1Ndaloŵa m'munda mwanga,
iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga.
Ndikukolola mure wanga ndi zokometsera chakudya.
Ndikudya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe.
Ndikumwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.
Akazi
Inu apaubwenzi, idyani ndi kumwa:
Inu okondana, imwani kwambiri!
Nyimbo YachinaiMkazi
2Kugona ndinagona,
koma mtima wanga unali maso.
Tamverani! Wokondedwa wanga akugogoda.
Mwamuna
“Tanditsekulira iwe mlongo wanga,
iwe wokondedwa wanga,
iwe nkhunda yanga, iwe wangwiro wanga.
Mutu wanga wanyowa ndi mame,
tsitsi langa lachita madzi
chifukwa cha nkhungu yausiku.”
Mkazi
3Zovala ndavula kale,
ndingazivalenso bwanji?
Ndasamba kale m'miyendo,
nanga ndiidetsenso poyenda?
4Pamene wokondedwa wanga adangoti pisu dzanja
pa chiboo chapachitseko,
mtima wanga udachita kuti phwii!
5Ndidanyamuka kukamtsekulira wokondedwa wanga,
manja anga ali noninoni ndi mure.
Zalazi zili mure chuchuchu
pa zogwirira za mpiringidzo.
6Ndidamtsekulira wokondedwa wanga,
koma nkuti iyeyo atachokapo, atapita.
Pamene iye ankalankhula,
mtima wanga udangoti fumu!
Ndidamfunafuna koma osampeza.
Ndidamuitana, koma iye osandiyankha.
7Alonda adandipeza pamene ankayendera mzinda.
Adandimenya mpaka kundipweteka.
Alonda apamalingawo adandilanda mwinjiro wanga.
8Inu akazi a ku Yerusalemu,
ndithu ndakupembani,
mukampeza wokondedwa wangayo
mumuuze kuti ine ndikumva chikondi chodwala nacho.
Akazi
9Iwe wokongola koposa akazi onsewe,
kodi wokondedwa wakoyo
ngwopambana wina aliyense bwanji?
Kodi wokondedwa wakoyo
ngwopambana ena onse chotani
kuti uzichita kupemba motere?
Mkazi
10Wokondedwa wangayo ngwokongola,
ndiponso wathanzi,
wodziŵika zedi pakati pa amuna zikwi khumi.
11Mutu wake uli ngati golide wosalala kwambiri.
Tsitsi lake nlopotana bwino,
lakuda bwino ngati nthenga za khwangwala.
12Maso ake amaoneka okongola
ngati nkhunda zitakhala pa akasupe a madzi,
ngati nkhunda zitasamba mu mkaka,
zitangoima bwinobwino.
13Masaya ake ali ngati timinda
ta mbeu zokometsera chakudya,
zopatsa fungo lokoma.
Milomo yake ili ngati akakombo,
ili noninoni ndi zodzoladzola za mure.
14Mikono yake ili ngati nthambi zagolide
za makaka a miyala yamtengowapatali.
Thupi lake nlosalala ngati mnyanga wanjovu
woti aikamo miyala ya safiro.
15Miyendo yake ili ngati mizati yamwala
yokhazikika pa maziko agolide.
Ali ndi maonekedwe aulemerero
ngati mapiri a ku Lebanoni,
maonekedwe aulemu
ngati mitengo ya paini ya pamapiripo.
16Milomo yake njosangalatsa kwambiri,
munthuyo amanditenga mtima kwabasi.
Ameneyutu ndiye wokondedwa wanga,
ndiponso bwenzi langa,
inu akazi a ku Yerusalemu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.