandani,

ndipo malangizo anu azindithandiza.

176Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera,

koma mundifunefune ine mtumiki wanu,

pakuti sindiiŵala malamulo anu.

Pemphero lopempha chithandizo

Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help