Mas. 93 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu ndiye mfumu

1Chauta ndiye mfumu.

Wavala ulemerero, wavala mphamvu ngati lamba.

Iye adakhazikitsa dziko lapansi,

silidzagwedezeka konse.

2Mpando wanu waufumu, Inu Chauta,

mudaukhazikitsa kuyambira makedzana,

Inu ndinu amuyaya.

3Inu Chauta, nyanja zazikulu zakwera, zikukokoma koopsa.

Mafunde ake akuchita mkokomo waukulu.

4Chauta amene ali pamwamba,

ndi wamphamvu kupambana kulindima kwa madzi ambiri,

ndi wamphamvu kuposa mafunde am'nyanja.

5Malamulo anu ndi osasinthika, Inu Chauta,

Nyumba yanu ndi yoyera mpaka muyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help