1Imbirani Chauta nyimbo yatsopano!
Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi!
2Imbirani Chauta, tamandani dzina lake!
Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
3Lengezani za ulemerero wake
kwa anthu a mitundu yonse,
simbani za ntchito zake zodabwitsa
kwa anthu a m'maiko onse.
4Chauta ngwamkulu,
ngwoyenera kumtamanda kwambiri.
Nwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
5Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu
ndi mafano chabe.
Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba.
6Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake.
Mphamvu ndi kukongola zili m'Nyumba mwake.
7 Mas. 29.1, 2 Tamandani, inu anthu a mitundu yonse,
vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nzake.
8Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.
Bwerani ndi zopereka,
ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake.
9Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera,
njenjemerani pamaso pake,
inu anthu onse a pa dziko lapansi.
10Uzani mitundu ya anthu kuti,
“Chauta ndiye Mfumu.
Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba,
silidzagwedezeka konse.
Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.”
11Zakumwamba zisangalale,
zapansi pano zikondwere,
nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo.
12Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo.
Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa
13pamaso pa Chauta,
pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi.
Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo,
adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.