Mt. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu alankhulapo pa za kusudzulana(Mk. 10.1-12; Lk. 16.18)

1Yesu atatsiriza kunena mau ameneŵa, adachoka ku Galileya nakafika ku dera la Yudeya kutsidya kwa mtsinje wa Yordani.

2Anthu ambirimbiri adamtsata, ndipo Iye ankachiritsa odwala kumeneko.

3Afarisi ena adadza kwa Iye. Tsono kufuna pomupezera chifukwa, adamufunsa kuti, “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”

4Gen. 1.27; 5.2 Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi?

5Gen. 2.24 Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’

6Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”

7 Deut. 24.1-4; Mt. 5.31 Afarisi aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji Mose adalamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo kenaka nkumuchotsa?”

8Yesu adaŵayankha kuti, “Mose adaakulolani kusudzula akazi anu chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pa chiyambi sizinali choncho ai.

9Mt. 5.32; 1Ako. 7.10, 11Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.”

10Ophunzira ake adamuuza kuti, “Ndiyetu ngati zili choncho pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndi bwino tsono kusakwatira.”

11Yesu adaŵauza kuti, “Si anthu onse angamvetse zimenezi ai, koma okhawo amene Mulungu aŵathandiza.

12Paja pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa adabadwa motero. Pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa anthu adaŵafula. Pali enanso amene adachita kusankha okha kusakwatira, kuti azitumikira bwino Mulungu. Yemwe angathe kumvetsa, amvetse.”

Yesu adalitsa ana(Mk. 10.13-16; Lk. 18.15-17)

13Anthu ena ankabwera ndi ana kuti Yesu aŵasanjike manja ndi kuŵapempherera, ophunzira ake nkumaŵazazira.

14Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”

15Atatero adaŵasanjika manja, kenaka nkumapita.

Za wachinyamata wina wolemera(Mk. 10.17-31; Lk. 18.18-30)

16Munthu wina wachinyamata adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndizichita chabwino chanji kuti ndikalandire moyo wosatha?”

17Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.”

18Eks. 20.13; Deut. 5.17; Eks. 20.14; Deut. 5.18; Eks. 20.15; Deut. 5.19; Eks. 20.16; Deut. 5.20 Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama,

19Eks. 20.12; Deut. 5.16; Lev. 19.18 lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

20Munthu uja adati, “Malamulo onseŵa ndakhala ndikuŵatsata, nanga chanditsaliranso nchiyani?”

21Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

22Koma pamene munthu uja adamva mau ameneŵa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa anali wolemera kwambiri.

23Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti nkwapatali kwambiri kuti munthu wolemera adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba.

24Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

25Pamene ophunzira aja adamva zimenezi, adadabwa kwambiri nati, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?”

26Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”

27Pamenepo Petro adayankhapo kuti, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani. Tsono ndiye kuti tidzalandira chiyani?”

28Mt. 25.31; Lk. 22.30Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu akadzakonzanso zinthu zonse, Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake wachifumu ndi waulemerero. Tsono inunso amene mudanditsatanu, mudzakhala pa mipando yachifumu khumi ndi iŵiri mukuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele.

29Motero aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ameneyo adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka adzalandira moyo wosatha.

30Mt. 20.16; Lk. 13.30Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help