1Mzimu wa Mulungu udamtsikira Azariya mwana wa Odedi.
2Tsono iye adatuluka mu mzinda wake kukakomana ndi Asa, ndipo adamuuza kuti, “Ndimvereni inu Asa, Ayuda nonsenu ndi inu Abenjamini. Chauta ali nanu nthaŵi yonse imene inu muli ndi Iye. Mukamfunafuna mudzampeza. Koma mukamsiya, nayenso adzakusiyani.
3Pa nthaŵi yaitali Aisraele adakhala opanda Mulungu woona, ndiponso opanda wansembe woŵaphunzitsa, ndipo analibe malamulo.
4Koma pamene anali pa mavuto, namabwera kudzafunafuna Chauta, Mulungu wa Israele, ankamupeza.
5Pa masiku amenewo panalibe mtendere kwa munthu amene ankatuluka kapena kuloŵa, pakuti mavuto adaaŵagwera onse amene ankakhala m'makomo.
6Anthuwo adagalukirana, mtundu wina unkamenyana ndi mtundu wina, mzinda unkamenyana ndi mzinda wina, pakuti Mulungu adaaŵavuta ndi mazunzo osiyanasiyana.
7Koma inu limbani mtima, manja anu asafooke chifukwa mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.”
8Tsono Asa atamva mau ameneŵa, mau aulosi a Azariya mwana wa Odedi, adalimba mtima. Adachotsa mafano onyansa ku dziko lonse la Yuda ndi la Benjamini. Adachotsanso mafano ku mizinda imene adailanda ku dziko lamapiri la Efuremu. Ndipo adakonza guwa la Chauta limene linali patsogolo pa khonde la Nyumba ya Chauta.
9Adasonkhanitsa Ayuda onse ndi Abenjamini ndiponso anthu a ku Efuremu, Manase ndi Simeoni amene ankangokhala nao, pakuti anthu ambiri anali atathaŵira kwa mfumu Asa, kuchoka ku Israele, ataona kuti Chauta Mulungu wake anali naye Asayo.
10Anthuwo adasonkhana ku Yerusalemu pa mwezi wachitatu chaka cha 15 cha ufumu wa Asa.
11Tsiku limenelo adapereka nsembe kwa Chauta zotapako pa za zofunkha zimene adaabwera nazo, ndiye kuti ng'ombe 700, ndi nkhosa 7,000.
12Tsono adapangana zoti azifunafuna Chauta, Mulungu wa makolo ao, ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse.
13Adaamvana kuti aliyense wosafunafuna Chauta, Mulungu wa Israele, aziphedwa, kaya ndi wamng'ono kaya wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.
14Zimenezi adalumbira kwa Chauta mokweza mau ndi mofuula, alikuliza malipenga ndi mbetete.
15Ndipo anthu onse a ku Yuda adakondwa pa mwambo wolumbirirawo, pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse. Ankafunafuna Chauta kwambiri, ndipo adampezadi. Motero Chauta adaŵapatsa mtendere ponse poŵazungulira.
Ntchito zina za Asa16Mfumu Asa adachotsa ngakhale ufumu wa Maaka, gogo wake, chifukwa choti Maakayo anali atachita chinthu choipa kwambiri popanga fano. Asa adagwetsa fanolo, nalitswanya, ndipo adakalitentha ku mtsinje wa Kidroni.
17Koma akachisi sadaŵaononge ku Israele. Ngakhale zinali choncho, mtima wa Asa udakhala wangwiro masiku onse a moyo wake.
18Ndipo adabwera ku Nyumba ya Chauta ndi mphatso zimene bambo wake adaapereka, ndiponso zopereka iye mwini, monga siliva, golide ndi ziŵiya.
19Tsono panalibenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ufumu wa Asa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.