1 Mas. 54 Tsiku lina anthu a ku Zifi adabwera kwa Saulo ku Gibea, namuuza kuti, “Davide akubisala ku phiri la Hakila limene lili kuvuma kwa Yesimoni.”
2Saulo adanyamuka napita ku chipululu cha Zifi atatenga ankhondo 3,000 osankhidwa, kuti akafunefune Davide kuchipululuko.
3Adamanga zithando zankhondo pa phiri la Hakila, limene lili pambali pa mseu, chakuvuma kwa Yesimoni. Koma Davide adakhalabe kuchipululuko. Tsono ataona kuti Saulo akumlondola,
4Davide adatuma anthu oti akazonde, ndipo adapezadi kuti Saulo wafika.
5Ndiye Davide adanyamuka nakafika pa malo amene Saulo adaamangapo zithando zake. Ndipo adaona malo amene ankagonapo Sauloyo ndi Abinere mwana wa Nere, mkulu wa ankhondo a Saulo. Sauloyo ankagona m'zithandomo, ndipo gulu lonse lankhondo lidaamanga zithando pomzungulira.
6Tsono Davide adafunsa Ahimeleki Muhiti ndi Abisai mkulu wa Yowabu, mwana wa Zeruya, kuti, “Kodi ndani apite nane ku zithando za Saulo?” Abisai adati, “Ine ndipita nanu.”
7Choncho Davide ndi Abisai adakaloŵa ku zithando zankhondo usiku. Saulo anali gone m'chithando chake, atazika mkondo wake pansi cha kumutu kwake. Abinere ndi ankhondo onse adaagona momzungulira.
8Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kaŵiri.”
9Koma Davide adamuuza kuti, “Ai, usamuphe. Ndani angathe kupweteka wodzozedwa wa Chauta nakhala wosachimwa?”
10Ndipo adalamulira kuti, “Pali Chauta wamoyo, Chautayo ndiye adzamkanthe kapena pamene lidzafike tsiku lake lakumwalira, kapena pamene adzapite ku nkhondo nakaphedwa.
111Sam. 24.6 Chauta andiletse kuti ndisapweteke wodzodzedwa wake. Koma tsono tingotenga mkondo umene uli kumutu kwakewu ndi mtsuko wa madziwu, ndipo tizipita.”
12Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziŵa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaaŵagonetsa tulo tofa nato.
13Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu.
14Tsono Davide adaitana gulu lankhondo ndi Abinere mwana wa Nere, naŵafunsa kuti, “Kodi sukumva iwe Abinere?” Abinere adayankha kuti, “Kodi ndiwe yani ukuitana mfumuwe?”
15Davide adafunsa Abinere kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndani ali wofanafana nawe m'dziko la Israele? Nanga chifukwa chiyani sudamlonde mbuyako mfumu? Tsopano apa munthu wina anabwera kumeneko kuti adzaphe mbuyakoyo.
16Zimene wachitazi si zabwino ai. Pali Chauta wamoyo, nonsenu muyenera kuphedwa chifukwa simudalonde mbuye wanu, wodzozedwa wa Chauta. Uyang'ane kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwake.”
17Saulo adazindikira liwu la Davide, ndipo adafunsa kuti, “Kodi liwu limeneli ndi lako, iwe mwana wanga Davide?” Davide adayankha kuti, “Inde, ndi liwu langadi, mbuyanga mfumu.
18Chifukwa chiyani mbuyanga mukundilondola ine mtumiki wanu? Kodi ndachita chiyani? Kodi tchimo langa nlotani?
19Nchifukwa chake tsono, mbuyanga mfumu, mumve mau a ine mtumiki wanu. Ngati ndi Chauta amene wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, Chautayo apepesedwe ndi nsembe. Koma ngati ndi anthu, iwowo Chauta aŵatemberere, pakuti tsono andipirikitsa, kuti ndisakhale nao m'dziko la Chauta. Akuti, ‘Pita katumikire milungu ina.’
20Ndiye inu tsono musalole kuti ndifere kutali ndi Chauta, pakuti mfumu ya Aisraele yatuluka kudzandifunafuna ine nthata, monga momwe amachitira munthu wosaka nkhwali ku thengo.”
21Tsono Saulo adati, “Ndachimwa. Bwerera, mwana wanga Davide, sindidzakuchitanso choipa, popeza kuti moyo wanga wauwona ngati wa mtengo wapatali. Ndithu ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.”
22Apo Davide adayankha kuti, “Suwu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi mwa ankhondowo adzatenge.
23Chauta amadalitsa munthu wokhulupirika ndi wochita zabwino. Chauta anakuperekani m'manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu.
24Monga ndakusungirani moyo wanu leromu, momwemonso Chauta ateteze moyo wanga, ndipo andipulumutse m'mavuto anga onse.”
25Apo Saulo adauza Davide kuti, “Mulungu akudalitse mwana wanga Davide. Udzachita zazikulu, ndipo pa zonsezo udzapambana.” Choncho Davide adachokapo, ndipo Saulo adabwerera kwao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.