1Tsiku lina anthu adadandaula, Chauta alikumva. Chauta atamva zimenezo, adapsa mtima, ndipo moto wa Chautayo udayaka pa anthuwo, nupsereza mbali imodzi ya mahema ao.
2Tsono anthu adalira kwa Mose, ndipo Moseyo atapemphera kwa Chauta, pompo motowo udazilala.
3Motero malowo adaŵatcha Tabera, chifukwa choti moto wa Chauta udayaka pakati pao.
Mose asankha atsogoleri makumi asanu ndi aŵiri4Nthaŵi imeneyo anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraele adamva nkhuli yaikulu. Aisraelenso adayamba kudandaula, adati, “Ndani adzatipatsa nyama kuti tizidya?
5Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Ejipito, minkhaka ija, mavwende ndi anyezi wamitundu-mitundu.
6Koma tsopano mphamvu zathu zatha, ndipo sitikuwona kanthu kena kakudya koma mana basi.”
7 Eks. 16.31 Manayo ankafanafana ndi njere za mapira, ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wouma.
8Eks. 16.13-15Anthu ankapita kukatola manayo, namapera pa mphero kapena kusinja mu mtondo, ndipo ankaphika, namapangira makeke. Kukoma kwake kunali ngati makeke ophika ndi mafuta.
9Pamene mame ankagwa usiku pamahemapo, ankagwera kumodzi ndi mana.
10Mose adaŵamva anthu aja akulira m'mabanja mwao monse, aliyense atakhala pakhomo pa hema lake. Chauta adaapsa mtima kwambiri, ndipo nayenso Mose adaaipidwa nazo.
11Mose adafunsa Chauta kuti, “Chifukwa chiyani mwandivutitsa chotere mtumiki wanune? Chifukwa chiyani simudandikomere mtima, mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onseŵa?
12Kodi ndidaatenga pathupi pa anthu onseŵa ndine? Kodi ndidaŵabala ndine, kuti Inu muzindiwuza kuti ndiŵafungate pachifuwa panga, monga momwe mlezi amachitira poyamwitsa mwana, ndipo kuti ndipite nawo ku dziko limene mudalonjeza makolo ao molumbira kuti mudzaŵapatsa?
13Kodi nyama yoti ndiŵapatse anthu onseŵa, ndiitenga kuti? Iwowo akundilirira ine kuti, ‘Tipatseni nyama, tidye.’
14Ine sindingathe kuŵasamala ndekha anthu onseŵa. Katundu ameneyu sindingathe kumsenza.
15Ndipotu mukafuna kundichita zimenezi, mungondipha basi, ngati mwandikomera mtima, kuti ndisaonenso mavutowo.”
16Chauta adauza Mose kuti, “Usonkhanitse amuna makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, anthu amene ukuŵadziŵa kuti ndi atsogoleri ndi akapitao a anthu. Ubwere nawo ku chihema chamsonkhano, ndipo aime kumeneko pamodzi ndi iwe.
17Ine nditsika kudzalankhula nawe komweko. Ndidzatengako mzimu uli pa iwe ndi kuuika pa iwowo. Ndipo adzasenza nawe katundu wa anthuwo, kuti usasenzenso wekha.
18Uŵauze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera zamaŵa, ndipo mudzadya nyama. Inuyo mudalira Chauta alikumva, pamene munkati, “Ndani atipatse nyama tidye? Paja zinthu zinkatiyendera bwino ku Ejipito.” Nchifukwa chake Chauta adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya.
19Simudzaidya tsiku limodzi lokha, kapena masiku aŵiri okha, kapena masiku asanu okha, kapena masiku khumi okha, kapena masiku makumi aŵiri okha ai.
20Imeneyo mudzaidya mwezi wathunthu, mpaka izikachita kutulukira m'makutu, inuyo nkumadwala nayo. Zimenezi zidzachitika chifukwa choti mwakana Chauta amene amakhala pakati panu, ndipo mwadandaula pamaso pake nkumati, “Chifukwa chiyani tidatuluka ku Ejipito?” ’ ”
21Koma Mose adati, “Anthu amene ndikuyenda nawoŵa akukwanira 600,000. Ndipo Inu mwanena kuti, ‘Ndiŵapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu.’
22Kodi zidzaphedwa nkhosa kapena ng'ombe zingati kuti ziŵakwanire? Ngakhale nsomba zonse zam'nyanja, kodi zingathe kukwanira?”
23Chauta adafunsanso Mose kuti, “Kodi dzanja la Chauta ndi lalifupi? Tsono uwona lero lomwe lino, ngati zichitikadi monga momwe ndanenera kapena ai.”
24Choncho Mose adatuluka nakauza anthu mau a Chauta aja. Adasonkhanitsa anthu makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, naŵakhazika mozungulira chihema chamsonkhano.
25Tsono Chauta adatsika mu mtambo nayamba kulankhula ndi Mose. Ndipo adatengako mzimu umene unali pa Moseyo nauika pa akuluakulu makumi asanu ndi aŵiriwo. Anthuwo atalandira mzimu uja, adayamba kulosa. Koma sadapitirire kulosako.
26Anthu aŵiri adatsalira m'mahema, wina anali Elidadi, wina Meladi, ndipo mzimu udakhala pa iwowo. Anali nao m'gulu la olembedwa aja, koma sadapite nao ku chihema chamsonkhano, motero ankalosera m'mahema.
27Ndiye mnyamata wina adathamanga nakauza Mose kuti, “Elidadi ndi Meladi akulosa kumahemaku.”
28Apo Yoswa, mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose, mmodzi mwa anthu ake osankhidwa aja, adati, “Mbuyanga Mose, aletseni amenewo.”
29Koma Mose adamuuza kuti, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikadakondwa anthu onse a Chauta akadakhala aneneri, ndipo Chauta akadaika mzimu wake pa iwo.”
30Tsono Mose ndi atsogoleri a Aisraele aja adabwerera ku mahema.
Chauta atumiza zinziri31Tsono Chauta adautsa mphepo kuchokera ku nyanja. Mphepoyo idabwera ndi zinziri, ndipo zidagwera pafupi ndi mahema. Kuchokera kumahemako, zinzirizo zidagwa pa mtunda woyenda ulendo wa tsiku limodzi mbali imodzi, mbali inanso chimodzimodzi, mozungulira mahemawo. Zitaunjikana, mjintchi wake unali ngati mita limodzi kuchokera pansi mpaka pamwamba.
32Anthu atadzuka, ankagwira zinzirizo masana onse ndi usiku. M'maŵa mwakenso tsiku lathunthu, adachita chimodzimodzi. Panalibe ndi mmodzi yemwe amene adagwira zinziri zochepera makilogaramu chikwi chimodzi. Ndipo adaziyanika kuzungulira mahema onsewo.
33Nyama ikadali m'kamwa mwao, asanaimeze nkomwe, Chauta adaŵapsera mtima anthuwo, ndipo adaŵagwetsera mliri woopsa.
34Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Mandaankhuli, chifukwa choti kumeneko ndiko kumene adakwirira anthu ankhuli.
35Kuchokera ku Mandaankhuliko, anthu adapita ku Hazeroti, ndipo adakhala komweko.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.