Mas. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Liwu la Chauta m'namondweSalmo la Davide.

1 Mas. 96.7-9 Tamandani Chauta, inu okhala kumwamba.

Tamandani ulemerero wake ndi mphamvu zake.

2Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta.

Mumpembedze mu ulemu wa ungwiro wake.

3Liwu la Chauta likumveka pamwamba pa nyanja.

Mulungu waulemerero wachita bingu,

liwu lake lamveka pa nyanja yaikulu.

4Liwu la Chauta ndi lamphamvu,

liwu la Chauta ndi laulamuliro.

5Liwu la Chauta limathyola mikungudza,

Chauta amathyolathyoladi mikungudza ya ku Lebanoni.

6Amagwedeza phiri la Lebanoni

kuti lizivinavina ngati likonyani,

amavinitsa phiri la Sirioni ngati mwanawanjati.

7Liwu la Chauta likutulutsa malaŵi amoto.

8Liwu la Chauta likugwedeza chipululu,

Chauta akugwedeza chipululu cha Kadesi.

9Liwu la Chauta likuzunguza miŵanga

likupulula masamba a mitengo yonse m'dondo.

Onse a m'nyumba mwake akufuula kuti,

“Ulemererowo!”

10Chauta amalamulira nyanja zonse,

amakhala kwamuyaya pa mpando wake wachifumu.

11Chauta amapatsa anthu ake mphamvu.

Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere.

Nyimbo ya Chipulumutso.

Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help