1 Aga. 4.27 “Fuula ndi chimwemwe iwe Yerusalemu
amene wakhala ngati chumba chopanda ana,
fuula mosangalala,
iwe amene sudamvepo zoŵaŵa za kubala.
Pakuti tsopano udzakhala ndi ana ochuluka
kuposa mkazi amene sadasiyidweko ndi mwamuna wake,”
akuterotu Chauta.
2“Ukuze malo omangapo hema lako,
ufunyulule kwambiri nsalu zake.
Usalephere, utalikitse zingwe zake,
ndipo ulimbitse zikhomo zake.
3Udzasendeza malire ake uku ndi uku.
Zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina,
zidzadzaza mizinda imene idasiyidwa.
4“Usaope, chifukwa sadzakunyozanso,
usataye mtima poti sadzakupeputsanso.
Udzaiŵala zimene zidakuchititsa manyazi
pa unyamata wako,
manyazi a pa umasiye wako sudzaŵakumbukanso.
5Mlengi wako ali ngati mwamuna wako.
Chauta Wamphamvuzonse ndiye dzina lake.
Woyera Uja wa Israele ndiye Momboli wako,
dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.
6Iwe Israele, Chauta wakuitananso.
Uli ngati msungwana wosiyidwa,
amene ali wodzaza ndi chisoni mu mtima,
ngati mkazi wapaunyamata amene wachotsedwa,
akuterotu Mulungu wako.”
7“Ndidaakusiya pa kamphindi kochepa,
koma ndidzakutenganso ndi chikondi chachikulu.
8Ndidaakufulatira pa mphindi yaing'ono
ndili wokwiya zedi,
koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,”
akuterotu Chauta, Momboli wako.
9 Gen. 9.8-17 “Kwa ine zimenezi zili monga m'mene
zinaliri nthaŵi ya Nowa:
monga momwe ndidaalumbirira nthaŵi imeneyo
kuti sindidzaononganso dziko lapansi ndi chigumula,
chonchonso tsopano ndikulumbiranso
kuti sindidzakupseranso mtima,
ndipo sindidzakudzudzulanso.
10 Yud. 16.15 Mapiri angathe kusuntha,
magomo angathe kugwedezeka,
koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha.
Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,”
akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Yerusalemu wam'tsogolo11 Chiv. 21.18-21 Tob. 13.16, 17 Chauta akunena kuti,
“Iwe Yerusalemu ndiwe mzinda
wozunzika, wosoŵa chithandizo,
wopanda wokutonthoza.
Ndidzakongoletsa miyala yako,
ndidzamanganso maziko ako
ndi miyala ya mtengo wapatali.
12Ndidzamanga nsanja zako
ndi miyala yofiira.
Ndidzamanga zipata zako
ndi miyala yochezimira ngati moto.
Ndidzamanganso linga lokuzungulira
ndi miyala ya mtengo wapatali.
13 Yoh. 6.45 Anthu ako ndidzaŵaphunzitsa ndekha, Ine Chauta,
ana ako ndidzaŵadalitsa ndi kuŵapatsa mtendere waukulu.
14Udzakhazikika m'chilungamo chenicheni.
Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa,
sudzakhalanso ndi mantha,
chifukwa manthawo sadzakufikira.
15Ngati wina autsa nkhondo,
si ndine ndachititsa ai.
Amene alimbana nawe adzalephera,
poti udzaŵagonjetsa.
16Udziŵe kuti ndidalenga ndine munthu wosula,
amene amakoleza moto wamakala kuti asulire zida.
Ndidalenganso ndine munthu wosakaza kuti aononge.
17Koma iwe palibe chida chopangidwa
ndi mdani chimene chidzakupweteke.
Onse okuneneza udzaŵatsutsa.
Ndimo adzapezera atumiki anga,
ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,”
akuterotu Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.