1“Adani akhala akundizunza kwambiri
kuyambira unyamata wanga,”
Israele anene choncho tsopano,
2“Adani akhala akundizunza kwambiri
kuyambira unyamata wanga,
komabe sadandipambane.
3“Pondikwapula adani anga
adachita ngati kulima pamsana panga,
kulima mizere yaitali.”
4Koma Chauta ndi wolungama,
wandimasula zingwe za anthu oipa.
5Anthu onse odana ndi Ziyoni
agonjetsedwe ndi kupirikitsidwa mwamanyazi.
6Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,
umene umafota usanakule.
7Woumweta sangadzaze nkumanja komwe,
womanga mitolo sangamange nchitsakato chomwe.
8Anthu odutsapo sadzanena kwa omwetawo kuti,
“Madalitso a Chauta akhale nanu.”
“Tikukudalitsani potchula dzina la Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.