1 Mphu. 21.6 Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu,
koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.
2Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Chauta,
koma munthu wokonzekera zoipa, Chauta amamzenga mlandu.
3Munthu sakhazikika bwino pochita uchimo,
koma maziko a munthu wochita zabwino sadzagwedezeka.
4Mkazi wabwino
ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake,
koma mkazi wochititsa manyazi
ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
5Maganizo a munthu wabwino ngoongoka,
koma malangizo a munthu woipa ngonyenga.
6Mau a munthu woipa mtima ngophetsa,
koma mau a munthu wolungama ngopulumutsa anthu.
7Anthu oipa mtima amagwetsedwa, naiŵalika,
koma banja la anthu omvera Mulungu silidzapasuka.
8Munthu amamuyamika malinga ndi nzeru zake,
koma munthu wa mtima wokhota amanyozeka.
9Munthu wamba, wodzigwirira ntchito
napeza zofunika, ali pabwino
kuposa wongodzikuza, pamene alibe nchakudya chomwe.
10Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake,
koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi.
11Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri,
koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.
12Nsanja yolimba ya anthu oipa mtima imaonongeka,
koma maziko a munthu wabwino ngosagwedezeka.
13Munthu woipa
amakodwa mu msampha wa zoipa za pakamwa pake,
koma munthu wochita zabwino amapulumuka ku zoipa.
14Munthu amalandira zabwino zambiri
chifukwa cha mau ake abwino,
ntchito zimene munthu amazichita
ndi manja ake zimampindulira.
15Zimene amachita munthu wopusa
mwiniwakeyo amaziyesa zolungama,
koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
16Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga,
koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe.
17Wolankhula zoona amapereka umboni woona,
koma mboni yonama imalankhula monyenga.
18Wofulumira kulankhula,
zonena zake zimalasa ngati mpeni,
koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.
19Mau oona amakhala mpaka muyaya,
koma zabodza sizikhalitsa.
20Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama,
koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe.
21Munthu wabwino vuto silimgwera,
koma woipa mavuto samchoka.
22Pakamwa pabodza pamamnyansa Chauta.
Koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amamkondweretsa.
23Munthu wochenjera amabisa nzeru zake,
koma anthu opusa amaonetsa poyera kupusa kwao.
24Ogwira ntchito mwakhama adzakhala olamulira,
koma aulesi adzakhala akapolo.
25Nkhaŵa ya munthu
imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake,
koma mau abwino amamsangalatsa.
26Munthu wochita zabwino
amatsogolera anzake pa njira yokhoza,
koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.
27Munthu waulesi sapeza zimene akukhumba,
koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengowapatali.
28Njira ya chilungamo imafikitsa ku moyo,
koma njira ya zoipa imafikitsa ku imfa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.