1 Miy. 1.20, 21 Kodi suja nzeru imaitana?
Suja nzeru zomvetsera zinthu zimakweza mau ake?
2Nzeru imakhala pa zitunda m'mbali mwa njira,
imakaima pa mphambano za miseu.
3Imafuula pafupi ndi zipata kumaso kwa mzinda,
ndiponso pamakomo poloŵera, imati,
4“Inu anthu, ndikukuitanani,
kuitanaku ndikuitana anthu nonsenu.
5Inu osadziŵa kanthunu, phunzirani nzeru,
inu opusanu, khalani tcheru.
6Mverani, ndikuuzani zazikulu kwambiri,
pakamwa panga palankhula zolungama.
7Pakamwa panga palankhula zoona,
kulankhula zoipa nchinthu chonyansa m'kamwa mwanga.
8Mau onse a pakamwa panga ngokondweretsa Mulungu,
m'mau angawo mulibe zopotoka kapena zokhotakhota.
9Mau anga ngoona kwa munthu womvetsa,
ngokhoza kwa anthu odziŵa zinthu.
10Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva,
funitsitsani kudziŵa zinthu,
osati kuthamangira golide wabwino kwambiri.
11 Mphu. 24.1-22 Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali.
Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.
12Ine nzeru ndimakhalira limodzi ndi kuchenjera.
Ndimadziŵa zinthu ndipo ndimaganiza moyenera.
13Kuwopa Chauta nkudana ndi zoipa.
Kunyada, kudzitama, kuchita zoipa
ndi kulankhula zonyenga,
zonsezo ndimadana nazo.
14Ndili ndi uphungu ndi maganizo abwino.
Ndimamvetsa bwino zinthu, ndilinso ndi mphamvu.
15Ndimathandiza mafumu polamulira ndine,
olamulira ndimaŵathandiza ndine kulamula zolungama.
16Ndine ndimathandiza akalonga polamula,
ndine ndimathandiza akuluakulu poweruza m'dziko.
17Anthu ondikonda, ine nzeru ndimaŵakonda,
anthu ondifunafuna mosamala, amandipeza.
18Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu,
chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira.
19Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide,
ngakhale golide wosalala.
Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi.
20Ndimachita zomwe zili zoyenera,
sindipatuka kuchoka m'njira za chilungamo.
21Ndimaŵapatsa chuma anthu ondikonda,
ndi kudzaza nyumba zao zosungiramo chuma.
22 Mphu. 1.4, 9; Chiv. 3.14 “Chauta adandilenga ine nzeru
pa chiyambi cha ntchito zake.
Mwa ntchito zake zakalekale woyambirira ndinali ine.
23Ndidapangidwa masiku akalekale,
pachiyambiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe.
24Nyanja zozama zisanalengedwe,
padakalibe akasupe odzaza ndi madzi,
nkuti ine nditabadwa kale.
25Mapiri asanaumbidwe, magomo asanakhalepo,
Mulungu anali atandilenga ineyo;
26lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake,
lisanakhaleponso dothi loyamba la dziko lapansi.
27 Lun. 9.9; Mphu. 24.3-6 Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba,
pamene ankalemba mzere wa malire a nyanja yozama,
28pamene ankaika thambo m'malo mwake,
pamene ankatsekula akasupe a m'nyanja yozama,
29pamene ankaika malire a nyanja
kuti madzi ake asabzole malirewo,
pamene ankaika maziko a dziko lapansi.
30Nthaŵiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake,
ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku,
ndikusangalala pamaso pake nthaŵi zonse.
31Ndinkasangalala m'dziko lake lokhalamo anthu,
ndi kumakondwa nawo ana a anthu.
32 Mphu. 14.20-27 “Ndipo tsopano, ana anga, tamverani,
ngodala anthu amene amasunga malangizo anga.
33Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru,
musamanyozere mau anga.
34Ngwodala munthu amene amatchera khutu kwa ine,
amene amakhala pakhomo panga tsiku ndi tsiku,
amene amadikira pa chitseko changa.
35Paja wondipeza ine, wapeza moyo,
ndipo amapeza kuyanja pamaso pa Chauta.
36Koma wosandipeza ine, akudzipweteka ameneyo.
Onse odana ndi ine, ngokonda imfa amenewo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.