1Zinanso zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya ndi izi: Panali dengu la zipatso zakupsa.
2Chauta adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Tsono Chauta adandiwuza kuti,
“Nthaŵi ya chimalizo yaŵakwanira anthu anga Aisraele,
sindidzaŵakhululukiranso.
3Nyimbo za m'Nyumba ya Mulungu
zidzasanduka kulira pa tsiku limenelo.
Mitembo ya anthu idzachuluka,
ndipo adzaiponya ponseponse.
Kudzangoti zii!”
Akuterotu Ambuye Chauta.
Chilango cha Aisraele4Amosi adati, “Imvani izi,
inu amene mumapondereza osoŵa,
amene mufuna kuwononga anthu osauka am'dzikomu.
5Inu mumadzifunsa kuti,
‘Kodi chikondwerero cha kukhala kwa
mwezi chidzatha liti,
kuti tigulitse dzinthu?
Kodi tsiku lopumula la Sabata litha liti
kuti tigulitsenso tirigu,
kutinso tipeze mpata wochepetsera miyeso
ndi kukweza mitengo,
ndiponso kuti tichenjeretse anthu
ndi masikelo onama,
6kuti osauka tiŵagule ndi siliva,
amphaŵi tiŵagule ndi nkhwaŵiro,
kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’ ”
7Chauta, Mulungu amene ana a Yakobe amamnyadira
walumbira kuti,
“Ndithudi, sindidzaiŵala zochita zao zonse.
8Chifukwa cha zonsezi dziko lapansi lidzagwedezeka,
ndipo onse okhala m'menemo adzamva chisoni!
Dziko lonse lapansi lidzagwedezeka ngati Nailo,
lidzafufuma ndi kuteranso
ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.”
9Ambuye Chauta akunena kuti,
“Pa tsiku limenelo ndidzadetsa dzuŵa masana,
ndidzagwetsa mdima pa dziko lapansi dzuŵa lili nye.
10Zikondwerero zanu ndidzazisandutsa kulira,
nyimbo zanu ndidzazisandutsa zamaliro.
Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu pathupi panu,
ndipo mitu yanu yonse idzachita dazi.
Mudzakhala ngati anakubala olira mwana wao mmodzi yekha.
Tsiku limenelo lidzakhaladi loŵaŵa mpaka kutha kwake.”
11Ambuye Chauta akunena kuti,
“Nthaŵi ikubwera
pamene ndidzagwetsa njala m'dzikomo.
Siidzakhala njala ya buledi,
kapena ludzu la madzi ai,
koma njala yosoŵa mau a Chauta.
12Anthu azidzangoyenda uku ndi uku
kuchoka ku nyanja ina kunka ku nyanja inanso,
azidzangoti piringupiringu
kuchoka chakumpoto kunka chakuvuma.
Azidzafunafuna mau a Chauta,
koma osaŵapeza.
13“Pa tsiku limenelo ngakhale anamwali
abiriŵiri ndi anyamata asee adzakomoka ndi ludzu.
14Onse amene amalumbira m'dzina la Asima,
mulungu wa Samariya,
nkumanena kuti, ‘Pali mulungu wa ku Dani!’
Kapena kuti, ‘Pali njira yopatulika ya ku Beereseba!’
Onsewo adzagwa osadzukanso.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.