1Ana a Israele naŵa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni,
2Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi, ndi Asere.
Zidzukulu za Yuda3Ana a Yuda naŵa: Eri, Onani, ndi Sela. Ana atatu ameneŵa adamubalira ndi Batisuwa mkazi wa ku Kanani. Tsono Eri mwana wa Yuda anali wa makhalidwe oipa, choncho Chauta adamupha.
4Mpongozi wake Tamara nayenso adamubalira Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu.
5Ana a Perezi naŵa: Hezironi ndi Hamuli.
6Ana a Zera naŵa: Zimiri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse pamodzi analipo asanu.
7Yos. 7.1 Ana a Karimi naŵa: Akara amene adaavuta Aisraele. Iyeyo adaaba zinthu zoyenera kuziwononga.
8Mwana wa Etani anali Azariya.
Makolo a Davide9Ana amene adabereka Hezironi naŵa: Yerameele, Ramu ndi Kelebe.
10Ramu adabereka Aminadabu, Aminadabu adabereka Nasoni, mkulu wa fuko la Yuda.
11Nasoni adabereka Salimoni, Salimoni adabereka Bowazi,
12Bowazi adabereka Obede, Obede adabereka Yese.
13Yese adabereka Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, wachitatu Simea,
14wachinai Netanele, wachisanu Radai,
15wachisanu ndi chimodzi Ozemu, wachisanu ndi chiŵiri Davide.
16Alongo ao anali Zeruya ndi Abigaile. Ana a Zeruya naŵa: Abisai, Yowabu ndi Asahele, onse pamodzi atatu.
17Abigaile adabala Amasa ndipo bambo wake wa Amasa anali Yetere Mwismaele.
Zidzukulu za Hezironi18Kalebe mwana wa Hezironi anali nawo ana omubalira mkazi wake Azuba ndiponso Yerioti. Ana amene adabala mkaziyo naŵa: Yesere, Sobabu ndi Aridoni.
19Atafa Azuba, Kalebe adakwatira Efrati amene adamubalira Huri.
20Huri adabereka Uri, ndipo Uri adabereka Bezalele.
21Pambuyo pake Hezironi, ali wa zaka 60, adakakwatira mwana wa Makiri bambo wake wa Giliyadi. Ndipo mkaziyo adamubalira Segubu.
22Segubu adabereka Yairi amene anali ndi mizinda 23 m'dziko la Giliyadi.
23Koma anthu a ku Gesuri ndi a ku Aramu adaŵalanda Havoti-Yairi, Kenati pamodzi ndi midzi yake yomwe, yonse pamodzi inalipo midzi 60. Onseŵa anali adzukulu a Makiri, bambo wake wa Giliyadi.
24Atafa Hezironi, Kalebe adakwatira Efurata, mkazi wa bambo wake Hezironi. Ndipo mkaziyo adamubalira Asuri, bambo wake wa Tekowa.
Zidzukulu za Yerameele25Ana a Yerameele, mwana wachisamba wa Hezironi, naŵa: Ramu mwana wachisamba, Buna, Oreni, Ozemu, ndi Ahiya.
26Yerameele analinso ndi mkazi wina dzina lake Atara. Mkaziyu adabala Onamu.
27Ana a Ramu, mwana wachisamba wa Yerameele, anali Maazi, Yamini ndi Ekeri.
28Ana a Onamu anali Samai ndi Yada. Ana a Samai anali Nadabu ndi Abisuri.
29Mkazi wake wa Abisuri anali Abihaili, ndipo mkaziyo adamubalira Abani ndi Molidi.
30Ana a Nadabu anali Seledi ndi Apaimu. Seledi adafa opanda ana.
31Mwana wa Apaimu anali Isi. Mwana wa Isi anali Sesani. Mwana wa Sesani anali Alai.
32Ana a Yada mbale wa Samai anali Yetere ndi Yonatani. Yetere adafa opanda ana.
33Ana a Yonatani anali Peleti ndi Zaza. Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Yerameele.
34Sesani analibe ana aamuna, anali ndi ana aakazi okhaokha. Koma anali ndi kapolo wake wa ku Ejipito, dzina lake Yara.
35Motero Sesani adakwatitsa mwana wake wamkazi kwa Yara kapolo wake uja. Ndipo mkaziyo adamubalira Attai.
36Attai adabereka Natani, Natani adabereka Zabadi.
37Zabadi adabereka Efilala, Efilala adabereka Obede.
38Obede adabereka Yehu, Yehu adabereka Azariya.
39Azariya adabereka Helezi, Helezi adabereka Eleasa.
40Eleasa adabereka Sisimai, Sisimai adabereka Salumu.
41Salumu adabereka Yekamiya, ndipo Yekamiya adabereka Elisama.
Zidzukulu zina za Kalebe42Ana a Kalebe mbale wa Yerameele naŵa: Maresa, mwana wake wachisamba, bambo wake wa Zifi. Mwana wa Maresa anali Hebroni.
43Ana a Hebroni naŵa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema.
44Sema adabereka Rahama, bambo wake wa Yorikeamu ndipo Rekemu adabereka Samai.
45Mwana wa Samai anali Maoni. Tsono Maoni adabereka Betezuri.
46Nayenso Efa, mzikazi wa Kalebe, adamubalira Harani, Moza ndi Gazezi. Harani adabereka Gazezi.
47Ana a Yadai naŵa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efa ndi Saafi.
48Maaka, mzikazi wa Kalebe, adamubalira Sebere ndi Tirihana.
49Mkaziyo adabalanso Saafi, bambo wake wa Madimana, ndi Seva bambo wake wa Makibena ndiponso bambo wa Gibea. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa.
50Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Kalebe.
Ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata, naŵa: Sobala amene adabereka Kiriyati-Yearimu,
51Salima amene adabereka Betelehemu, ndiponso Harefi amene adabereka Betegadere.
52Sobala bambo wake wa Kiriyati-Yearimu adaberekanso ana ena, naŵa: Harowe, ndiye kuti theka la Amenuwoti.
53Mabanja a Kiriyati-Yearimu naŵa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Ameneŵa ndiwo makolo a Azorati ndi Aesitaoli.
54Ana a Salima naŵa: Betelehemu, Anetofa, Ataroti-Beti-Yowabu ndi hafu la Amanahati, ndiponso Azori.
55Mabanjanso a alembi amene ankakhala ku Yabesi naŵa: Atirati, Asimeati ndi Asukati. Ameneŵa ndiwo Akeni amene adachokera kwa Hamati, kholo la banja la Rekabu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.