1 Mbi. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Akonzekera zokatenga bokosi lachipangano

1Davide adadzimangira nyumba zina mu mzinda wa Davide. Adakonza malo a Bokosi lachipangano la Chauta, namanga hema loikamo Bokosilo.

2Deut. 10.8 Tsono Davide adati, “Alevi okha ndiwo amene asenze Bokosi lachipangano la Mulungu, wina aliyense ai, pakuti Chauta adasankhula Aleviwo kuti azisenza Bokosilo ndiponso kuti azimtumikira mpaka muyaya.”

3Kenaka Davide adasonkhanitsa Aisraele onse ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta ndi kubwera nalo ku malo ake amene Davideyo adalikonzera.

4Tsono Davide adasonkhanitsa zidzukulu za Aroni ndi Alevi enanso.

5Mwa ana a Kohati, Uriyele ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 120.

6Mwa ana a Merari, Asaya ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 220.

7Mwa ana a Geresomo, Yowele ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 130.

8Mwa ana a Elizafani, Semaya ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 200.

9Mwa ana a Hebroni, Eliyele ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 80.

10Mwa ana a Uziyele, Aminadabu ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 112.

11Tsono Davide adaitana ansembe aŵa Zadoki ndi Abiyatara, kudzanso Alevi aŵa, Uriyele, Asaya, Yowele, Semaya, Eliyele ndi Aminadabu.

12Ndipo adaŵauza kuti, “Inuyo ndinu atsogoleri a mabanja a makolo a Alevi. Mudzipatule eniakenu ndi abale anu omwe, kuti musenze Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo mukaliike ku malo amene ndidalikonzera.

13Popeza kuti simudalinyamule ndinu poyamba paja, Chauta adatikantha, chifukwa choti sitidasamale mwambo wake polinyamula.”

14Motero ansembe ndi Alevi aja adadzipatula kuti akanyamule Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wa Aisraele.

15Eks. 25.14Ndipo Alevi adanyamula ndi mphiko Bokosilo pamapuzi pao, monga momwe Mose adaalamulira potsata mau a Chauta.

16Pambuyo pake Davide adalamulanso atsogoleri a Alevi kuti asankhe ena mwa abale ao, kuti aziimba ndi kuliza mwamphamvu zipangizo zoimbira monga azeze, apangwe, ndiponso ziwaya zamalipenga, kuti mau achimwemwe amveke bwino.

17Motero Alevi adasankha Hemani mwana wa Yowele, ndipo mwa abale ake adasankha Asafu mwana wa Berekiya. Mwa ana a Merari, abale ao, adasankha Etani mwana wa Kusaya.

18Pamodzi ndi iwowo, otsatana nawo osankhidwanso anali Zekariya, Yaaziyele, Semiramoti, Yehiyele, Uni, Eliyabu, Benaya, Maaseiya, Matitiya, Elifelehu ndiponso Mikineya, kudzanso alonda apamakomo, Obededomu ndi Yeiyele.

19Anthu oimba aja, Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo amene ankaimba ziwaya zamalipenga zamkuŵa.

20Zekariya, Aziyele, Semarimoti, Yehiyele, Uni, Eliyabu, Maaseiya ndi Benaya ndiwo amene ankaimba azeze a liwu lapamwamba.

21Koma Matitiya, Elibelehu, Mikineya, Obededomu, Yeiyele ndiponso Azaziya ndiwo amene ankatsogolera, namaimba apangwe a liwu lapansi.

22Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi poimba nyimbo, ndiye amene ankatsogolera kuimbako, poti anali katswiri.

23Benekiya ndi Elikana ndiwo adasankhidwa kuti akhale alonda apakhomo olonda Bokosilo.

24Ansembe aŵa, Sebaniya, Yosafati, Netanele, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliyezere ndiwo ankayenera kuliza malipenga patsogolo pa Bokosi lachipangano la Mulungu. Obededomu ndi Yehiya nawonso anali alonda apakhomo a Bokosilo.

Bokosi lachipangano abwera nalo ku Yerusalemu(2 Sam. 6.12-22)

25Motero Davide pamodzi ndi akuluakulu a Aisraele ndiponso atsogoleri a ankhondo zikwi-zikwi, adapita mokondwera kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta kunyumba kwa Obededomu.

26Pofuna kuti Mulungu aŵathandize Alevi amene ankanyamula Bokosilo, anthuwo adaperekera nsembe ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.

27Davide anali atavala mkanjo wabafuta wa thonje losalala, monga momwe adavalira Alevi amene ankanyamula Bokosi lachipangano, kudzanso anthu oimba ndiponso Kenaniya mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo. Koma Davide adaavalanso efodi.

28Motero Aisraele onse adabwera nalo Bokosi lachipangano la Chauta akufuula ndi kuimba mbetete, malipenga ndi ziwaya zamalipenga. Ankalizanso azeze ndi apangwe mokweza.

29Pamene Bokosi lachipangano lija lidadza ku mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help