1M'maŵa kutangocha, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi aphunzitsi a Malamulo, pamodzi ndi ena onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda adapanga upo. Adammanga Yesu napita naye kwa Pilato.
2Pilatoyo adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha.”
3Akulu a ansembe aja adayamba kumneneza zambiri.
4Pilato adamufunsanso kuti, “Kodi ulibe poyankha? Ona zonse zimene akukunenezazi.”
5Koma Yesu sadayankhenso kanthu, kotero kuti Pilato adadabwa.
Pilato agamula kuti Yesu aphedwe(Mt. 27.15-26; Lk. 23.13-25; Yoh. 18.39—19.16)6Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira mkaidi mmodzi, yemwe Ayudawo ankapempha.
7Panali munthu wina, dzina lake Barabasi, amene anali m'ndende pamodzi ndi anthu ena chifukwa choukira Boma ndi kupha anthu.
8Tsono chikhamu cha anthu chidabwera, nkuyamba kupempha Pilato kuti aŵachitire zomwe adaazoloŵera.
9Pilato adaŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?”
10Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo akulu a ansembewo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe.
11Koma akulu a ansembewo adasonkhezera anthu onse aja kuti apemphe kuŵamasulira Barabasi.
12Tsono Pilato adaŵafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndichite naye chiyani uyu amene mukuti ndi Mfumu ya Ayudayu?”
13Anthuwo adafuula kuti, “Mpachikeni pa mtanda!”
14Pilato adaŵafunsa kuti, “Adalakwanji?” Koma iwo adafuula koposa kuti, “Mpachikeni pa mtanda!”
15Choncho Pilato, pofuna kukondwetsa anthuwo, adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda.
Asilikali achita Yesu chipongwe(Mt. 27.27-31; Yoh. 19.2-3)16Pamenepo asilikali adaloŵetsa Yesu m'bwalo, kunyumba kwa bwanamkubwa, nasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao.
17Adamuveka chovala chofiirira, naluka nsangamutu yaminga nkuiika pamutu pake.
18Kenaka adayamba kumampatsa moni kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”
19Ankamumenya m'mutu ndi ndodo, namamthira malovu, nkumamugwadira monyodola.
20Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija, namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.
Yesu apachikidwa pa mtanda(Mt. 27.32-44; Lk. 23.26-43; Yoh. 19.17-27)21 kuti amwe, koma Iye adakana.
24 chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi.
39Mkulu wa asilikali amene adaaimirira pomwepo kuyang'anana naye, ataona kuti Yesu watsirizika akufuula chotero, adati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.”
40
43Yosefe wa ku Arimatea adafika. Adaali mkulu wodziŵika ndithu, wa m'Bwalo Lalikulu la Ayuda. Nayenso ankayembekeza Ufumu wa Mulungu. Tsono iye adalimba mtima, napita kwa Pilato kukapempha kuti ampatsire mtembo wa Yesu.
44Pilato adaadabwa kumva kuti Yesu wafa kale. Choncho adaitanitsa mkulu wa asilikali uja, namufunsa kuti, “Kodi Yesu wafa kaledi?”
45Mkulu wa asilikaliyo atavomera, Pilato adamlola Yosefe kuti akatenge mtembowo.
46Yosefeyo adagula nsalu yoyera yabafuta, natsitsa mtembo uja nkuukuta ndi nsaluyo. Adauika m'manda ochita chosema m'thanthwe, kenaka adagubuduzira chimwala pa khomo kutseka pamandapo.
47Maria uja wa ku Magadala, ndi Maria mai wa Yosefe, ankaona kumene adamuika Yesu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.